Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 20:1-4

Malamulo Khumi

20 Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:

“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”

“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko.

Eksodo 20:7-9

“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi.

Eksodo 20:12-20

12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

13 “Usaphe.

14 “Usachite chigololo.

15 “Usabe.

16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.

17 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

18 Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”

20 Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”

Masalimo 19

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

19 Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu;
    thambo limalalikira ntchito za manja ake.
Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri,
    usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru.
Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse;
    liwu lawo silimveka.
Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi,
    mawuwo amafika mpaka
kumalekezero a dziko lapansi.
    Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake,
    ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano.
Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo
    ndi kuzungulira mpaka mbali inanso;
    palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake.

Lamulo la Yehova ndi langwiro,
    kutsitsimutsa moyo.
Maumboni a Yehova ndi odalirika,
    amapereka nzeru kwa wopanda nzeru.
Malangizo a Yehova ndi olungama,
    amapereka chimwemwe mu mtima.
Malamulo a Yehova ndi onyezimira,
    amapereka kuwala.
Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro,
    chimakhala mpaka muyaya.
Maweruzo a Yehova ndi owona
    ndipo onse ndi olungama;
10 ndi a mtengowapatali kuposa golide,
    kuposa golide weniweni;
ndi otsekemera kuposa uchi,
    kuposa uchi wochokera pa chisa chake.
11 Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo;
    powasunga pali mphotho yayikulu.

12 Ndani angathe kudziwa zolakwa zake?
    Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika.
13 Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa;
    iwo asandilamulire.
Kotero ndidzakhala wosalakwa,
    wopanda mlandu wa tchimo lalikulu.

14 Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga
    zikhale zokondweretsa pamaso panu,
    Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.

Afilipi 3:4-14

ngakhale kuti ineyo ndili ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupizo.

Ngati pali winanso amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zokwanira kudalira zinthu za thupi, ineyo ndili ndi zifukwa zoposa pamenepo. Ndinachita mdulidwe pa tsiku lachisanu ndi chitatu nditangobadwa. Ndine wa mtundu wa Israeli, wa fuko la Benjamini, Mhebri wa Ahebri, kunena za malamulo, ndinali Mfarisi. Kunena za changu changa, ndinkazunza mpingo. Kunena za chilungamo chopezeka chifukwa chotsata malamulo, ineyo ndinali wopanda cholakwa.

Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. 10 Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake 11 kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.

Kuthamanga Mpaka Kumapeto pa Mpikisano wa Liwiro

12 Sikuti ndazipeza kale zonsezi, kapena kuti ndakhala kale wangwiro, koma ndikuthamangabe ndi kuyesetsa kuti ndipeze chimene Khristu Yesu anandiyitanira. 13 Abale, sindidziyesera ndekha kuti ndachipeza kale chimenechi. Koma chinthu chimodzi chimene ndimachita, nʼkuyiwala zamʼmbuyo ndi kuthamangira molimbika zinthu zimene zili mʼtsogolo mwanga. 14 Ndikuthamangira kokathera mpikisanowo kuti ndikalandire mphotho imeneyi kumwamba, imene Mulungu anandiyitanira mwa Khristu Yesu.

Mateyu 21:33-46

Fanizo la Alimi

33 “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. 34 Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.

35 “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. 36 Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. 37 Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.

38 “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ 39 Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.

40 “Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”

41 Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”

42 Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti:

“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana,
    womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya.
Ambuye wachita izi,
    ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’

43 “Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake. 44 Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”

45 Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo. 46 Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.