Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
106 Tamandani Yehova.
Yamikani Yehova chifukwa ndi wabwino;
pakuti chikondi chake ndi chosatha.
2 Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova
kapena kumutamanda mokwanira?
3 Odala ndi amene amasunga chilungamo,
amene amachita zolungama nthawi zonse.
4 Mundikumbukire Yehova, pamene mukuonetsa kukoma mtima kwanu kwa anthu anu,
bwerani mudzandithandize pamene mukuwapulumutsa iwo,
5 kuti ndidzasangalale ndi chuma cha anthu anu osankhika,
kuti ndidzakhale nacho chimwemwe cha anthu anu
ndi kukhala pamodzi ndi cholowa chanu pa kukutamandani.
6 Ife tachimwa monga momwe anachitira makolo athu;
tachita zolakwa ndipo tachita moyipa.
19 Iwo anapanga mwana wangʼombe pa Horebu
ndi kulambira fano loyengedwa kuchokera ku chitsulo.
20 Anasinthanitsa ulemerero wawo
ndi fano la ngʼombe yayimuna imene imadya udzu.
21 Anayiwala Mulungu amene anawapulumutsa,
amene anachita zinthu zazikulu mu Igupto,
22 zozizwitsa mʼdziko la Hamu
ndi machitidwe ake woopsa pa Nyanja Yofiira.
23 Choncho Iye anawawuza kuti adzawawononga,
pakanapanda Mose, mtumiki wake wosankhidwa,
kuyima pamaso pake,
ndi kuletsa mkwiyo wake kuti usawawononge.
Kutsimikizira kwa Pangano
24 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali. 2 Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.”
3 Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” 4 Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena.
Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 5 Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano. 6 Mose anatenga theka la magazi ndi kuyika mʼmbale, ndipo theka linalo analiwaza pa guwa lansembe. 7 Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.”
8 Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.”
Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo
5 Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. 2 Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. 3 Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. 4 Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.
5 Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,
“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”
Mawu Otsiriza
12 Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu. 13 Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni. 14 Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.