Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 38

Salimo la Davide. Kupempha.

38 Yehova musandidzudzule mutapsa mtima
    kapena kundilanga muli ndi ukali.
Pakuti mivi yanu yandilasa,
    ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.
Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa;
    mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.
Kulakwa kwanga kwandipsinja
    ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.

Mabala anga akuwola ndipo akununkha
    chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.
Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri;
    tsiku lonse ndimangolira.
Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika,
    mulibe thanzi mʼthupi langa.
Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu;
    ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.

Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,
    kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.
10 Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha;
    ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.
11 Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga;
    anansi anga akhala kutali nane.
12 Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo,
    oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga;
    tsiku lonse amakonza zachinyengo.

13 Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve,
    monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;
14 Ndakhala ngati munthu amene samva,
    amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.
15 Ndikudikira Inu Yehova;
    mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.
16 Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere
    kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”

17 Pakuti ndili pafupi kugwa,
    ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.
18 Ndikuvomereza mphulupulu zanga;
    ndipo ndavutika ndi tchimo langa.
19 Ambiri ndi adani anga amphamvu;
    amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.
20 Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino
    amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

21 Inu Yehova, musanditaye;
    musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.
22 Bwerani msanga kudzandithandiza,
    Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.

Yesaya 30:18-26

18 Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
    iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
    Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!

19 Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. 20 Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. 21 Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” 22 Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”

23 Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. 24 Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. 25 Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. 26 Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.

Machitidwe a Atumwi 14:8-18

Ku Lusitra ndi ku Derbe

Ku Lusitra kunali munthu wolumala miyendo, amene sanayendepo chibadwire chake. Iyeyu, amamvetsera pamene Paulo amayankhula. Paulo anamuyangʼanitsitsa ndipo anaona kuti anali ndi chikhulupiriro choti achiritsidwe nacho. 10 Ndipo Paulo anamuyitana mofuwula nati, “Imirira!” Atamva zimenezi, munthuyo anayimirira, nayamba kuyenda.

11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazi, linafuwula mʼChilukaoniya kuti, “Milungu yatitsikira yooneka ngati anthu!” 12 Barnaba anamutcha Zeusi ndipo Paulo anamutcha Herimesi chifukwa ndiye amatsogolera kuyankhula. 13 Wansembe wa Zeusi amene nyumba yopembedzera Zeusiyo inali kunja pafupi ndi mzindawo, anabweretsa ngʼombe yayimuna yovekedwa nkhata za maluwa pa chipata cha mzindawo chifukwa iyeyo pamodzi ndi anthu ena onse aja amafuna kudzipereka nsembe kwa Paulo ndi Barnaba.

14 Koma Barnaba ndi Paulo atamva zimenezi, anangʼamba zovala zawo, nathamangira pakati pa gulu la anthuwo, akufuwula kuti, 15 “Anthu inu, bwanji mukuchita zimenezi? Ifenso ndife anthu monga inu nomwe. Ife takubweretserani Uthenga Wabwino, kuti musiye zinthu zachabezi ndi kutsata Mulungu wamoyo, amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo. 16 Kale Iye analola anthu a mitundu ina yonse kutsata njira zawozawo. 17 Komabe wakhala akudzichitira yekha umboni: Iye amaonetsa kukoma mtima kwake pogwetsa mvula kuchokera kumwamba ndi zipatso pa nyengo yake. Amakupatsani chakudya chambiri ndipo amadzaza mitima yanu ndi chimwemwe.” 18 Ngakhale ndi mawu awa, anavutika kuletsa gulu la anthu kuti asapereke nsembe kwa iwo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.