Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 99

99 Yehova akulamulira,
    mitundu ya anthu injenjemere;
Iye wakhala pa mpando wake waufumu, pakati pa akerubi,
    dziko lapansi ligwedezeke.
Mʼziyoni wamkulu ndi Yehova;
    Iye ndi wokwezeka pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.
Anthu atamande dzina lanu lalikulu ndi loopsa kwambiri,
    Iye ndi woyera.

Mfumu yamphamvu, iyo imakonda chilungamo
    Inu mwakhazikitsa khalidwe losakondera;
mwachita zolungama ndi zoyenera mwa Yakobo.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mulambireni pa mapazi ake;
    Iye ndi woyera.

Mose ndi Aaroni anali ena mwa ansembe ake,
    Samueli anali pamodzi ndi iwo amene anayitana pa dzina lake;
iwo anayitana Yehova
    ndipo Iyeyo anawayankha.
Iye anayankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo;
    iwo anasunga malamulo ake ndi zophunzitsa zomwe anawapatsa.

Inu Yehova Mulungu wathu,
    munawayankha iwo;
Inu kwa Israeli munali Mulungu wokhululuka,
    ngakhale munawalanga pa zochita zawo zoyipa.
Kwezani Yehova Mulungu wathu
    ndipo mumulambire pa phiri lake loyera,
    pakuti Yehova Mulungu wathu ndi woyera.

Eksodo 31:1-11

Bezaleli ndi Oholiabu

31 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi: Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti, tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani, guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake, 10 ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe, 11 ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.”

1 Petro 5:1-5

Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo

Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.

Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,

“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,
    koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.