Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

Levitiko 14:21-32

21 “Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. 22 Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.

23 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe. 24 Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25 Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 26 Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere, 27 ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 28 Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula. 29 Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova. 30 Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, 31 imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.

32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.

Mateyu 26:6-13

Yesu Adzozedwa ku Betaniya

Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.

Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”

10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 11 Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 12 Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 13 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.