Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Genesis 18

Alendo Atatu a Abrahamu

18 Yehova anadza kwa Abrahamu pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya thundu ya ku Mamre. Abrahamu nʼkuti atakhala pansi pa khoma la tenti yake masana, dzuwa likutentha. Tsono Abrahamu atakweza maso ake patali anangoona anthu atatu atayima cha potero. Atawaona, ananyamuka mofulumira kuti awachingamire. Atafika anaweramitsa mutu pansi mwa ulemu nati, “Ngati mwandikomera mtima, mbuye wanga, musamulambalale mtumiki wanu. Ndikupatseniko timadzi pangʼono kuti nonse musambitse mapazi anu ndi kupumula pansi pa mtengo uwu. Tsono ndikutengereniko kachakudya kuti mudye kuti mwina nʼkupezako mphamvu zopitirizira ulendo wanu. Inu mwafika kumalo kwa mtumiki wanu.”

Ndipo iwo anamuyankha nati, “Zikomo kwambiri, chita monga wanenera.”

Choncho Abrahamu anafulumira kupita kwa Sara mʼtenti nati, “Tafulumira, tenga mabeseni atatu a ufa wosalala, ukande ndi kupanga buledi.”

Kenaka Abrahamu anakatenga mwana wangʼombe wonenepa ndi wofewa bwino ndi kupatsa wantchito wake amene anachita changu kukonza ndiwoyo. Tsono Abrahamu anatenga chambiko, mkaka ndi mwana wangʼombe wokonzedwa uja nazipereka kwa anthu aja. Alendowo akudya, Abrahamu ankawayangʼana atayimirira pansi pa mtengo.

Anthuwo anafunsa Abrahamu kuti, “Mkazi wako Sara ali kuti?”

Iye anati, “Ali mu tentimu.”

10 Tsono mmodzi mwa iwo anati, “Mosakayikira ndidzabweranso pa nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”

Koma Sara amene anali kumbuyo kwa Abrahamu pa khoma la tenti ankamva zonsezi. 11 Abrahamu ndi Sara anali okalamba kale ndipo anali ndi zaka zambiri. Sara nʼkuti atapyola kale pa msinkhu oti nʼkubereka. 12 Choncho anangoseka nati mu mtima mwake, “Kodi munthu wothayitha ngati ine ndingasangalalenso kugona pamodzi ndi mbuye wanga? Mwamuna wanga nayenso ndi wokalamba.”

13 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Nʼchifukwa chiyani Sara anaseka nʼkumati, ‘Moti ine nʼkudzakhaladi ndi mwana mmene ndakalambiramu?’ 14 Kodi pali chimene chikhoza kumukanika Yehova? Pa nthawi yake, ngati yomwe ino chaka chamawa ndidzabweranso, ndipo Sara adzabala mwana wamwamuna.”

15 Koma Sara ndi mantha ananama nati, “Sindinaseke.”

Koma Iye anati, “Inde iwe unaseka.”

Abrahamu Apembedzera Sodomu

16 Kenaka anthu aja ananyamuka ndi kumapita, molunjika ku Sodomu. Ndipo Abrahamu anayenda nawo pamodzi kuwaperekeza. 17 Tsono Yehova anati mu mtima mwake, “Kodi ndingamubisire Abrahamu chimene ndikuti ndichite posachedwa? 18 Abrahamu adzakhaladi mtundu wa anthu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi adzadalitsika kudzera mwa iye. 19 Pakuti ndasankha iyeyu kuti adzatsogolere ana ake ndi a pa banja lake, kuti asunge mawu a Yehova pochita zoyenera ndi zachilungamo. Choncho Yehova adzachita kwa Abrahamu chimene anamulonjeza iye.”

20 Ndipo Yehova anati kwa Abrahamu, “Kulirira Gomora kwakula ndipo tchimo lawo lafika poyipa kwambiri 21 choncho ndikuti ndipiteko ndikaone ngati zimene achita zilidi zoyipa monga mmene madandawulo andipezera Ine. Ngati sizili choncho, ndikadziwa.”

22 Anthu aja anatembenuka nʼkumapita, kulowera ku Sodomu, koma Abrahamu anali chiyimirire pamaso pa Yehova. 23 Kenaka Abrahamu anasendera kufupi ndi Iye nati, “Kodi mudzawonongera kumodzi wolungama ndi woyipa? 24 Nanga bwanji patakhala anthu makumi asanu olungama mu mzindamo? Kodi mudzawonongadi onse osausiyako mzindawo chifukwa cha anthu makumi asanu olungama omwe ali mʼmenemo? 25 Ndithu simungachite zimenezi, kupha anthu olungama pamodzi ndi oyipa. Nʼzosatheka kuti inu nʼkufananitsa olungama ndi oyipa. Kodi woweruza wa dziko lapansi nʼkulephera kuchita chilungamo?”

26 Yehova anati, “Nditapeza anthu makumi asanu olungama mu mzinda wa Sodomu, ndidzasiya malo onsewo osawawononga chifukwa cha iwo.”

27 Ndipo Abrahamu anayankhulanso nati, “Tsono poti ndalimba mtima kuyankhula ndi Ambuye, ngakhale kuti ndine fumbi ndi phulusa chabe, 28 bwanji anthu olungama atacheperapo ndi asanu pa anthu makumi asanu? Kodi mudzawononga mzinda wonse chifukwa cha asanuwo?”

Iye anati, “Nditapezamo anthu 45, sindidzawuwononga.”

29 Kenakanso anayankhula kwa Iye nati, “Bwanji atangopezekamo anthu 40 okha?”

Iye anayankha, “Chifukwa cha anthu 40 amenewa, sindidzatero.”

30 Ndipo Abrahamu anati, “Pepanitu musandipsere mtima Ambuye, koma mundilole kuti ndiyankhule. Nanga mutapezekamo anthu makumi atatu okha?”

Iye anayankha, “Sindidzatero ngati atapezekamo anthu makumi atatu.”

31 Abrahamu anati, “Tsono poti ndalimba mtima chonchi kumayankhula ndi Ambuye, bwanji atangopezeka anthu makumi awiri okha?”

Iye anati, “Chifukwa cha anthu makumi awiriwo, sindidzawuwononga.”

32 Kenaka Abrahamu anati, “Pepani Ambuye musandipsere mtima, ndingoyankhula kamodzi kokhaka basi. Bwanji atangopezeka khumi okha mʼmenemo?”

Iye anayankha nati, “Chifukwa cha khumiwo, sindidzawuwononga.”

33 Yehova atatsiriza kuyankhula ndi Abrahamu, anachoka ndipo Abrahamu anabwerera ku nyumba yake.

Mateyu 17

Maonekedwe Aulemerero a Yesu pa Phiri

17 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.

Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”

Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”

Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.

Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”

10 Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”

11 Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. 12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.” 13 Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.

Yesu Achiritsa Wodwala Matenda Akugwa

14 Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. 15 Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. 16 Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”

17 Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.” 18 Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.

19 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”

20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani. 21 Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”

Yesu Anena za Imfa yake Kachiwiri

22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu. 23 Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.

Yesu Apereka Msonkho

24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”

25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”

Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”

26 Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”

Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.

Nehemiya 7

Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa. Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena. Ine ndinawawuza kuti, “Musalole kuti zipata za Yerusalemu zitsekulidwe mpaka dzuwa litatentha, ndipo alonda asanaweruke aonetsetse kuti atseka zitseko ndi kuzipiringidza. Musankhe alonda pakati pa anthu okhala mu Yerusalemu, ena akhale pa malo pawo ndi ena akhale moyangʼanana ndi nyumba zawo.”

Mndandanda wa Anthu Oyamba Kubwera Kuchokera ku Ukapolo

Tsono mzinda wa Yerusalemu unali wotambasuka ndiponso waukulu koma munali anthu ochepa ndipo nyumba zinali zisanamangidwe. Ndipo Mulungu wanga anayika mu mtima mwanga maganizo oti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, akuluakulu ndi anthu onse kuti alembetse mayina mwa mabanja awo. Ndinapeza buku limene munalembedwa mayina a mabanja a iwo amene anayamba kubwera kuchokera ku ukapolo. Izi ndi zimene ndinazipeza zitalembedwa mʼmenemo:

Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerera kuchokera ku ukapolo amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawatenga ukapolo. Iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake. Anabwera pamodzi ndi atsogoleri awa: Zerubabeli, Yesuwa, Nehemiya, Azariya, Raamiya, Nahamani, Mordekai, Bilisani, Misipereti, Bigivai, Nehumu ndi Baana.

Tsono chiwerengero cha anthu a ku Israeli chinali chotere:

Zidzukulu za Parosi2,172
Zidzukulu za Sefatiya372
10 Zidzukulu za Ara652
11 Zidzukulu za Pahati-Mowabu (kudzera mu mʼbado wa Yesuwa ndi Yowabu)2,818
12 Zidzukulu za Elamu1,254
13 Zidzukulu za Zatu845
14 Zidzukulu za Zakai760
15 Zidzukulu za Binuyi648
16 Zidzukulu za Bebai628
17 Zidzukulu za Azigadi2,322
18 Zidzukulu za Adonikamu667
19 Zidzukulu za Abigivai2,067
20 Zidzukulu za Adini655
21 Zidzukulu za Ateri (kudzera mwa Hezekiya)98
22 Zidzukulu za Hasumu328
23 Zidzukulu za Bezayi324
24 Zidzukulu za Harifu112
25 Zidzukulu za Gibiyoni95.
26 Anthu a ku Betelehemu ndi Netofa188
27 Anthu a ku Anatoti128
28 Anthu a ku Beti-Azimaveti42
29 Anthu a ku Kiriati Yeyarimu Kefira ndi Beeroti743
30 Anthu a ku Rama ndi Geba621
31 Anthu a ku Mikimasi122
32 Anthu a ku Beteli ndi Ai123
33 Anthu a ku Nebo winayo52
34 Ana a Elamu wina1,254
35 Zidzukulu za Harimu320
36 Zidzukulu za Yeriko345
37 Zidzukulu za Lodi, Hadidi ndi Ono721
38 Zidzukulu za Senaya3,930.

39 Ansembe anali awa:

A banja la Yedaya (ndiye kuti zidzukulu za Yesuwa)973
40 Zidzukulu za Imeri1,052
41 Zidzukulu za Pasi-Huri1,247
42 Zidzukulu za Harimu1,017.

43 Alevi anali awa:

A banja la Yesuwa ndi Kadimieli, ndiye kuti zidzukulu za Hodaviya74.

44 Anthu oyimba:

Zidzukulu za Asafu148.

45 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
Salumu, Ateri, Talimoni, Hatita ndi Sobai138.

46 Anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu anali awa:

Zidzukulu za
Ziha, zidzukulu za Hasufa, zidzukulu za Tabaoti,
47 Zidzukulu Kerosi, zidzukulu za Siya, zidzukulu za Padoni
48 Zidzukulu za Lebana za Hagaba, ndi za Salimayi,
49 Zidzukulu za Hanani, zidzukulu za Gideli, zidzukulu za Gahari,
50 Zidzukulu za Reyaya, zidzukulu za Rezini, zidzukulu za Nehoda,
51 Zidzukulu za Gazamu, zidzukulu za Uza, zidzukulu za Paseya,
52 Zidzukulu za Besai, zidzukulu za Meunimu, zidzukulu za Nefusimu,
53 Zidzukulu za Bakibuku, zidzukulu za Hakufa, zidzukulu za Harihuri,
54 Zidzukulu za Baziliti, zidzukulu za Mehida, zidzukulu za Harisa,
55 Zidzukulu za Barikosi, zidzukulu za Sisera, zidzukulu za Tema
56 Zidzukulu za Neziya, ndi zidzukulu za Hatifa.

57 Zidzukulu za antchito a Solomoni:

Zidzukulu za
Sotai, zidzukulu za Sofereti, zidzukulu za Perida
58 zidzukulu za Yaala, zidzukulu za Darikoni, zidzukulu za Gideli,
59 zidzukulu za Sefatiya, zidzukulu za Hatilu
zidzukulu za Pokereti-Hazebaimu ndi zidzukulu Amoni.
60 Anthu onse ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi zidzukulu za antchito a Solomoni analipo392.

61 Ali munsiwa anachokera ku Teli-Mela, Teri-Harisa, Kerubi, Adoni, ndi Imeri, koma sanathe kunena mwa tchutchutchu kuti makolo awo kapena mafuko awo analidi Aisraeli kapena ayi.

62 Zidzukulu za
Delaya, zidzukulu za Tobiya ndi zidzukulu za Nekoda642.

63 Ndiponso ena pakati pa ansembe anali awa:

zidzukulu za

Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai (munthu amene anakwatira mwana wamkazi wa Barizilai wa ku Giliyadi ndipo amatchedwa dzina limenelo).

64 Iwowa anafufuzafufuza mayina awo mʼbuku la mibado ya mabanja awo ndipo sanapeze mayina awo kotero anachotsedwa pa unsembe nawerengedwa ngati odetsedwa pa chipembedzo. 65 Choncho bwanamkubwa anawawuza anthuwo kuti asamadye nawo chakudya china chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mpaka patapezeka wansembe wodziwa kugwiritsa bwino ntchito ya Urimu ndi Tumimu.

66 Chiwerengero chonse cha anthuwa chinali 42,360. 67 Kuwonjezera pamenepa panali antchito awo aamuna ndi aakazi 7,337 ndiponso anthu aamuna ndi aakazi oyimba nyimbo okwanira 245. 68 Panali akavalo 736, abulu angʼonoangʼono 245. 69 Ngamira zawo zinalipo 435 ndipo abulu analipo 6,720.

70 Atsogoleri ena a mabanja anapereka mphatso zothandizira ntchito. Bwanamkubwa anapereka ku thumba losungira chuma, ndalama zagolide za makilogalamu asanu ndi atatu, mabeseni makumi asanu ndi zovala za ansembe 530. 71 Atsogoleri ena amabanja anapereka ku thumba losungira chuma ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndiponso ndalama za siliva zokwana makilogalamu 1,250. 72 Anthu ena onse otsala anapereka ndalama zagolide zokwana makilogalamu 168, ndalama za siliva zokwana makilogalamu 140, ndiponso zovala za ansembe 67.

73 Choncho ansembe, Alevi, alonda a Nyumba ya Mulungu, anthu oyimba nyimbo, ena mwa anthu wamba, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu pamodzi ndi Aisraeli ena onse ankakhala mʼmizinda yawo.

Ezara Awerenga Malamulo

Pofika mwezi wachisanu ndi chiwiri Aisraeli onse anali atakhazikika mʼmizinda yawo.

Machitidwe a Atumwi 17

Paulo ku Tesalonika

17 Atadutsa ku Amfipoli ndi Apoloniya, anafika ku Tesalonika, kumene kunali sunagoge ya Ayuda. Paulo, monga mwachizolowezi chake, analowa mʼsunagoge, ndipo anakambirana nawo Mawu a Mulungu kwa masabata atatu, kuwafotokozera ndi kuwatsimikizira kuti Khristu anayenera kufa ndi kuuka. Iye anati, “Yesu amene ndikukulalikirani ndiye Khristu.” Ena mwa Ayuda anakopeka mtima ndipo anatsatira Paulo ndi Sila, monganso linachitira gulu lalikulu la Agriki woopa Mulungu, pamodzi ndi amayi odziwika ambiri.

Koma Ayuda ena anachita nsanje; kotero anasonkhanitsa anthu akhalidwe loyipa ochokera pa msika ndipo napanga gulu nayambitsa chipolowe mu mzindawo. Anathamangira ku nyumba ya Yasoni kukafuna Paulo ndi Sila kuti awabweretse pa gulu la anthu. Koma atalephera kuwapeza, anakokera Yasoniyo ndi abale ena ku bwalo la akulu a mzindawo akufuwula kuti, “Anthu awa, Paulo ndi Sila, amene akhala akusokoneza dziko lonse lapansi, tsopano afikanso kuno. Yasoni ndiye anawalandira mʼnyumba mwake. Onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara pomanena kuti palinso mfumu ina, yotchedwa Yesu.” Atamva zimenezi, gulu la anthu ndi akulu a mzinda anavutika mu mtima. Iwo analipiritsa Yasoni ndi anzakewo ndipo anawamasula.

Ku Bereya

10 Mdima utagwa, abale anatumiza Paulo ndi Sila ku Bereya. Atafika kumeneko anapita ku sunagoge ya Ayuda. 11 Tsopano anthu a ku Bereya anali akhalidwe labwino kusiyana ndi Atesalonika, pakuti iwo analandira mawu ndi chidwi chachikulu ndipo ankasanthula Malemba tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zimene ankanena Paulozo zinali zoona. 12 Ayuda ambiri anakhulupirira, monga anachitiranso amayi ndi amuna ambiri odziwika a Chigriki.

13 Ayuda a ku Tesalonika atadziwa kuti Paulo akulalikira Mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko, ndi kuwutsa mitima ya anthu nayambitsa chisokonezo. 14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo ku nyanja koma Sila ndi Timoteyo anatsalira ku Bereya. 15 Anthu amene anamuperekeza Paulo nafika naye ku Atene, ndipo anabwerera ku Bereya atawuzidwa kuti Sila ndi Timoteyo amutsatire msanga.

Ku Atene

16 Paulo akudikira Timoteyo ndi Sila ku Atene, anavutika mu mtima kwambiri poona kuti mzindawo unali odzaza ndi mafano. 17 Tsono anakambirana ndi Ayuda ndi Agriki amene amaopa Mulungu mʼsunagoge, komanso anthu amene amapezeka pa msika tsiku ndi tsiku ndi ena amene amakumana nawo. 18 Gulu la Aepikureya ndi Astoiki, anthu anzeru, anayamba kutsutsana naye. Ena a iwo anafunsa kuti, “Kodi wolongololayu akufuna kunena chiyani?” Enanso anati, “Akuoneka ngati akulalikira milungu yachilendo.” Iwo ananena zimenezi chifukwa Paulo amalalikira Uthenga Wabwino wa Yesu ndi kuuka kwa akufa. 19 Kenaka iwo anamutenga nafika naye ku bwalo la Areopagi kumene anamufunsa kuti, “Kodi tingadziweko chiphunzitso chatsopano chimene ukuchifotokozachi? 20 Iwe ukubweretsa zinthu zina zachilendo mʼmakutu mwathu, ndipo ife tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21 Atene onse ndi alendo amene amakhala kumeneko samachita kanthu kena koma kufotokoza ndi kumvera fundo zatsopano.

22 Paulo anayimirira mʼbwalo la Areopagi nati: “Inu anthu a ku Atene! Ine ndikuona kuti mʼnjira zonse ndinu opembedza kwambiri. 23 Pakuti pamene ndimayenda ndi kuona zinthu zimene mumazipembedza, ndapezanso guwa lansembe lolembedwapo kuti, kwa mulungu wosadziwika. Tsopano chimene mumachipembedza osachidziwa ndi chimene ndikuchilalikira.

24 “Mulungu amene analenga dziko lapansi ndiponso zonse zili mʼmenemo ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndipo sakhala mʼnyumba zachipembedzo zomangidwa ndi manja. 25 Ndipo satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti Iye amasowa kanthu, chifukwa Iye ndiye amapereka moyo ndi mpweya kwa anthu onse ndi zina zonse. 26 Kuchoka kwa munthu mmodzi Iye analenga mtundu uliwonse wa anthu, kuti akakhale pa dziko lonse lapansi; ndipo Iye anakonzeratu nthawi yawo ndiponso malo enieni kumene adzakhale. 27 Mulungu anachita izi kuti anthu amufunefune, ndikuti pomufunafunapo amupeze ngakhale kuti Iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 ‘Pakuti timakhala mwa Iye, kuyenda mwa Iye ndi kukhala moyo mwa Iye.’ Monga olemba ndakatulo anu ena akuti, ‘Ife ndi zidzukulu zake.’

29 “Tsono popeza ndife ana a Mulungu, tisaganize kuti umulungu wake ndi wofanana ndi ndalama zagolide, zasiliva, mwala, kapenanso fanizo lopangidwa mwaluso la nzeru za anthu. 30 Nthawi imene anthu sankadziwa, Mulungu anawalekerera koma tsopano akulamulira kuti anthu onse, kulikonse atembenuke mtima. 31 Pakuti Iye wayika tsiku limene adzaweruze dziko lapansi mwa chilungamo kudzera mwa Munthu amene anamusankha. Iye watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”

32 Atamva za kuuka kwa akufa, ena a iwo anaseka, koma enanso anati, “Ife tikufuna tidzamvenso zimenezi tsiku lina.” 33 Ndipo Paulo anatuluka mʼBwalolo. 34 Anthu ena ochepa anamutsatira Paulo ndipo anakhulupirira. Pakati pawo panali Dionisiyo mmodzi wa bwalo la Areopagi ndi mayi wina wotchedwa Damalisi ndi enanso.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.