Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
31 “Masiku akubwera,” akutero Yehova,
“pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
32 Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
ngakhale ndinali mwamuna wawo,”
akutero Yehova.
33 “Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
ndipo iwo adzakhala anthu anga.
34 Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’
chifukwa onse adzandidziwa Ine,
kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”
akutero Yehova.
“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo
ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
10 Chifukwa chakuti Yesu Khristu anachita zimene Mulungu anafuna kuti achite, ndife oyeretsedwa ndi nsembe ya thupi lake, limene analipereka kamodzi kokha.
11 Wansembe aliyense amayimirira tsiku ndi tsiku nʼkutumikira, ndipo amapereka nsembe imodzimodzi mobwerezabwereza, nsembe zimene sizingathe kuchotsa machimo. 12 Koma pamene wansembe uyu anapereka kamodzi kokha nsembe imodzi yokha chifukwa cha machimo, Iye anakhala pansi ku dzanja lamanja la Mulungu. 13 Kumeneko akudikira tsono kuti Mulungu asandutse adani ake kukhala chopondapo mapazi ake. 14 Chifukwa cha nsembe imodzi Iye anasandutsa angwiro kwamuyaya iwo amene akuwayeretsa.
15 Mzimu Woyera nayenso akuchitira umboni za zimenezi kwa ife. Poyamba Iye anati,
16 “Ili ndi pangano limene ndidzachita nawo
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika malamulo anga mʼmitima mwawo,
ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo mwawo.”
17 Ndipo akutinso:
“Sindidzakumbukiranso konse
machimo awo ndi zolakwa zawo.”
18 Ndipo pamene machimo akhululukidwa, sipafunikanso nsembe yoperekedwa chifukwa cha machimowo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.