M’Cheyne Bible Reading Plan
Sarai ndi Hagara
16 Tsono Sarai, mkazi wa Abramu anali asanamuberekere ana Abramuyo. Koma anali ndi wantchito wamkazi wa ku Igupto dzina lake Hagara; 2 ndipo Sarai anati kwa Abramu, “Yehova sanalole kuti ine ndikhale ndi ana. Bwanji mulowe mwa wantchito wanga wamkaziyu kuti mwina ndingaone ana kudzera mwa iyeyu.”
Abramu anamvera Sarai. 3 Tsono Sarai anatenga Hagara wantchito wake wamkazi wa ku Igupto uja namupereka kwa Abramu mwamuna wake kuti akhale mkazi wake. Izi zinachitika Abramu atakhala ku Kanaani zaka khumi. 4 Abramu atalowana ndi Hagara, Hagara uja anatenga mimba.
Pamene Hagara anadziwa kuti anali woyembekezera anayamba kunyoza mbuye wake Sarai. 5 Pamenepo Sarai anati kwa Abramu, “Inu ndinu amene mwandiputira nkhanza zikundichitikirazi. Ndinakupatsani wantchito wanga wamkazi kuti akhale mkazi wanu, ndiye tsopano wayamba kundinyoza ine chifukwa wadziwa kuti ndi woyembekezera. Yehova ndiye amene aweruze pakati pa inu ndi ine.”
6 Abramu anati, “Wantchito wakoyu ali mʼmanja mwako. Chita naye chilichonse chimene ukuganiza kuti ndi chokukomera.” Tsono Sarai anazunza Hagara mpaka anathawa.
7 Mngelo wa Yehova anamupeza Hagara pafupi ndi chitsime mʼchipululu. Chinali chitsime chimene chili mʼmphepete mwa msewu wopita ku Suri. 8 Ndipo mngeloyo anati, “Hagara, iwe wantchito wa Sarai, ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?”
Iye anayankha, “Ndikuthawa mbuye wanga Sarai.”
9 Mngelo wa Yehova anamuwuza kuti, “Bwerera kwa mbuye wako ndipo ukamugonjere. 10 Ndidzakupatsa zidzukulu zambiri zoti munthu sangaziwerenge.”
11 Mngelo wa Yehova uja anamuwuzanso kuti,
“Ndiwe woyembekezera
ndipo udzabala mwana wamwamuna.
Udzamutcha dzina lake Ismaeli,
pakuti Yehova wamva kulira chifukwa cha kuzunzika kwako.
12 Iye adzakhala munthu wa khalidwe ngati mʼmbulu wamisala;
adzadana ndi aliyense
ndipo anthu onse adzadana naye,
adzakhala mwaudani pakati pa abale ake
onse.”
13 Hagara anatcha Yehova amene anamuyankhula uja dzina loti: “Ndinu Mulungu amene mumandiona,” popeza anati, “Ndakumana ndi Yehova atatha kundikomera mtima.” 14 Nʼchifukwa chake chitsime chija chimene chili pakati pa Kadesi ndi Beredi chinatchedwa Beeri-lahai-roi.
15 Tsono Hagara anamuberekera Abramu mwana wamwamuna ndipo Abramu anamutcha mwanayo Ismaeli. 16 Pamene Hagara anamubalira Ismaeli nʼkuti Abramuyo ali ndi zaka 86.
Miyambo ya Makolo
15 Pamenepo Afarisi ena ndi aphunzitsi amalamulo anabwera kwa Yesu kuchokera ku Yerusalemu ndipo anamufunsa kuti, 2 “Chifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya mwambo wa akuluakulu? Iwo sasamba mʼmanja pakudya!”
3 Yesu anayankha kuti, “Nanga chifukwa chiyani inu mumaphwanya lamulo la Mulungu chifukwa cha mwambo wa makolo anu? 4 Pakuti Mulungu anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako’ ndipo ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ 5 Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukalirandira kuchokera kwa ine ndi mphatso yoperekedwa kwa Mulungu,’ 6 iye sakulemekeza nayo abambo ake ndipo ndi khalidwe lotere inu mumapeputsa nalo Mawu a Mulungu chifukwa cha mwambo wanu. 7 Inu anthu achiphamaso, Yesaya ananenera za inu kuti,
8 “ ‘Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
9 Amandilambira Ine kwachabe
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.’ ”
10 Yesu anayitana gulu la anthu nati, “Mverani ndipo zindikirani. 11 Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu sichimuchititsa kukhala woyipa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake, icho ndi chimene chimamuchititsa kukhala woyipa.”
12 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Iye ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukudziwa kuti Afarisi anakhumudwa pamene anamva mawu aja?”
13 Iye anayankha kuti, “Mbewu iliyonse imene Atate anga akumwamba sanadzale idzazulidwa ndi mizu yomwe. 14 Alekeni, ndi atsogoleri osaona. Ngati munthu wosaona atsogolera wosaona mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”
15 Petro anati, “Timasulireni fanizoli.”
16 Yesu anawafunsa kuti, “Kani ngakhale inunso simumvetsa? 17 Kodi inu simudziwa kuti chilichonse cholowa mʼkamwa chimapita mʼmimba ndipo kenaka chimatuluka kunja kwa thupi? 18 Koma zinthu zimene zituluka mʼkamwa zimachokera mu mtima ndipo zimenezi zimamuchititsa munthu kukhala woyipa. 19 Pakuti mu mtima mumatuluka maganizo oyipa, zakupha, zachigololo, zadama, zakuba, zaumboni wonama ndi zachipongwe. 20 Izi ndi zimene zimachititsa munthu kukhala woyipa; koma kudya ndi mʼmanja mosasamba sikumuchititsa munthu kukhala woyipa.”
Mayi wa ku Kanaani
21 Yesu atachoka kumalo amenewo anapita kudera la ku Turo ndi ku Sidoni. 22 Mayi wa Chikanaani wochokera dera la komweko anabwera kwa Iye akulira, nati, “Ambuye, Mwana wa Davide, ndichitireni chifundo! Mwana wanga wamkazi akuzunzika kwambiri ndi chiwanda.”
23 Yesu sanayankhe kanthu. Ndipo ophunzira ake anabwera namupempha Iye kuti, “Muwuzeni achoke chifukwa akulira mofuwula pambuyo pathu.”
24 Iye anayankha kuti, “Ine ndinatumidwa kwa nkhosa zotayika za Israeli zokha.”
25 Mayiyo anabwera ndi kugwada pamaso pake, nati, “Ambuye ndithandizeni!”
26 Iye anayankha kuti, “Sibwino kutenga chakudya cha ana ndi kuponyera agalu.”
27 Mayiyo anati, “Inde Ambuye. Komatu ngakhale agalu amadya nyenyeswa zimene zimagwa kuchokera pa tebulo la mbuye wawo.”
28 Pomwepo Yesu anayankha kuti, “Mayi iwe uli ndi chikhulupiriro chachikulu! Pempho lako lamveka.” Ndipo mwana wake wamkazi anachira nthawi yomweyo.
Yesu Adyetsa Anthu 4,000
29 Yesu anachoka kumeneko napita mʼmbali mwa nyanja ya Galileya. Ndipo anakwera ku phiri nakhala pansi. 30 Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye ndi anthu olumala, osaona, ofa ziwalo, osayankhula ndi ena ambiri nawagoneka pa mapazi ake ndipo Iye anawachiritsa. 31 Anthu ataona osayankhula akuyankhula, ofa ziwalo akuchira, olumala miyendo akuyenda ndi osaona akuona anadabwa kwambiri. Ndipo analemekeza Mulungu wa Israeli.
32 Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala kale ndi Ine masiku atatu ndipo alibe chakudya. Ine sindifuna kuti apite kwawo ndi njala chifukwa angakomoke pa njira.”
33 Ophunzira anayankha kuti, “Ndikuti kumene tingakapeze buledi mʼtchire muno okwanira kudyetsa gulu lotere?”
34 Yesu anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri ndi tinsomba pangʼono.”
35 Iye anawuza gululo kuti likhale pansi. 36 Kenaka anatenga malofu asanu ndi awiri aja ndi tinsombato ndipo atayamika anagawa napatsa ophunzira ake ndipo iwo anagawira anthuwo. 37 Onse anadya ndipo anakhuta. Pomaliza ophunzira anatolera zotsalira nadzaza madengu asanu ndi awiri. 38 Chiwerengero cha anthu amene anadya chinali 4,000 kupatula amayi ndi ana. 39 Yesu atatha kuwuza gululo kuti lipite kwawo, analowa mʼbwato ndipo anapita kudera la Magadala.
Nehemiya Ateteza Anthu Aumphawi
5 Tsono anthu ena ndi akazi awo anayamba kudandaula kwambiri chifukwa cha Ayuda anzawo. 2 Ena ankanena kuti, “Ife ndi ana athu aamuna ndi aakazi, tilipo ochuluka kwambiri. Choncho tikufuna tirigu kuti tidye ndi kukhala ndi moyo.”
3 Panali ena amene ankanena kuti, “Ife tikuchita kupereka minda yathu, mitengo yathu ya mphesa ndi nyumba zathu ngati chikole kuti tipeze tirigu chifukwa njala yakula.”
4 Panalinso ena amene ankanena kuti, “ife tinachita kukongola ndalama zoti tipereke msonkho wa minda ndi mitengo yathu ya mphesa kwa mfumu. 5 Ngakhale kuti ndife amodzi ndi abale athuwa, ndipo ngakhalenso ana athu ndi ofanana ndi ana awo, ife tikukakamiza ana athu kuti akhale akapolo. Ena mwa ana athu aakazi atengedwa kale ukapolo. Ife tilibe mphamvu yochitapo kanthu popeza anthu ena anatenga kale minda yathu ndi mitengo yathu ya mphesa.”
6 Nditamva madandawulo awo ndi zimene amanenazi ndinapsa mtima kwambiri. 7 Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu 8 ndipo ndinati, “Monga zakhaliramu ife tikutha kuwombola abale anthu amene anagulitsidwa ukapolo kwa anthu ena. Kodi tsopano inu mukugulitsanso abale anu kwa anzawo kuti ife tiwumirizidwe kuwawombola?” Iwo anakhala chete, chifukwa sanapeze mawu oti anene.
9 Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi? 10 Ine ndi abale anga ndiponso antchito anga tikuwakongozanso anthuwa ndalama ndi tirigu. Ndipo tiyeni tilekeretu zolandira chiwongoladzanja! 11 Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.”
12 Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.”
Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo. 13 Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!”
Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera.
14 Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. 15 Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu. 16 Ndiponso ndinadzipereka kugwira ntchito yomanga khoma la mzinda wa Yerusalemu popanda ngakhale kugulapo munda. Antchito anganso anasonkhana komweko kuti agwire ntchito ndipo sitinafunenso malo ena.
17 Kuwonjezera apa, ndinkadyetsa Ayuda, akuluakulu kuphatikizanso anthu amene ankabwera kwa ife kuchokera kwa mitundu ya anthu otizungulira okwanira 150. 18 Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu.
19 Kuti zinthu zindiyendere bwino, kumbukirani Yehova Mulungu wanga pa zonse zimene ndachitira anthu awa.
Msonkhano wa ku Yerusalemu
15 Anthu ena ochokera ku Yudeya anafika ku Antiokeya ndipo amaphunzitsa abale kuti, “Ngati simuchita mdulidwe potsata mwambo wa Mose, simungapulumuke.” 2 Zimenezi zinachititsa Paulo ndi Barnaba kuti atsutsane nawo kwambiri. Kotero Paulo ndi Barnaba anasankhidwa pamodzi ndi abale ena kuti apite ku Yerusalemu kukaonana ndi atumwi ndi akulu ampingo kukakambirana za nkhaniyi. 3 Mpingo unawaperekeza, ndipo pamene amadutsa ku Foinike ndi Samariya, iwo anafotokoza momwe a mitundu ina anatembenukira mtima. Nkhani imeneyi inakondweretsa kwambiri abale onse. 4 Atafika ku Yerusalemu, iwo analandiridwa ndi mpingo, pamodzi ndi atumwi ndiponso akulu ampingo. Paulo ndi Barnaba anawafotokozera zonse zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.
5 Kenaka, okhulupirira ena amene kale anali a gulu la Afarisi anayimirira ndipo anati, “Anthu a mitundu ina ayenera kuchita mdulidwe ndi kusunga malamulo a Mose.”
6 Atumwi ndi akulu ampingo anasonkhana kuti akambirane za nkhaniyi. 7 Atakambirana kwambiri Petro anayimirira, ndipo anawayankhula nati: “Abale, mukudziwa kuti masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu kuti anthu a mitundu ina amve kuchokera pakamwa panga mawu a Uthenga Wabwino ndi kukhulupirira. 8 Mulungu amene amadziwa mtima wa munthu, Iye anaonetsa kuti anawalandira powapatsa Mzimu Woyera, monga momwe anachita kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse pakati pa ife ndi iwo, pakuti anayeretsa mitima yawo mwachikhulupiriro. 10 Tsopano, chifukwa chiyani mukuyesa Mulungu poyika goli mʼkhosi la ophunzira, limene ngakhale ife kapena makolo athu sangathe kulisenza? 11 Osatero! Ife tikukhulupirira kuti tinapulumutsidwa mwachisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, monga iwonso anachitira.”
12 Gulu lonse linakhala chete pamene amamvetsera Barnaba ndi Paulo akuwawuza za zizindikiro zodabwitsa zimene Mulungu anazichita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13 Iwo atatha kuyankhula, Yakobo anayankhula nati: “Abale, tandimverani. 14 Simoni watifotokozera mmene Mulungu poyamba paja anaonetsa kukhudzidwa kwake pomwe anatenga anthu a mitundu ina kukhala ake. 15 Mawu a aneneri akuvomereza zimenezi, monga kwalembedwa kuti,
16 “ ‘Zitatha izi Ine ndidzabwerera
ndipo ndidzamanganso nyumba ya Davide imene inagwa.
Ndidzakonzanso malo amene anagumuka,
ndi kuyimanganso,
17 kuti anthu otsalawo afunefune Ambuye,
ndi anthu onse a mitundu ina amene atchedwa ndi dzina langa,
akutero Ambuye, amene amachita zinthu zimenezi
18 zinaululidwa kuyambira kalekale.’
19 “Chifukwa chake, ine ndikuweruza kuti tisamavute anthu a mitundu ina amene atembenuka mtima kutsata Mulungu. 20 Koma tiwalembere iwo, kuwawuza kuti asadye chakudya choperekedwa kwa mafano, apewenso dama, asadyenso nyama zochita kupotola kapena kudya magazi. 21 Pakuti malamulo a Mose akhala akulalikidwa mu mzinda uliwonse, kuyambira kalekale ndipo amawerengedwa mʼMasunagoge tsiku la Sabata.”
Kalata Yopita kwa Anthu a Mitundu ina
22 Pamenepo atumwi ndi akulu ampingo, pamodzi ndi mpingo onse, anagwirizana zosankha anthu ena pakati pawo kuti awatume ku Antiokeya pamodzi ndi Paulo ndi Bamaba. Iwo anasankha Yudasi, wotchedwa Barsaba ndi Sila, anthu awiri amene anali atsogoleri pakati pa abale, 23 kuti akapereke kalata yonena kuti,
Kuchokera kwa atumwi ndi akulu ampingo, abale anu,
Kwa anthu a mitundu ina okhulupirira a ku Antiokeya, Siriya ndi Kilikiya:
Tikupereka moni.
24 Ife tamva kuti anthu ena ochokera pakati pathu, amene sitinawatume anakusokonezani maganizo ndi kukuvutitsani ndi zimene amakuwuzani. 25 Tsono ife tagwirizana kuti, tisankhe anthu ena ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi abale athu okondedwa Paulo ndi Barnaba, 26 anthu amene anapereka moyo wawo chifukwa cha dzina la Ambuye athu Yesu Khristu. 27 Nʼchifukwa chake, tikutumiza Yudasi ndi Sila kuti adzachitire umboni ndi mawu a pakamwa pawo za zimene ife talemba. 28 Pakuti zinakomera Mzimu Woyera ndiponso ife kuti tisakusenzetseni katundu wina, kupatula zoyenera zokhazi: 29 Mupewe kudya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano, musadye magazi, kapena nyama yopha mopotola ndiponso musachite dama. Mudzachita bwino mukapewa zimenezi.
Tsalani bwino.
30 Anthu aja anatumidwa ndipo anafika ku Antiokeya, kumene anasonkhanitsa mpingo pamodzi napereka kalatayo. 31 Anthuwo anawerenga kalatayo ndipo abalewo anakondwa chifukwa cha mawu ake achirimbikitso. 32 Yudasi ndi Sila amene analinso aneneri, ananena zambiri zowalimbikitsa ndi kuwapatsa mphamvu abalewo. 33 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, abale aja anatsanzikana nawo mwamtendere kuti abwerere kwa amene anawatuma. 34 Koma Sila anasankha kuti akhale komweko. 35 Koma Paulo ndi Barnaba anatsalira ku Antiokeya kumene iwo pamodzi ndi ena ambiri anaphunzitsa ndi kulalikira Mawu a Ambuye.
Paulo Asiyana ndi Barnaba
36 Patapita masiku ena Paulo anati kwa Barnaba, “Tiyeni tibwerere kuti tikaone abale ku mizinda yonse imene tinalalika Mawu a Ambuye ndipo tikaone mmene akuchitira.” 37 Barnaba anafuna kutenga Yohane, wotchedwanso Marko, kuti apite nawo. 38 Koma Paulo anaganiza kuti sichinali cha nzeru kumutenga Yohane chifukwa iye anawathawa ku Pamfiliya ndipo sanapitirire nawo pa ntchito. 39 Iwo anatsutsana kwambiri kotero kuti anapatukana. Barnaba anatenga Marko ndipo anakwera sitima ya pamadzi kupita ku Kupro. 40 Paulo anasankha Sila. Abale atawapempherera kwa Ambuye kuti alandire chisomo, ananyamuka. 41 Iye anadutsa ku Siriya ndi ku Kilikiya kupita akulimbikitsa mipingo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.