Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 148

148 Tamandani Yehova.

Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
    mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
Mutamandeni, inu angelo ake onse,
    mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
    mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
    ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
Zonse zitamande dzina la Yehova
    pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
    analamula ndipo sizidzatha.

Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
    inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
    mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
inu mapiri ndi zitunda zonse,
    inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
    inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
    inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
    inu nkhalamba ndi ana omwe.

13 Onsewo atamande dzina la Yehova
    pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
    ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
    matamando a anthu ake onse oyera mtima,
    Aisraeli, anthu a pamtima pake.

Tamandani Yehova.

Miyambo 8:32-36

32 “Ndiye tsono ana inu, ndimvereni;
    odala anthu amene amasunga njira zanga.
33 Mverani malangizo anga kuti mukhale ndi nzeru;
    musanyozere mawu anga.
34 Wodala munthu amene amandimvera,
    amene amakhala pa khomo panga tsiku ndi tsiku,
    kudikirira pa chitseko changa.
35 Paja aliyense amene apeza ine wapeza moyo
    ndipo Yehova amamukomera mtima.
36 Koma amene alephera kundipeza, amadzipweteka yekha;
    onse amene amandida amakonda imfa.”

Yohane 21:19-24

19 Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”

20 Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?” 21 Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”

22 Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” 23 Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”

24 Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.