Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 48

Nyimbo. Salimo la ana a Kora.

48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
    mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
Lokongola mu utali mwake,
    chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
    mzinda wa Mfumu yayikulu.
Mulungu ali mu malinga ake;
    Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.

Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
    pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
    anathawa ndi mantha aakulu.
Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
    ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
    zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.

Monga momwe tinamvera,
    kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
    mu mzinda wa Mulungu wathu.
    Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.

Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
    ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
    matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
    dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
    midzi ya Yuda ndi yosangalala
    chifukwa cha maweruzo anu.

12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
    werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
    penyetsetsani malinga ake,
    kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
    Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.

Numeri 24:1-14

24 Tsopano Balaamu ataona kuti kunakomera Yehova kudalitsa Israeli, sanapitenso ku mawula monga ankachitira kale, koma kuyangʼana ku chipululu. Balaamu atayangʼana, anaona Aisraeli atamanga misasa yawo fuko ndi fuko. Pamenepo mzimu wa Mulungu unabwera pa iye ndipo ananena uthenga wake:

“Uthenga wa Balaamu mwana wa Beori,
    uthenga wa amene diso lake ndi lotsekuka,
uthenga wa amene amamva mawu a Mulungu,
    yemwe amaona masomphenya wochokera kwa Wamphamvuzonse,
    yemwe amagwa chafufumimba, koma maso ake ali chipenyere:

“Matenti ako ndi okongola kwambiri iwe Yakobo,
    misasa yako, iwe Israeli!

“Monga zigwa zotambalala,
    monga minda mʼmbali mwa mtsinje,
monga aloe wodzalidwa ndi Yehova,
    monga mikungudza mʼmbali mwa madzi.
Madzi adzayenderera mʼmitsuko yake;
    mbewu zake zidzakhala ndi madzi ambiri.

“Mfumu yake idzakhala yamphamvu kuposa Agagi;
    ufumu wake udzakwezedwa.

“Mulungu womutulutsa mʼdziko la Igupto
    ali ndi mphamvu ngati za njati.
Amawononga mitundu yomuwukira
    ndi kuphwanya mafupa awo,
    amalasa ndi mivi yake.
Monga mkango waumuna, amabisala nagona pansi,
    monga mkango waukazi, adzamuputa ndani?

“Amene adalitsa iwe, adalitsike
    ndipo amene atemberera iwe, atembereredwe!”

10 Kenaka Balaki anakwiyira Balaamu. Anawomba mʼmanja ndi kunena naye kuti, “Ndinakuyitana kuti utemberere adani anga, koma taona, wawadalitsa katatu konseka. 11 Tsopano choka msanga uzipita kwanu! Ndinanena kuti ndidzakulipira bwino kwambiri, koma Yehova sanafune kuti ulandire malipirowo.”

12 Balaamu anayankha Balaki kuti, “Kodi sindinawawuze amithenga amene munawatumiza kwa ine, 13 kuti ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yaufumu yodzaza ndi siliva ndi golide sindingathe kuchita zinthu mwa ine ndekha, zabwino kapena zoyipa, kuposa lamulo la Yehova ndi kuti ndiyenera kunena zokhazo zimene Yehova akunena? 14 Tsopano ndikupita kwa anthu anga, koma tabwerani ndikuchenjezeni zimene anthu awa adzachitira anthu anu masiku akubwerawa.”

Luka 1:26-38

Aneneratu za Kubadwa kwa Yesu

26 Mwezi wachisanu ndi chimodzi, Mulungu anatuma mngelo Gabrieli ku Nazareti, mudzi wa ku Galileya, 27 kwa namwali wopalidwa ubwenzi ndi Yosefe, wa fuko la Davide. Dzina la namwaliyo linali Mariya. 28 Mngeloyo anafika kwa iye nati, “Moni, inu amene Ambuye wakukomerani mtima kwambiri! Ambuye ali ndi inu.”

29 Mariya anavutika kwambiri ndi mawu awa ndipo anadabwa ndi kulonjera kotere. 30 Koma mngeloyo anati kwa iye, “Usachite mantha Mariya, pakuti wapeza chisomo pamaso Mulungu. 31 Udzakhala woyembekezera ndipo udzabala mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. 32 Iye adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wammwambamwamba. Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando waufumu wa abambo ake Davide, 33 ndipo adzalamulira pa nyumba ya Yakobo ku nthawi zonse; ufumu wake sudzatha.”

34 Mariya anafunsa mngeloyo kuti, “Izi zingatheke bwanji popeza ine sindidziwa mwamuna?”

35 Mngelo anayankha kuti, “Mzimu Woyera adzabwera pa iwe ndipo mphamvu ya Wammwambamwamba idzakuphimba, ndipo Woyerayo amene adzabadwe adzatchedwa Mwana wa Mulungu. 36 Ngakhale Elizabeti mʼbale wako adzakhala ndi mwana mu ukalamba wake ndipo iye amene amati ndi wosabereka, uno mwezi wake wachisanu ndi chimodzi. 37 Pakuti palibe chinthu chosatheka ndi Mulungu.”

38 Mariya anayankha kuti, “Ine ndine mtumiki wa Ambuye. Zikhale kwa ine monga mwanenera.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.