Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 31:9-16

Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;
    maso anga akulefuka ndi chisoni,
    mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.
10 Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima
    ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;
mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,
    ndipo mafupa anga akulefuka.
11 Chifukwa cha adani anga onse,
    ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;
ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.
    Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.
12 Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;
    ndakhala ngati mʼphika wosweka.
13 Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;
    zoopsa zandizungulira mbali zonse;
iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,
    kuti atenge moyo wanga.

14 Koma ndikudalira Inu Yehova;
    ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”
15 Masiku anga ali mʼmanja mwanu;
    ndipulumutseni kwa adani anga
    ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.
16 Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;
    pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.

Levitiko 23:1-8

23 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Awa ndi masiku anga osankhika a chikondwerero, masiku osankhika olemekeza Yehova amene uyenera kulengeza kuti akhale masiku opatulika a misonkhano.

Za Sabata

“ ‘Pa masiku asanu ndi limodzi muzigwira ntchito, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata lopuma, tsiku la msonkhano wopatulika. Kulikonse kumene inu mukukhala musamagwire ntchito iliyonse tsiku limeneli popeza ndi tsiku la Sabata la Yehova.

Za Paska ndi za Buledi Wopanda Yisiti

“ ‘Awa ndiwo masiku osankhidwa a zikondwerero za Yehova, masiku woyera a misonkhano amene muti mudzalengeze pa nthawi yake: Chikondwerero cha Paska chiziyamba madzulo a tsiku la 14 la mwezi woyamba. Tsiku la 15 la mwezi womwewo ndi tsiku lolemekeza Yehova ndipo muziyamba Chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti. Muzidya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri. Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse. Pa masiku asanu ndi awiri muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wopatulika ndipo musamagwire ntchito yolemetsa.’ ”

Luka 22:1-13

Yudasi Avomera Kumupereka Yesu

22 Phwando la buledi wopanda yisiti lotchedwa Paska litayandikira, akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo amafunafuna mpata woti amuphere Yesu, pakuti ankachita mantha ndi anthu. Kenaka Satana analowa mwa Yudasi, wotchedwa Isikarioti, mmodzi wa khumi ndi a iwiriwo. Ndipo Yudasi anapita kwa akulu a ansembe ndi akulu oyangʼanira Nyumba ya Mulungu ndi kukambirana nawo za mmene iye angaperekere Yesu. Iwo anakondwa ndipo anagwirizana zomupatsa ndalama. Iye anavomera, ndipo anayamba kufunafuna mpata wabwino wakuti amupereke Yesu kwa iwo pamene panalibe gulu la anthu pafupi.

Paska Womaliza

Kenaka linafika tsiku la buledi wopanda yisiti pamene mwana wankhosa wa Paska amaperekedwa nsembe. Yesu anatuma Petro ndi Yohane nati, “Pitani kukatikonzera Paska kuti tikadye.”

Iwo anafunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonzere kuti?”

10 Iye anayankha kuti, “Taonani, mukamalowa mu mzinda, mudzakumana ndi mwamuna atanyamula mtsuko wamadzi. Mulondoleni ku nyumba imene akalowe, 11 ndipo mukamuwuze mwini nyumbayo kuti, ‘Aphunzitsi kufunsa kuti, chili kuti chipinda cha alendo, kumene Ine ndi ophunzira anga tikadyere Paska?’ 12 Iyeyo adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala ndi zonse. Kachiteni zokonzekera mʼmenemo.”

13 Iwo anapita nakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Tsono anakonza Paska.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.