Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 20

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
    dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
    akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
Iye akumbukire nsembe zako zonse
    ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
            Sela
Akupatse chokhumba cha mtima wako
    ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
    ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.

Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
    Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
    ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
    koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
    koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.

Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
    Tiyankheni pamene tikuyitanani!

Oweruza 9:7-15

Yotamu atamva izi anapita kukayima pamwamba pa phiri la Gerizimu ndipo anafuwula nati, “Tandimverani inu anthu a ku Sekemu, kuti Mulungu akumvereninso. Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ ”

“Koma mtengo wa olivi uja unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye mafuta angawa amene amalemekezera nawo milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo?’ ”

10 Apo mitengo inawuza mtengo wa mkuyu kuti, “Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.”

11 Koma mtengo wa mkuyu unayankha kuti, “Kodi ndisiye chipatso changa chokoma ndi chozunachi kuti ndizikalamulira mitengo?”

12 Kenaka mitengo ija inawuza mtengo wamphesa kuti, “Bwera ndiwe kuti ukhale mfumu yathu.”

13 Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?”

14 Pomaliza mitengo yonse inawuza mkandankhuku kuti, “Bwera ndipo ukhale mfumu yathu.”

15 Mkandankhuku uja unayankha kuti, “Ngati mukufunadi kuti mudzoze ine kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mu mthunzi mwangamu, koma ngati simutero, moto utuluka kwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.”

1 Yohane 2:18-28

Anthu Okana Khristu

18 Ana anga, ino ndi nthawi yotsiriza, ndipo monga munamva kale kuti anthu okana Khristu akubwera, ngakhale tsopano okana Khristu ambiri afika kale. Zimenezi zikutisonyeza kuti ino ndi nthawi yotsiriza. 19 Anthu amenewa anachoka pakati pathu, komatu sanali a mʼgulu lathu. Pakuti akanakhala a mʼgulu lathu, akanakhalabe nafe, koma kuchoka kwawo kunatisonyeza kuti sanali a mʼgulu lathu.

20 Koma inu muli ndi kudzoza kochokera kwa Woyerayo, ndipo nonsenu mukudziwa choonadi. 21 Sindikukulemberani chifukwa choti simudziwa choonadi ayi, koma chifukwa choti mumadziwa choonadicho, ndipo mukudziwanso kuti bodza silichokera pa choonadi. 22 Wabodzayo ndani? Ndi munthu aliyense amene amanena kuti Yesu si Mpulumutsi. Munthu woteroyo ndi wokana Khristu, ndiponso amakana Atate, ndi Mwana. 23 Aliyense wokana Mwana alibenso Atate. Wovomereza Mwana alinso ndi Atate.

24 Onetsetsani kuti zimene munazimva kuyambira pachiyambi zikhalebe mwa inu. Ngati zikhala mwa inu, inunso mudzakhala mwa Mwana ndiponso mwa Atate. 25 Ndipo chimene anatilonjeza nʼchimenechi: moyo wosatha.

26 Ine ndikukulemberani zimenezi kuti ndikuwuzeni za amene akufuna kukusocheretsani. 27 Koma za inu, kudzoza kumene munalandira kwa Khristu kuli mwa inu, ndipo sipafunika wina aliyense kuti akuphunzitseni. Koma kudzozako kumakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo popeza kudzoza kwakeko nʼkoona osati konama, monga munaphunzira, khalani mwa Iyeyo.

Ana a Mulungu

28 Tsopano ana okondedwa, khalani mwa Yesu, kuti pamene adzaonekera, ife tidzakhale otsimikizika mu mtima ndi wopanda manyazi pamaso pake akamadzabwera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.