Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
3 Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”
2 Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa. 3 Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo, 4 ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.
68 “Alemekezeke Ambuye, Mulungu wa Israeli
chifukwa wabwera ndi kuwombola anthu ake.
69 Iye wakweza nyanga yachipulumutso kwa ife
mu nyumba ya mtumiki wake Davide.
70 (Monga mmene ananenera kudzera mwa aneneri oyera),
71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu
ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,
72 kuonetsa chifundo kwa makolo athu
ndi kukumbukira pangano lake loyera,
73 lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abrahamu:
74 kutilanditsa ife mʼdzanja la adani athu,
ndi kutipanga ife timutumikire Iye mopanda mantha,
75 mʼchiyero ndi mʼchilungamo masiku athu onse.
76 “Ndipo iwe mwana wanga udzatchedwa mneneri wa Wammwambamwamba;
pakuti udzapita patsogolo pa Ambuye kukonza njira yake,
77 kupatsa anthu ake chidziwitso cha chipulumutso
kudzera mwa chikhululukiro cha machimo awo,
78 chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu,
ndipo kuwala kwa dzuwa kudzafikira ife kuchokera kumwamba,
79 kuwalira iwo okhala mu mdima
ndi mu mthunzi wa imfa,
kutsogolera mapazi athu mu njira yamtendere.”
Kuyamika ndi Pemphero
3 Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. 4 Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe 5 chifukwa mwakhala mukundithandiza polalikira Uthenga Wabwino kuyambira tsiku loyamba mpaka tsopano. 6 Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.
7 Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu. 8 Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.
9 Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, 10 kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu. 11 Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.
Yohane Mʼbatizi Akonza Njira
3 Mʼchaka cha 15 mu ulamuliro wa Tiberiyo Kaisara, Pontiyo Pilato ali bwanamkubwa wa Yudeya, Herode ankalamulira ku Galileya, mʼbale wake Filipo ankalamulira ku Iturea ndi ku dera la Trakoniti, ndipo Lusaniyo ankalamulira ku Abilene. 2 Inalinso nthawi ya mkulu wa ansembe wa Anasi ndi Kayafa, pamene mawu a Mulungu anabwera kwa Yohane mwana wa Zakariya mʼchipululu. 3 Iye anapita ku dziko lonse lozungulira mtsinje wa Yorodani, nalalikira ubatizo wa kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo. 4 Monga analembera mʼbuku la Yesaya mneneri kuti:
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.
5 Chigwa chilichonse chidzadzazidwa
ndipo phiri lililonse ndi mtunda uliwonse zidzasalazidwa,
misewu yokhotakhota idzawongoledwa,
ndi njira zosasalala zidzasalazidwa.
6 Ndipo anthu onse adzaona chipulumutso cha Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.