M’Cheyne Bible Reading Plan
Yakobo Alandira Madalitso kwa Isake
27 Isake atakalamba maso ake anachita khungu mwakuti sankatha kuona. Iye anayitana mwana wake wamkulu Esau nati kwa iye, “Mwana wanga.”
Iye anayankha, “Ine abambo.”
2 Isake anati, “Tsopano ine ndakalamba, ndipo sindidziwa tsiku langa lakufa. 3 Tsono tenga zida zako, muvi wako ndi uta, pita kuthengo ukandiphere nyama. 4 Undikonzere chakudya chabwino monga muja ndimakonderamu ndipo ubwere nacho kwa ine kuti ndidye ndi kuti ndikudalitse ndisanamwalire.”
5 Koma Rebeka amamvetsera pamene Isake amayankhula ndi mwana wake Esau. Esau atanyamuka kupita kuthengo kukaphera abambo ake nyama, 6 Rebeka anati kwa mwana wake Yakobo, “Taona ndamva abambo ako akuwuza mʼbale wako Esau kuti, 7 ‘Bweretsere nyama yakutchire ndipo undikonzere chakudya chokoma kuti ndidye; kuti ndikudalitse pamaso pa Yehova ndisanamwalire.’ 8 Tsopano mwana wanga, mvetsetsa ndipo uchite zimene ndikuwuze: 9 Pita ku khola, ukatenge ana ambuzi abwino awiri, kuti ndikonzere abambo ako chakudya chokoma monga amakondera. 10 Kenaka upite nacho chakudyacho kwa abambo ako kuti adye ndi kukudalitsa asanafe.”
11 Koma Yakobo anati kwa Rebeka amayi ake, “Komatu mʼbale wanga Esau ndi munthu wa khungu la ubweya zedi, ndipo ine ndine munthu wa khungu losalala. 12 Mwina abambo anga adzandikhudza, ndipo ndidzaoneka kuti ndawapusitsa. Tsono ndizadzitengera temberero mʼmalo mwa madalitso.”
13 Amayi ake anati kwa iye, “Mwana wanga, temberero limenelo ligwere ine. Iwe ungochita zimene ine ndikukuwuza; pita kanditengere timbuzito.”
14 Choncho anapita nakatenga timbuzito ndi kubwera nato kwa amayi ake. Choncho Rebeka anaphika chakudya chokoma monga momwe Isake amakondera. 15 Tsono Rebeka anatenga zovala zabwino kwambiri za Esau mwana wake wamkulu zimene zinali mʼnyumba namuveka Yakobo. 16 Anamuvekanso manja ake ndi khosi lake ndi zikopa za mwana wambuzi. 17 Kenaka, anamupatsa Yakobo chakudya chokoma chija chimene anaphika pamodzi ndi buledi.
18 Yakobo anapita kwa abambo ake ndipo anati, “Abambo anga.”
Ndipo anayankha, “Eya, kodi ndiwe mwana wanga uti?”
19 Yakobo anati kwa abambo ake, “Ndine Esau mwana wanu woyamba. Ndachita monga munandiwuzira. Chonde dzukani ndi kukhala tsonga kuti mudyeko nyama ndakukonzeraniyi kuti tsono mundidalitse.”
20 Isake anafunsa mwana wake, “Wayipeza msanga chotere bwanji mwana wanga?”
Iye anayankha, “Yehova Mulungu wanu anandithandiza kuti ndiyipeze.”
21 Pamenepo Isake anati kwa Yakobo, “Tabwera pafupi ndikukhudze mwana wanga, kuti ndidziwedi ngati uli mwana wanga Esau kapena ayi.”
22 Yakobo anasendera kufupi ndi abambo ake Isake ndipo anamukhudza nati, “Mawuwa ndi mawu a Yakobo koma mikonoyi ndi mikono ya Esau.” 23 Sanamuzindikire, popeza mikono yake inali ndi ubweya ngati ya mʼbale wake Esau; choncho anamudalitsa. 24 Isake anafunsa, “Kodi ndiwedi mwana wanga Esau?”
Yakobo anayankha, “Inde ndine.”
25 Ndipo iye anati, “Mwana wanga, patseko nyama yakoyo ndidye kuti ndikudalitse.”
Yakobo anabwera ndi nyama ija kwa Isake ndipo anadya. Kenaka anamupatsanso vinyo ndipo anamwa. 26 Tsono Isake anati kwa Yakobo, “Bwera kuno mwana wanga undipsompsone.”
27 Choncho anapita namupsompsona. Apa Isake anamva fungo la zovala zake, ndipo anamudalitsa nati,
“Haa, fungo la mwana wanga
lili ngati fungo la munda
umene Yehova waudalitsa.
28 Mulungu akugwetsere mame akumwamba
ndipo minda yako ibale tirigu wambiri
ndi vinyo watsopano.
29 Mitundu ya anthu ikutumikire iwe
ndipo anthu akugwadire iwe.
Ukhale wolamula abale ako,
ndipo ana aamuna a amayi ako akugwadire.
Amene akutemberera iwe atembereredwe
ndipo amene adalitsa iwe adalitsike.”
30 Isake atatsiriza kudalitsa Yakobo, atangochoka pamaso pa abambo akewo, Esau anabwera kuchokera kosaka kuja. 31 Nayenso anakonza chakudya chokoma nabwera nacho kwa abambo ake. Ndipo anati kwa iye, “Chonde abambo, dzukani mukhale tsonga kuti mudye nyamayi ndi kuti mundidalitse.”
32 Abambo ake, Isake, anamufunsa kuti, “Ndiwe yani?”
Iye anayankha, “Ndine mwana wanu woyamba Esau.”
33 Isake ananjenjemera kwambiri nati, “Nanga ndani uja anakapha nyama kutchire nʼkudzandipatsa? Ine ndadya kale, ndadya nyamayo iwe utangotsala pangʼono kubwera ndipo ndamudalitsa ndipo adzakhaladi wodalitsika.”
34 Esau atamva mawu a abambo ake, analira mokweza ndi mowawidwa mtima nati kwa abambo ake, “Inenso dalitseni abambo anga!”
35 Koma iye anati, “Mʼbale wako anabwera mwachinyengo ndipo watenga madalitso ako.”
36 Esau anati, “Kodi nʼchifukwa chake iyeyu dzina lake lili Yakobo eti? Aka nʼkachiwiri kundinyenga: Anatenga ukulu wanga, pano watenga madalitso anga!” Kenaka anafunsa, “Kodi simunandisungireko ena madalitsowo?”
37 Koma Isake anamuyankha nati, “Ndamudalitsa iye kuti akhale wokulamulira iwe. Ndaperekanso abale ake onse kuti akhale omutumikira iye, ndipo ndamudalitsa ndi tirigu wambiri, ndi vinyo watsopano. Ndiye ndingakuchitirenso chiyani mwana wanga?”
38 Esau anati kwa abambo ake, “Kodi muli ndi dalitso limodzi lokhali, abambo anga? Inenso mundidalitse chonde abambo anga!” Pomwepo Esau analira mokuwa.
39 Tsono Isake abambo ake anamuyankha kuti,
“Malo ako okhalapo
sadzabala dzinthu,
ndipo mvula sidzagwa pa minda yako.
40 Udzakhala ndi moyo podalira lupanga
ndipo udzatumikira mʼbale wako.
Koma idzafika nthawi
pamene udzakhala mfulu
udzachotsa goli lake mʼkhosi mwako.”
Yakobo Athawira kwa Labani
41 Ndipo Esau anamusungira chiwembu Yakobo chifukwa cha madalitso amene abambo ake anamupatsa. Esau anati kwa iye yekha, “Masiku olira abambo anga ayandikira; pambuyo pake ndidzamupha mʼbale wangayu Yakobo.”
42 Pamene Rebeka anamva zimene mwana wake wamkulu Esau ankaganiza, anayitanitsa Yakobo nati kwa iye, “Mʼbale wako Esau akulingalira zakuti akuphe kuti akulipsire. 43 Tsopano mwana wanga, chita zimene ndinene: Nyamuka tsopano, uthawire kwa mlongo wanga Labani ku Harani. 44 Ukakhale naye kwa kanthawi mpaka mkwiyo wa mʼbale wako utatsika. 45 Tsono mkwiyo wa mʼbale wakoyo ukadzatsika ndi kuyiwala zonse wamuchitirazi, ndidzatuma munthu kuti adzakutenge. Nanga nditayirenji nonse awiri nthawi imodzi?”
46 Tsono Rebeka anati kwa Isake, “Ine sindikukondwera nawo anamwali a Chihiti. Ndipo ngati Yakobo angapeze mbeta kuno mwa anamwali a Chihitiwa, ndiye kuli bwino kungofa.”
Chiwembu cha Ayuda pa Yesu
26 Yesu atamaliza kuyankhula zonsezi, anati kwa ophunzira ake, 2 “Monga mukudziwa, kwatsala masiku awiri kuti Paska ifike ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kuti apachikidwe.”
3 Pamenepo akulu a ansembe ndi akuluakulu anasonkhana ku nyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa, 4 ndipo anapangana kuti amugwire Yesu mobisa ndi kumupha. 5 Ndipo anati, “Osati nthawi yaphwando chifukwa pangabuke chipolowe pakati pa anthu.”
Yesu Adzozedwa ku Betaniya
6 Yesu ali ku Betaniya mʼnyumba Simoni Wakhate, 7 mayi wina anabwera kwa Iye ndi botolo la mafuta onunkhira a mtengowapatali, amene anathira pa mutu pake Iye akudya pa tebulo.
8 Ophunzira ataona izi anayipidwa nafunsa kuti, “Chifukwa chiyani akuwononga chotere? 9 Mafuta amenewa akanatha kugulitsidwa pa mtengo waukulu, ndipo ndalama zake zikanaperekedwa kwa osauka.”
10 Yesu podziwa izi anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Wandichitira Ine chinthu chabwino. 11 Osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. 12 Pamene wathira mafuta onunkhirawa pa thupi langa, wachita izi kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. 13 Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwinowu udzalalikidwa ku dziko lonse lapansi, zimene wachitazi zidzanenedwanso pomukumbukira.”
Yudasi Avomereza Kupereka Yesu
14 Pamenepo mmodzi wa khumi ndi awiriwo wotchedwa Yudasi Isikarioti anapita kwa akulu a ansembe 15 nafunsa kuti, “Kodi mundipatsa chiyani ngati nditamupereka Iye kwa inu?” Pamenepo anamuwerengera ndalama zokwanira masiliva makumi atatu. 16 Kuyambira pamenepo Yudasi anafunafuna nthawi yabwino yoti amupereke Yesu.
Paska Womaliza ndi Mgonero wa Ambuye
17 Pa tsiku loyamba laphwando la buledi wopanda yisiti, ophunzira anabwera kwa Yesu ndi kumufunsa kuti, “Kodi mukufuna tikakonze kuti malo odyera Paska?”
18 Iye anayankha kuti, “Pitani mu mzinda kwa munthu wakutiwakuti ndipo kamuwuzeni kuti, ‘Aphunzitsi akuti, nthawi yanga yoyikidwa yayandikira. Ine ndidzadya phwando la Paska ndi ophunzira anga ku nyumba kwako.’ ” 19 Pamenepo ophunzira ake anachita monga momwe Yesu anawawuzira ndipo anakonza Paska.
20 Kutada, Yesu ndi ophunzira ake khumi ndi awiriwo anakhala pa tebulo nʼkumadya. 21 Akudya, Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka.”
22 Iwo anamva chisoni kwambiri ndipo anayamba kuyankhulana naye mmodzimmodzi nati, “Kodi nʼkukhala ine Ambuye?”
23 Yesu anayankha nati, “Iye amene akusunsa mʼmbale pamodzi ndi Ine, yemweyo adzandipereka. 24 Mwana wa Munthu adzaphedwa monga mmene kunalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene apereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
25 Ndipo Yudasi amene anamupereka Iye anati, “Monga nʼkukhala ine Aphunzitsi?”
Yesu anayankha nati, “Iwe watero.”
26 Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, idyani; ili ndi thupi langa.”
27 Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo nati, “Imwani nonsenu. 28 Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri kuti akhululukidwe machimo. 29 Ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mtengo wa mpesa kuyambira lero mpaka tsiku ilo pamene ndidzamwenso mwatsopano ndi inu mu ufumu wa Atate anga.”
30 Atayimba nyimbo, anatuluka kupita ku phiri la Olivi.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:
“ ‘Kantha mʼbusa,
ndipo nkhosa zidzabalalika.’
32 Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
33 Petro anayankha nati, “Ngakhale onsewa atakuthawani, ine ndekha ayi.”
34 Yesu anayankha nati, “Zoonadi, ndikukuwuza kuti usiku omwe uno, asanalire tambala, udzandikana Ine katatu.”
35 Koma Petro ananenetsa nati, “Ngakhale kutakhala kufa nanu pamodzi, sindidzakukanani.” Ndipo ophunzira onse ananena chimodzimodzi.
Yesu mu Getsemani
36 Kenaka Yesu anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo anawawuza kuti, “Khalani pano pamene Ine ndikukapemphera apo.” 37 Anatenga Petro ndi ana awiri a Zebedayo, ndipo anayamba kumva chisoni ndi kuvutika mu mtima. 38 Pamenepo anawawuza kuti, “Moyo wanga uli ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo dikirani pamodzi ndi Ine.”
39 Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi chafufumimba napemphera kuti, “Atate anga, ngati ndikotheka, chikho ichi chichotsedwe kwa Ine. Koma osati monga mmene ndifunira, koma monga mufunira Inu.”
40 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nawapeza ali mtulo. Iye anafunsa Petro kuti, “Kodi anthu inu, simukanakhala maso pamodzi ndi Ine kwa ora limodzi lokha? 41 Khalani maso ndi kupemphera kuti musagwe mʼmayesero. Mzimu ukufuna koma thupi ndi lofowoka.”
42 Anachokanso nakapemphera kachiwiri kuti, “Atate anga, ngati chikhochi sichingandichoke, mpaka nditamwa, kufuna kwanu kuchitike.”
43 Atabweranso anawapeza ali mtulo chifukwa zikope zawo zinalemedwa ndi tulo. 44 Choncho anawasiya napitanso kukapemphera kachitatu nanenanso chimodzimodzi.
45 Kenaka anabwera kwa ophunzira ake nati kwa iwo, “Kodi mukanagonabe ndi kupumula? Taonani, ora layandikira ndipo Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa ochimwa. 46 Imirirani, tiyeni tizipita! Wondipereka Ine wafika!”
Amugwira Yesu
47 Akuyankhula choncho, Yudasi mmodzi mwa khumi ndi awiriwo anafika. Pamodzi ndi iye panali gulu lalikulu la anthu ali ndi mikondo ndi zibonga otumidwa ndi akulu a ansembe ndi akuluakulu. 48 Womuperekayo anawawuziratu chizindikiro anthuwo kuti, “Amene ndidzapsompsona ndi iyeyo; mugwireni.” 49 Pamenepo Yudasi anapita kwa Yesu nati, “Moni, Aphunzitsi!” Ndipo anapsompsona Iye.
50 Yesu anayankha kuti, “Bwenzi langa, chita chimene wabwerera.”
Pamenepo anthuwo anabwera patsogolo namugwira Yesu ndi kumumanga. 51 Pa chifukwa ichi, mmodzi wa anzake a Yesu anagwira lupanga lake, nalisolola ndi kutema wantchito wa mkulu wa ansembe, nadula khutu lake.
52 Yesu anati kwa iye, “Bwezera lupanga lako mʼchimake, chifukwa onse amene amapha ndi lupanga adzafa ndi lupanga. 53 Kodi mukuganiza kuti sindingathe kupempha Atate anga ndipo nthawi yomweyo nʼkundipatsa magulu a angelo oposa khumi ndi awiri? 54 Koma nanga malemba akwaniritsidwa bwanji amene akuti ziyenera kuchitika motere?”
55 Pa nthawi yomweyo Yesu anati kwa gululo, “Kodi ndine mtsogoleri wa anthu owukira kuti mwabwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mʼNyumba ya Mulungu kuphunzitsa, koma simunandigwire. 56 Koma zonsezi zachitika kuti zolembedwa ndi aneneri zikwaniritsidwe.” Pamenepo ophunzira anamusiya nathawa.
Yesu ku Bwalo la Akulu Ayuda
57 Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana. 58 Koma Petro anamutsatira Iye patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Analowa nakhala pansi pamodzi ndi alonda kuti aone zotsatira.
59 Akulu a ansembe ndi akulu olamulira Ayuda amafunafuna umboni wonama wofuna kuphera Yesu. 60 Koma sanathe kupeza uliwonse, angakhale kuti mboni zambiri zabodza zinapezeka.
Pomalizira mboni ziwiri zinabwera patsogolo. 61 Ndipo zinati, “Munthu uyu anati, ‘Ndikhoza kupasula Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso mʼmasiku atatu.’ ”
62 Pamenepo mkulu wa ansembe anayimirira nati kwa Yesu, “Kodi suyankha? Kodi umboni umenewu ndi otani umene anthu awa akupereka kukutsutsa Iwe?” 63 Koma Yesu anakhalabe chete.
Mkulu wa ansembe anati kwa Iye, “Ndikulamulira Iwe ndi lumbiro pamaso pa Mulungu wa Moyo: utiwuze ife ngati ndiwe Khristu Mwana wa Mulungu.”
64 Yesu anayankha nati, “Mwanena ndinu. Koma ndikunena kwa inu nonse: mʼtsogolomo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera ndi mitambo ya kumwamba.”
65 Pamenepo mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zake nati, “Wanyoza Mulungu! Tifuniranji mboni zina? Taonani, tsopano mwamva mwano wake. 66 Mukuganiza bwanji?”
Iwo anayankha kuti, “Ayenera kuphedwa!”
67 Kenaka anamulavulira kumaso namumenya ndi zibakera. Ena anamumenya makofi. 68 Ndipo anati, “Tanenera kwa ife, Khristu. Wakumenya ndani?”
Petro Amukana Yesu
69 Tsopano Petro anakhala ku bwalo la nyumbayo, ndipo mtsikana wantchito anabwera kwa iye nati, “Iwenso unali ndi Yesu wa ku Galileya.”
70 Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”
71 Kenaka anachoka kupita ku khomo la mpanda, kumene mtsikana wina anamuonanso nawuza anthu nati, “Munthu uyu anali ndi Yesu wa ku Nazareti.”
72 Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”
73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”
74 Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!”
Nthawi yomweyo tambala analira. 75 Ndipo Petro anakumbukira mawu amene Yesu anayankhula kuti, “Tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.” Ndipo anatuluka panja nakalira kwambiri.
Chiwembu cha Hamani Chopha a Yuda
3 Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse. 2 Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira.
3 Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?” 4 Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda.
5 Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri. 6 Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira.
7 Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara.
8 Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere. 9 Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.”
10 Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. 11 Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.”
12 Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake. 13 Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo. 14 Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo.
15 Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka.
Mawu a Paulo Pamaso pa Mfumu Agripa
26 Ndipo Agripa anawuza Paulo kuti, “Takulola kuti unene mawu ako.” Paulo anatambasula dzanja lake nayamba kudziteteza kuti, 2 “Mfumu Agripa ine ndikudziyesa wa mwayi kuyima pamaso panu lero lino ndi kudziteteza, kutsutsa zonse zimene Ayuda andinenera, 3 ndipo makamaka chifukwa inu mukudziwa bwino miyambo yonse ya Chiyuda ndiponso zonse zimene amatsutsana. Nʼchifukwa chake ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.
4 “Ayuda onse akudziwa za moyo wanga mmene ndakhalira kuyambira ndili mwana, kuchokera pachiyambi cha moyo wanga mʼdziko lathu ndiponso mu Yerusalemu. 5 Iwo akundidziwa kuyambira kalekale ndipo angathe kuchitira umboni kuti ndakhala ndili Mfarisi moyo wanga wonse, mmodzi wa gulu limene limasamala chipembedzo chathu koposa. 6 Ndipo tsopano ndikuyimbidwa mlandu lero chifukwa cha chiyembekezo changa pa zimene Mulungu analonjeza makolo athu. 7 Ili ndi lonjezo limene mafuko athu khumi ndi awiri akuyembekezera kuti likwaniritsidwe pamene akupembedza Mulungu molimbika usana ndi usiku. Wolemekezeka Mfumu, nʼchifukwa cha chiyembekezo chimenechi Ayuda kuti akundiyimba mlandu. 8 Nʼchifukwa chiyani ena a inu mukuganiza kuti nʼkosatheka kuti Mulungu aukitse akufa?
9 “Inenso ndimaganiza kuti ndimayenera kuchita zinthu zambiri pofuna kuthana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10 Ndipo izi ndi zimene ndinazichita ku Yerusalemu. Ndi ulamuliro wa akulu a ansembe, ine ndinayika mʼndende oyera mtima ambiri, ndipo pamene amaphedwa, ine ndimavomereza. 11 Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze.
12 “Pa ulendo wina wotere, ndikupita ku Damasiko ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa akulu a ansembe, 13 Wolemekezeka Mfumu, nthawi ya masana pamene ndimayenda pa msewu, ndinaona kuwala kuchokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa kutandizungulira ine pamodzi ndi anzangawo. 14 Tonse tinagwa pansi ndipo ndinamva mawu mʼChihebri akuti, ‘Saulo, Saulo chifukwa chiyani ukundizunza Ine? Nʼkovuta kulimbikira mtunda wopanda madzi.’ ”
15 Ndipo ine ndinafunsa kuti, “Ndinu ndani Ambuye?”
Ambuye anayankha kuti, “Ndine Yesu, amene iwe ukumuzunza. 16 Tsopano dzuka ndipo imirira. Ine ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki ndiponso mboni ya zimene waziona za Ine ndiponso zimene ndidzakuonetsa. 17 Ine ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu a mtundu wako ndiponso mwa anthu a mitundu ina. Ine ndikukutuma kwa iwo, 18 kuti ukatsekule maso awo kuti atembenuke mtima kuchoka ku mdima ndi kulowa mʼkuwala, kuchoka ku mphamvu za Satana ndi kupita kwa Mulungu, kuti alandire chikhululukiro cha machimo awo ndi kukhala mʼgulu la amene akuyeretsedwa chifukwa chokhulupirira Ine.
19 “Nʼchifukwa chake Mfumu Agripa, sindinakane kumvera masomphenya wochokera kumwamba. 20 Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko, a ku Yerusalemu, a ku Yudeya konse ndi kwa anthu a mitundu inanso, ndinalalikira kuti akuyenera kulapa ndi kutembenukira kwa Mulungu ndikuti aonetse kulapa kwawo mwa ntchito zawo. 21 Ichi nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nafuna kundipha. 22 Koma Mulungu wakhala akundithandiza mpaka lero lino. Ine ndayima pano kuti ndichitire umboni kwa anthu onse otchuka ndi anthu wamba. Ine sindikunena zina zowonjezera koma zimene Aneneri ndi Mose ananena kuti zidzachitika. 23 Iwo ananena kuti Khristu adzamva zowawa ndipo popeza Iye adzakhala woyamba kuuka kwa akufa, adzalalikira za kuwunika kwa anthu a mtundu wake ndiponso kwa anthu a mitundu ina.”
24 Paulo akudziteteza, Festo anakweza mawu nati, “Wazungulira mutu Paulo! Kuphunzira kwako kwakuchititsa misala.”
25 Paulo anayankha nati, “Wolemekezeka Festo, sindine wozungulira mutu. Zimene ndikunena ndi zoona ndiponso za nzeru. 26 Mfumu ikuzidziwa bwino zinthu izi, ndipo ndikuyankhula momasuka kwa iyo. Ine ndikukhulupirira kuti palibe kanthu nʼkamodzi komwe kamene sukukadziwa, chifukwa izi sizinachike mseri. 27 Mfumu Agripa, kodi mumakhulupirira mawu a aneneri? Ine ndikudziwa kuti mumakhulupirira.”
28 Kenaka Agripa anati kwa Paulo, “Kodi ukuganiza kuti mʼkanthawi kochepa kotere ungandikope kuti ndikhale Mkhristu?”
29 Paulo anayankha kuti, “Ngakhale kanthawi kochepa kapena nthawi yayitali, ine ndikupempha kwa Mulungu kuti osati inu nokha koma aliyense amene akundimva lero lino akhale monga ine, kupatulapo maunyolo okhawa.”
30 Mfumu inayimirira pamodzi ndi bwanamkubwa ndi Bernisi ndiponso anthu onse amene anakhala nawo pamodzi. 31 Inatuluka mʼchipindamo, ndipo pamene imayankhula inati, “Munthu uyu sanachite kanthu koyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”
32 Agripa anati kwa Festo, “Munthu uyu akanamasulidwa akanakhala kuti sanapemphe zokaonekera kwa Kaisara.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.