Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Deuteronomo 34

Mose Amwalira

34 Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani. Dera lonse la Nafutali, dziko lonse la Efereimu ndi Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kukafika kumadzulo kwa nyanja, Negevi ndi chigawo chonse kuchokera ku Chigwa cha Yeriko, Mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”

Choncho Mose mtumiki wa Yehova anamwalira kumeneko ku Mowabu, monga momwe ananenera Yehova. Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. Mose anamwalira ali ndi zaka 120, koma maso ake ankaonabe ndipo anali amphamvu. Aisraeli analira maliro a Mose mʼchikhwawa cha Mowabu kwa masiku makumi atatu mpaka nthawi ya kulira maliro ndi kukhuza inatha.

Tsono Yoswa, mwana wa Nuni anadzazidwa ndi mzimu wanzeru chifukwa nʼkuti Mose atamusanjika manja. Choncho Aisraeli anamumvera ndipo anachita zomwe Yehova analamula Mose.

10 Kuyambira nthawi imeneyi, mu Israeli simunakhalepo mneneri wina aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova amayankhula naye maso ndi maso. 11 Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse. 12 Ndithudi palibe mneneri wina aliyense amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zofanana ndi zomwe Mose anachita pamaso pa Aisraeli onse.

Masalimo 90:1-6

BUKU LACHINAYI

Masalimo 90–106

Pemphero la Mose munthu wa Mulungu.

90 Ambuye, mwakhala muli malo athu okhalamo
    pa mibado yonse.
Mapiri asanabadwe,
    musanalenge nʼkomwe dziko lapansi ndi dziko lonse,
    kuyambira muyaya mpaka muyaya Inu ndinu Mulungu.

Inu mumabwezera anthu ku fumbi,
    mumati, “Bwerera ku fumbi iwe mwana wa munthu.”
Pakuti zaka 1,000 pamaso panu
    zili ngati tsiku limene lapita
    kapena ngati kamphindi ka usiku.
Inu mumasesa anthu mʼtulo ta imfa,
    iwo ali ngati udzu watsopano wa mmawa,
ngakhale kuti mmawa umaphuka watsopano,
    pofika madzulo wauma ndi kufota.

Masalimo 90:13-17

13 Lezani mtima Inu Yehova! Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
    Achitireni chifundo atumiki anu.
14 Mutikhutitse mmawa ndi chikondi chanu chosatha,
    kuti tiyimbe ndi chimwemwe ndi kukhala okondwa masiku athu onse.
15 Tisangalatseni masiku ambiri monga masiku amene mwatisautsa,
    kwa zaka zambiri monga momwe tinaonera mavuto.
16 Ntchito zanu zionetsedwe kwa atumiki anu,
    kukongola kwanu kwa ana awo.

17 Kukoma mtima kwa Ambuye Mulungu wathu kukhale pa ife;
    tikhazikitsireni ntchito ya manja athu;
    inde, khazikitsani ntchito ya manja athu.

1 Atesalonika 2:1-8

Utumiki wa Paulo ku Atesalonika

Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa. Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu.

Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu.

Mateyu 22:34-46

Lamulo Lalikulu Koposa

34 Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi. 35 Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati, 36 “Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?” 37 Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. 38 Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse. 39 Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ 40 Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”

Kodi Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41 Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti, 42 “Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”

43 Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,

44 “Ambuye anati kwa Ambuye wanga:
    ‘Khala pa dzanja langa lamanja
mpaka ndiyike adani ako
    pansi pa mapazi ako.’

45 Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?” 46 Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.