Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
20 Yehova akuyankhe pamene uli pa msautso;
dzina la Mulungu wa Yakobo likuteteze.
2 Iye atumize thandizo kuchokera ku malo ake opatulika;
akugwirizize kuchokera ku Ziyoni.
3 Iye akumbukire nsembe zako zonse
ndipo alandire nsembe zako zopsereza.
Sela
4 Akupatse chokhumba cha mtima wako
ndipo akuthandize kuti zonse wakonza zichitike.
5 Ife tidzafuwula ndi chimwemwe pamene iwe wapambana
ndipo tidzanyamula mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu,
Yehova ayankhe zopempha zako zonse.
6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake;
Iye amamuyankha kuchokera kumwamba ku malo ake opatulika
ndi mphamvu yopulumutsa ya dzanja lake lamanja.
7 Ena amadalira magaleta ndipo ena akavalo
koma ife tidzadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.
8 Iwo amagonjetsedwa ndi kugwa,
koma ife timadzuka ndi kuyima chilili.
9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!
Tiyankheni pamene tikuyitanani!
Adzutsa Chihema
40 Kenaka Yehova anati kwa Mose, 2 “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi. 3 Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani. 4 Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake. 5 Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema.
6 “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano. 7 Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi. 8 Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo.
9 “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa. 10 Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri. 11 Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule.
12 “Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. 13 Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe. 14 Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro. 15 Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado”
Kulimbika Mtima ndi Kupirira pa Chikhulupiriro
19 Ndipo tsono abale, molimba mtima timalowa mʼMalo Opatulika kwambiri chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye anatitsekulira njira yatsopano ndi yamoyo kudutsa chinsalu chotchinga, chimene ndi thupi lake. 21 Ndiponso tili ndi wansembe wamkulu woyangʼanira nyumba ya Mulungu. 22 Tsono tiyeni tiyandikire kwa Mulungu ndi mtima woona ndi wodzaza ndi chikhulupiriro. Popeza mitima yathu yayeretsedwa, ndi yopanda chikumbumtima chotitsutsa, ndiponso matupi athu asambitsidwa ndi madzi woyera. 23 Tiyeni tigwiritsitse mosagwedezeka zimene timaziyembekezera ndi kuzivomereza, pakuti amene anatilonjezayo ndi wokhulupirika. 24 Tiziganizira mmene tingalimbikitsirane wina ndi mnzake pokondana ndi kuchita ntchito zabwino. 25 Tiyeni tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi monga mmene ena amachitira, koma tizilimbikitsana makamaka poona kuti tsiku la Ambuye layandikira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.