Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
BUKU LACHIWIRI
Masalimo 42–72
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.
42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
2 Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
3 Misozi yanga yakhala chakudya changa
usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
4 Zinthu izi ndimazikumbukira
pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
pakati pa anthu a pa chikondwerero.
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi 6 Mulungu wanga.
Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
7 Madzi akuya akuyitana madzi akuya
mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
andimiza.
8 Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.
9 Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
“Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
“Mulungu wako ali kuti?”
11 Bwanji ukumva chisoni,
iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.
43 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;
ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;
mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
2 Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.
Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
woponderezedwa ndi mdani?
3 Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu
kuti zinditsogolere;
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,
kumalo kumene inu mumakhala.
4 Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.
Ndidzakutamandani ndi zeze,
Inu Mulungu wanga.
5 Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?
Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu,
pakuti ndidzamutamandabe Iye,
Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.
14 “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka,
ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse.
15 Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga,
ngati mitsinje imene imathamanga.
16 Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja,
imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula,
17 koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe,
ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo.
18 Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi;
iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu.
19 Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi,
anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo.
20 Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi;
koma akafika kumeneko, amangokhumudwako.
21 Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza,
mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha.
22 Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake,
ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu,
23 ndilanditseni mʼdzanja la mdani,
ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’
24 “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete;
ndionetseni pomwe ndalakwitsa.
25 Ndithu, mawu owona ndi opweteka!
Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani?
26 Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena,
ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe?
27 Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye
ndi kumugulitsa bwenzi lanu.
28 “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana.
Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu?
29 Fewani mtima, musachite zosalungama;
ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe.
30 Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga?
Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa?
Lamulo ndi Lonjezo
15 Abale, ndiloleni ndipereke chitsanzo cha zochitika mʼmoyo wa tsiku ndi tsiku. Pangano likakhazikitsidwa palibe amene angachotsepo kapena kuwonjezerapo, choncho ndi chimodzimodzi pa nkhani iyi. 16 Malonjezo awa anaperekedwa kwa Abrahamu ndi kwa mbewu yake. Malemba sakunena kuti, “kwa mbewu zake,” kutanthauza anthu ambiri, koma, “kwa mbewu yako,” kutanthauza munthu mmodzi, amene ndi Khristu. 17 Chimene ndikutanthauza ine ndi ichi: Malamulo amene anabwera patatha zaka 430, sangathetse pangano limene linakhazikitsidwa kale ndi Mulungu ndi kuliwononga lonjezolo. 18 Ngati madalitso athu akudalira ntchito za lamulo ndiye kuti madalitsowo sakupatsidwa chifukwa cha lonjezo. Koma Mulungu mwachisomo chake anadalitsa Abrahamu kudzera mu lonjezo.
19 Nanga tsono cholinga cha lamulo chinali chiyani? Linaperekedwa chifukwa cha zolakwa mpaka itafika mbewu imene lonjezo limanena. Malamulowo anaperekedwa ndi angelo kudzera mwa mʼkhalapakati. 20 Ngakhale zili chomwecho, mʼkhalapakati sayimira mbali imodzi yokha, koma Mulungu ndi mmodzi.
21 Kodi ndiye kuti lamulo limatsutsana ndi malonjezo a Mulungu? Ayi. Nʼkosatheka! Pakuti ngati tikanapatsidwa malamulo opatsa moyo ndiye kuti mwa lamulo tikanakhala olungama. 22 Koma Malemba akunenetsa kuti dziko lonse lili mu ulamuliro wauchimo, kuti mwachikhulupiriro mwa Yesu Khristu, chimene chinalonjezedwa chiperekedwe kwa amene akhulupirira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.