Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Molingana ndi seminiti. Salimo la Davide.
6 Inu Yehova, musandidzudzule mu mkwiyo wanu,
kapena kundilanga mu ukali wanu.
2 Ndichitireni chifundo Inu Yehova, pakuti ndalefuka;
Inu Yehova chiritseni, pakuti mafupa anga ali pa ululu waukulu.
3 Moyo wanga uli pa mazunzo aakulu.
Mpaka liti, Inu Yehova, mpaka liti?
4 Tembenukani Inu Yehova, ndipo mundilanditse;
pulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chosasinthika.
5 Palibe amene amakukumbukirani pamene wamwalira;
Amakutamandani ndani ali ku manda?
6 Ine ndatopa ndi kubuwula;
usiku wonse pa bedi panga pamadzaza ndi misozi yanga;
ndimanyowetsa pogona panga ndi misozi.
7 Maso anga atupa chifukwa cha chisoni;
akulephera kuona chifukwa cha adani anga.
8 Chokani kwa ine inu nonse amene mumachita zoyipa,
pakuti Yehova wamva kulira kwanga.
9 Yehova wamva kupempha kwanga kofuna chifundo;
Yehova walandira pemphero langa.
10 Adani anga onse adzachita manyazi ndipo adzakhala ndi mantha;
adzabwerera msangamsanga mwa manyazi.
Akhate Anayi Awulula za Kuthawa kwa Aaramu
3 Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa? 4 Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.”
5 Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe, 6 pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!” 7 Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo.
8 Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso.
9 Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”
10 Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.”
Maphwando a Mafano ndi Mgonero wa Ambuye
14 Choncho abwenzi anga okondedwa, lekani kupembedza mafano. 15 Ndikuyankhula kwa a anthu anzeru zawo, nokha muweruze pa zimene ndikunenazi. 16 Pamene tidalitsa chikho cha Mgonero wa Ambuye, mothokoza Mulungu, kodi sitikugawana magazi a Khristu? Nanga buledi amene timanyemayo, kodi sitikugawana thupi la Khristu? 17 Pakuti buledi ndi mmodzi yekha, ifenso ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, popeza tonse timagawana buledi mmodzi yemweyo.
18 Taganizirani zimene amachita Aisraeli. Kodi onse amene amadya zoperekedwa nsembe, samachita nawo miyambo ya pa guwapo? 19 Kodi ndikutanthauza kuti nsembe zoperekedwa kwa mafano ndi kanthu konse, kapena kuti mafano ndi kanthu konse? 20 Ayi. Nsembe za osakhulupirira zimaperekedwa kwa ziwanda, osati kwa Mulungu, ndipo sindikufuna kuti muziyanjana ndi ziwandazo. 21 Simungamwe chikho cha Ambuye, ndi kukamweranso chikho cha ziwanda. Simungadyere pa tebulo la Ambuye ndiponso la ziwanda. 22 Kodi tikufuna kuwutsa mkwiyo wa Ambuye? Kodi ndife amphamvu kuposa Iye?
Ufulu wa Munthu Wokhulupirira
23 Mutha kunena kuti, “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zili za phindu. “Zinthu zonse nʼzololedwa,” komatu si zonse zimathandiza. 24 Munthu aliyense asafunefune zokomera iye yekha, koma zokomeranso ena.
25 Idyani nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 26 Popeza kuti, “Dziko lapansi ndi la Ambuye ndi zonse za mʼmenemo ndi zake.”
27 Ngati wosakhulupirira akuyitanani kuti mukadye naye, inuyo ndi kuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni ndipo musakafunse mafunso okhudzana ndi chikumbumtima chanu. 28 Koma ngati wina akuwuzani kuti, “Izi zaperekedwa nsembe,” musadye zimenezo, pofuna kuthandiza amene wakuwuzaniyo komanso chifukwa cha chikumbumtima. 29 Ndikunena za chikumbumtima cha winayo osati chanu. Tsono mungafunse kuti, nʼchifukwa chiyani ufulu wanga ukuphwanyidwa chifukwa cha chikumbumtima cha munthu wina? 30 Ngati ndikuyamika Mulungu chifukwa cha chakudya, nanga munthu angandinyoze bwanji pa zinthu zomwe ndayamikira nazo Mulungu?
31 Nʼchifukwa chake chilichonse mungadye kapena kumwa, kapena chimene mungachite, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. 32 Musakhumudwitse aliyense, kaya ndi Myuda, Mgriki, kapena mpingo wa Mulungu. 33 Mu zonse ndikuyesetsa kukondweretsa aliyense mʼnjira iliyonse. Popeza sindikufunafuna zokondweretsa ine ndekha koma zokomera ambiri kuti apulumutsidwe.
11 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.