Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:41-48

Wawi

41 Chikondi chanu chosasinthika chibwere kwa ine, Inu Yehova,
    chipulumutso chanu monga mwa lonjezo lanu;
42 ndipo ndidzayankha amene amandinyoza,
    popeza ndimadalira mawu anu.
43 Musakwatule mawu a choonadi mʼkamwa mwanga,
    pakuti ndakhazikitsa chiyembekezo changa mʼmalamulo anu.
44 Ndidzasunga malamulo anu nthawi zonse,
    ku nthawi za nthawi.
45 Ndidzayendayenda mwaufulu,
    chifukwa ndinafunafuna malangizo anu.
46 Ndidzayankhula za umboni wanu pamaso pa mfumu
    ndipo sindidzachititsidwa manyazi,
47 popeza ndimakondwera ndi malamulo anu
    chifukwa ndimawakonda.
48 Ndikweza manja anga ku malamulo anu, ku malamulo amene ndimawakonda,
    ndipo ndimalingalira malangizo anu.

Deuteronomo 26:16-27:7

Tsatirani Malamulo a Yehova

16 Yehova Mulungu wanu akukulamulani lero lino kuti mutsate malangizo ndi malamulo ake ndipo muwasunge mosamalitsa ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 17 Mwanena motsimikiza lero lino kuti Yehova ndiye Mulungu wanu ndi kuti mudzayenda mʼnjira zake, kusunga malangizo, malamulo ndi zonse akukulamulani ndi kutinso mudzamumvera. 18 Ndipo Yehova wanenetsa lero lino kuti inu ndinu anthu ake, chuma chake chamtengowapatali monga momwe analonjezera, ndipo mukuyenera kusunga malamulo ake onse. 19 Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.

Guwa Lansembe ku Phiri la Ebala

27 Mose ndi akuluakulu a Israeli analamula anthu kuti, “Sungani malamulo onse amene ndikukupatsani lero lino. Mukawoloka mtsinje wa Yorodani kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, muyimiritse miyala ingapo ikuluikulu ndi kuyikulungiza. Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani. Ndipo mukawoloka Yorodani muyimike miyala iyi pa Phiri la Ebala monga momwe ndikukulamulirani lero lino ndipo muyikulungize. Pamenepo mumange guwa lansembe la miyala la Yehova Mulungu wanu. Musagwiritse ntchito chida chilichonse chachitsulo pa miyalapo. Mumange guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu ndi miyala yakutchire ndi kuperekerapo nsembe yopsereza kwa Yehova Mulungu wanu. Muperekerepo nsembe zopereka za chiyanjano, muzidye ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

Mateyu 19:16-22

Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu

16 Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”

17 Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”

18 Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”

Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19 lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”

20 Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?”

21 Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”

22 Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.