Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 11:1-9

Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya

11 Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese
    ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye
    Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,
    Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,
    Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.

Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
    kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,
    adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.
Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;
    atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake
    ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.

Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,
    kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,
mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi
    ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,
    ana awo adzagona pamodzi,
    ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,
    ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga
    pa phiri lopatulika la Yehova,
pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova
    monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.

Mika 4:8-13

Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga,
    iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni,
ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe;
    ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”

Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula,
    kodi ulibe mfumu?
Kodi phungu wako wawonongedwa,
    kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?
10 Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
    ngati mayi pa nthawi yake yobereka,
pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda
    ndi kugona kunja kwa mzindawo.
Udzapita ku Babuloni;
    kumeneko udzapulumutsidwa,
kumeneko Yehova adzakuwombola
    mʼmanja mwa adani ako.

11 Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu
    yasonkhana kulimbana nawe.
Iwo akuti, “Tiyeni timudetse,
    maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”
12 Koma iwo sakudziwa
    maganizo a Yehova;
iwo sakuzindikira cholinga chake,
    Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.

13 “Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,
    pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo;
ndidzakupatsa ziboda zamkuwa
    ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.”

Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova,
    chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.

Luka 7:31-35

31 “Kodi ndingawafanizire chiyani anthu a mʼbado uno? Ali ngati chiyani? 32 Ali ngati ana amene akukangana pa msika, ena akufunsa anzawo kuti,

“ ‘Ife tinakuyimbirani chitoliro,
    koma inu simunavine.
Tinakuyimbirani nyimbo zamaliro,
    koma inu simunalire.’

33 Pakuti Yohane Mʼbatizi sanabwere kudzadya buledi kapena kumwa vinyo, koma inu mumati, ‘Ali ndi chiwanda.’ 34 Mwana wa Munthu anabwera nadya ndi kumwa, ndipo inu mukuti, ‘Ali ndi dyera komanso ndi woledzera, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa.’ 35 Ndipo nzeru zimaoneka zolondola mwa ana ake onse.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.