Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 122

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

122 Ndinakondwera atandiwuza kuti,
    “Tiyeni ku nyumba ya Yehova.”
Mapazi athu akuyima mʼzipata
    zako, Iwe Yerusalemu.

Yerusalemu anamangidwa ngati mzinda
    umene uli wothithikana pamodzi.
Kumeneko ndiye kumene kumapita mafuko,
    mafuko a Yehova,
umboni wa kwa Israeli,
    kuti atamande dzina la Yehova.
Kumeneko anayikako mipando yaufumu yachiweruzo,
    mipando yaufumu ya nyumba ya Davide.

Pemphererani mtendere wa Yerusalemu:
    “Iwo amene amakukonda iwe zinthu ziwayendere bwino.
Mukhale mtendere mʼkati mwa makoma ako,
    ndipo mʼnyumba zako zaufumu mukhale chitetezo.”
Chifukwa cha abale anga ndi abwenzi anga
    ndidzati, “Mtendere ukhale mʼkati mwako.”
Chifukwa cha Nyumba ya Yehova Mulungu wathu,
    ndidzakufunira zabwino.

Estere 9:1-5

Chigonjetso cha Ayuda

Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.

Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo.

Estere 9:18-23

Kukondwerera Purimu

18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.

19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.

20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.

23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai.

Luka 12:4-12

“Ine ndikuwuzani, abwenzi anga, musachite mantha ndi amene amapha thupi chifukwa akatero sangachitenso kanthu. Koma Ine ndidzakuonetsani amene muyenera kumuopa: Wopani Iye, amene pambuyo pakupha thupi, ali ndi mphamvu yakukuponyani ku gehena. Inde, Ine ndikuwuzani, muopeni Iye. Kodi atimba asanu samagulidwa ndi ndalama ziwiri? Ngakhale zili chomwecho palibe imodzi ya izo imene imayiwalika ndi Mulungu. Ndithudi, tsitsi lonse la mʼmutu mwanu ndi lowerengedwa. Musachite mantha; inu ndi oposa kwambiri mpheta zambiri.

“Ine ndikukuwuza kuti, aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Mwana wa Munthu adzamuvomerezanso pamaso pa angelo a Mulungu. Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu adzakanidwanso pamaso pa angelo a Mulungu. 10 Ndipo aliyense amene ayankhulira Mwana wa Munthu mawu oyipa adzakhululukidwa, koma iye wochitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa.

11 “Akadzakutengerani ku masunagoge pamaso pa oweruza ndi a maulamuliro, musadere nkhawa mmene mudzadzitchinjirizire nokha kapena chimene mudzayankhule, 12 pakuti Mzimu Woyera nthawi imeneyo adzakuphunzitsani zoyenera kunena.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.