Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Pamene Sauli anatumiza anthu kuti akalondere nyumba ya Davide ndi cholinga choti amuphe.
59 Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu;
munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.
2 Landitseni kwa anthu ochita zoyipa
ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.
3 Onani momwe iwo akundibisalira!
Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane;
osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.
4 Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo.
Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!
5 Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,
dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse;
musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.
6 Iwo amabweranso madzulo
akuchita phokoso ngati agalu
ndi kumangoyendayenda mu mzinda.
7 Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo;
iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo,
ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”
8 Koma Inu Yehova, mumawaseka,
mumayinyoza mitundu yonseyo.
9 Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu;
Inu Mulungu, ndinu linga langa. 10 Mulungu wanga wachikondi.
Mulungu adzapita patsogolo panga
ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.
11 Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu,
kuopa kuti anthu anga angayiwale.
Mwa mphamvu zanu,
lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.
12 Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo
chifukwa cha mawu a milomo yawo,
iwo akodwe mʼkunyada kwawo.
Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula
13 muwawononge mu ukali (wanu)
muwawononge mpaka atheretu.
Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi
kuti Mulungu amalamulira Yakobo.
14 Iwo amabweranso madzulo,
akuchita phokoso ngati agalu
ndi kumangoyenda mu mzinda.
15 Iwo amayendayenda kufuna chakudya
ndipo amawuwa ngati sanakhute.
16 Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu,
mmawa ndidzayimba zachikondi chanu;
pakuti ndinu linga langa,
pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.
17 Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu;
Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.
Yehu Adzozedwa Ufumu wa ku Israeli
9 Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi. 2 Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati. 3 Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”
4 Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi. 5 Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.”
Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?”
Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
6 Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova. 7 Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli. 8 Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu. 9 Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. 10 Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’ ” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.
11 Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?”
Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
12 Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.”
Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”
13 Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”
Khristu ndiye Nzeru ndi Mphamvu za Mulungu
18 Pakuti uthenga wa mtanda ndi chopusa kwa iwo amene akuwonongeka, koma kwa ife amene tikupulumutsidwa uthengawu ndi mphamvu ya Mulungu. 19 Pakuti kwalembedwa kuti,
“Ine ndidzawononga nzeru za anthu anzeru;
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
20 Munthu wanzeru ali kuti? Munthu wozama ndi maphunziro ali kuti? Munthu wodziwa zakuya zamakono ali kuti? Kodi Mulungu sanazipusitse nzeru za dziko lapansi? 21 Tsono poti mwa nzeru za Mulungu dziko lapansi mu nzeru zake silinamudziwe Iye, Mulungu amakondweretsedwa kuti kudzera mu chopusa cha zomwe zinalalikidwa apulumutse iwo amene akhulupirira. 22 Ayuda amafuna zizindikiro zodabwitsa ndipo Agriki amafunafuna nzeru, 23 koma ife timalalikira Khristu wopachikidwa. Chitsa chokhumudwitsa kwa Ayuda ndi chopusa kwa a mitundu ina. 24 Koma kwa iwo amene Mulungu anawayitana, Ayuda ndi Agriki omwe, Khristu ndi mphamvu ya Mulungu ndi nzeru za Mulungu. 25 Pakuti za Mulungu zooneka ngati zopusa, ndi za nzeru kuposa nzeru za munthu, ndipo za Mulungu zooneka ngati zofowoka, zili ndi mphamvu kuposa mphamvu za munthu.
26 Abale taganizirani mmene munalili musanayitanidwe. Si ambiri a inu munali a nzeru, si ambiri a inu munali a mphamvu zamakopedwe. Si ambiri a inu munali obadwa pa ulemerero. 27 Koma Mulungu anasankha zinthu zopusa za dziko lapansi kuti achititse manyazi anzeru. Mulungu anasankha zinthu zofowoka za dziko lapansi kuti achititse manyazi amphamvu. 28 Anasankha zinthu zapansipansi ndi zopeputsidwa za dziko la pansi lino, zinthu zimene kulibe, kuti asukulutse zimene zilipo, 29 kuti munthu asanyade pamaso pa Mulungu. 30 Nʼchifukwa cha Iye kuti inu muli mwa Khristu Yesu, amene wakhala nzeru ya kwa Mulungu, kwa ife, kunena kuti kulungama kwathu, chiyero ndi chipulumutso. 31 Choncho poti zinalembedwa kuti, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.