Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
118 Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake chosasinthika ndi chosatha.
2 Israeli anene kuti:
“Chikondi chake ndi chosatha.”
14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.
15 Mfuwu wachimwemwe ndi chipambano
ukumveka mʼmatenti a anthu olungama mtima kuti:
“Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!
16 Dzanja lamanja la Yehova latukulidwa mmwamba
Dzanja lamanja la Yehova lachita zamphamvu!”
17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo
ndipo ndidzalalika za ntchito ya Yehova.
18 Yehova wandilanga koopsa,
koma sanandipereke ku imfa.
19 Tsekulireni zipata zachilungamo,
kuti ndifike kudzayamika Yehova.
20 Ichi ndicho chipata cha Yehova
chimene olungama mtima okha adzalowerapo.
21 Ndidzakuyamikani chifukwa Inu munandiyankha;
mwakhala chipulumutso changa.
22 Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wasanduka wapangodya;
23 Yehova ndiye wachita zimenezi
ndipo nʼzodabwitsa pamaso pathu.
24 Lero ndiye tsiku limene Yehova walipanga;
tiyeni tikondwere ndi kusangalala nalo.
Bokosi la Chipangano Libwera ku Yerusalemu
6 Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. 2 Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo. 3 Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, 4 imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake. 5 Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga.
6 Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. 7 Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo.
8 Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza.
9 Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” 10 Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. 11 Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse.
12 Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. 13 Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa. 14 Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala, 15 pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga.
Yesu Auka kwa Akufa
24 Pa tsiku loyamba la Sabata, mmamawa kwambiri, amayi anatenga zonunkhira napita ku manda. 2 Anaona mwala wa pa manda utagubuduzika 3 ndipo atalowamo sanapeze mtembo wa Ambuye Yesu. 4 Pamene iwo ankadabwa za zimenezi, mwadzidzidzi, amuna awiri ovala zovala zonyezimira kwambiri anayimirira pambali pawo. 5 Ndi mantha, amayiwo anaweramitsa nkhope zawo pansi, koma amunawo anawawuza kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufuna wamoyo pakati pa akufa? 6 Iye sali muno ayi. Wauka! Kumbukirani zimene anakuwuzani pamene anali nanu ku Galileya: 7 ‘Mwana wa Munthu ayenera kuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa, napachikidwa ndipo tsiku lachitatu adzaukitsidwanso.’ ” 8 Ndipo anakumbukira mawu ake.
9 Atabwerera kuchokera ku mandako, anafotokoza zinthu zonse kwa khumi ndi mmodziwo ndi kwa ena onse. 10 Amayi anali Mariya Magadalena, Yohana, Mariya amayi a Yakobo, ndi ena anali nawo amene anawuza atumwi. 11 Koma iwo sanawakhulupirire amayiwa, chifukwa mawu awo amaoneka kwa iwo ngati opanda nzeru. 12 Komabe Petro anayimirira ndi kuthamangira ku manda. Atasuzumira, anaona nsalu zimene anamukulungira zija zili pa zokha, ndipo iye anachoka, akudabwa ndi zimene zinachitikazo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.