Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 77:1-2

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Yedutuni. Salimo la Asafu.

77 Ndinafuwulira Mulungu kupempha thandizo;
    ndinafuwula mokweza kwa Mulungu kuti anditcherere khutu.
Pamene ndinali pa masautso ndinafunafuna Ambuye;
    usiku ndinatambasula manja mosalekeza
    ndipo moyo wanga unakana kutonthozedwa.

Masalimo 77:11-20

11 Ine ndidzakumbukira ntchito za Yehova;
    Ine ndidzakumbukira zodabwitsa zanu za kalekale.
12 Ndidzakumbukira ntchito zanu
    ndi kulingalira zodabwitsa zanu.”

13 Njira zanu Mulungu ndi zoyera.
    Kodi ndi mulungu uti ali wamkulu kuposa Mulungu wathu?
14 Inu ndinu Mulungu wochita zodabwitsa;
    Mumaonetsera mphamvu yanu pakati pa mitundu ya anthu.
15 Ndi dzanja lanu lamphamvu munawombola anthu anu,
    zidzukulu za Yakobo ndi Yosefe.
            Sela

16 Madzi anakuonani Mulungu,
    madzi anakuonani ndipo anachita mantha;
    nyanja yozama inakomoka.
17 Mitambo inakhuthula madzi ake pansi,
    mu mlengalenga munamveka mabingu;
    mivi yanu inawuluka uku ndi uku.
18 Bingu lanu linamveka mʼmphepo ya kamvuluvulu,
    mphenzi yanu inawalitsa dziko lonse;
    dziko lapansi linanjenjemera ndi kugwedezeka.
19 Njira yanu inadutsa pa nyanja,
    njira yanu inadutsa pa madzi amphamvu,
    ngakhale zidindo za mapazi anu sizinaoneke.

20 Inu munatsogolera anthu anu ngati gulu la nkhosa
    mwa dzanja la Mose ndi Aaroni.

1 Mafumu 22:29-40

Ahabu Aphedwa ku Ramoti Giliyadi

29 Choncho mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. 30 Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo.

31 Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.” 32 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula, 33 olamulira akavalo anaona kuti sanali mfumu ya ku Israeli ndipo analeka kumuthamangitsa.

34 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.” 35 Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira. 36 Pamene dzuwa linkalowa, kunamveka mfuwu wa nkhondo kuti, “Munthu aliyense apite ku mzinda wa kwawo, aliyense apite ku dziko la kwawo!”

37 Ndipo mfumu ija inafa, nabwera nayo ku Samariya, ndipo anayika mʼmanda kumeneko. 38 Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera.

39 Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli? 40 Ahabu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

1 Mafumu 22:51-53

Ahaziya Mfumu ya ku Israeli

51 Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 52 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli. 53 Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.

2 Akorinto 13:5-10

Tadzisanthulani nokha kuti muone ngati muli mʼchikhulupiriro; dziyeseni nokha. Kodi simuzindikira kuti Khristu Yesu ali mwa inu, ngati si choncho mwalephera mayesowa? Ndipo ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitinalephere mayesowo. Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro. 10 Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.