M’Cheyne Bible Reading Plan
Kuyesedwa kwa Abrahamu
22 Nthawi ina zitatha izi, Mulungu anamuyesa Abrahamu. Iye anati, “Abrahamu!”
Ndipo iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
2 Ndipo Mulungu anati, “Tenga Isake, mwana wako yekhayo amene umamukonda ndi kupita naye ku dziko la Moriya. Ukamupereke iye ngati nsembe yopsereza pa limodzi la mapiri a kumeneko limene ndidzakuwuza.”
3 Abrahamu anadzuka mmamawa wake namangirira chokhalira pa bulu. Atadula nkhuni zokwanira zowotchera nsembe yopsereza, Abrahamu, antchito ake awiri pamodzi ndi Isake ananyamuka kupita kumalo kumene Mulungu anamuwuza Abrahamu. 4 Pa tsiku lachitatu, Abrahamu anakweza maso ake ndipo anaona malowo chapatali. 5 Ndipo Abrahamu anati kwa antchito ake aja, “Bakhalani pano ndi buluyu. Ine ndi mnyamatayu tipita uko kukapemphera, koma tibweranso.”
6 Abrahamu anatenga nkhuni za nsembe yopsereza zija namusenzetsa mwana wake Isake, ndipo iye mwini anatenga moto ndi mpeni. Pamene awiriwo amayendera pamodzi, 7 Isake anati kwa abambo ake Abrahamu, “Abambo?”
Abrahamu anayankha, “Ee mwana wanga.”
Isake anafunsa, “Moto ndi nkhuni zilipo, koma nanga mwana wankhosa wa nsembe yopsereza ali kuti?”
8 Abrahamu anayankha, “Mwana wanga, Mulungu adzipezera yekha mwana wankhosa wa nsembe yopsereza.” Ndipo awiriwo anapitiriza ulendo.
9 Atafika pamalo pamene Mulungu anamuwuza paja, Abrahamu anamangapo guwa lansembe nayika nkhuni pamwamba pa guwapo. Kenaka anamumanga mwana wake Isake namugoneka paguwapo, pamwamba pa nkhuni paja. 10 Kenaka Abrahamu anatambasula dzanja lake natenga mpeni kuti aphe mwana wake. 11 Koma mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba nati, “Abrahamu! Abrahamu!”
Iye anayankha kuti, “Ee Ambuye.”
12 Mngeloyo anati, “Usatambasulire mwanayo dzanja lako kuti umuphe, pakuti tsopano ndadziwa kuti iwe umaopa Mulungu. Iwe sunandimane mwana wako mmodzi yekhayo.”
13 Abrahamu anatukula maso ake ndipo anaona nkhosa yamphongo itakoledwa ndi nyanga zake mu ziyangoyango. Iye anapita nakatenga nkhosa ija ndikuyipha ngati nsembe yopsereza mʼmalo mwa mwana wake. 14 Choncho Abrahamu anatcha malo amenewa kuti Yehova-Yire (Wopereka). Ndipo mpaka lero amatchula malowo kuti ndi “Pa phiri la Yehova wopereka.”
15 Mngelo wa Yehova anayitana Abrahamu kuchokera kumwamba kachiwiri 16 ndipo anati, “Ndikulumbira mwa Ine ndekha kuti popeza wachita zimenezi, wosandikaniza mwana wako mmodzi yekhayu, 17 ndidzakudalitsa ndithu ndipo ndidzakupatsa zidzukulu zochuluka ngati nyenyezi zamlengalenga komanso ngati mchenga wa mʼmphepete mwa nyanja. Zidzukulu zako zidzalanda mizinda ya adani awo, 18 ndipo kudzera mwa chidzukulu chako, mitundu yonse ya anthu pa dziko lapansi idzadalitsika, chifukwa iwe wandimvera.”
19 Kenaka Abrahamu anabwerera kumene anasiya antchito ake kuja nanyamukira nawo pamodzi kupita ku Beeriseba. Ndipo Abrahamu anakhala ku Beeriseba.
Ana Aamuna a Nahori
20 Patapita nthawi, Abrahamu anamva kuti, “Milika nayenso anaberekera Nahori, mʼbale wake ana. 21 Woyamba anali Huzi ndipo kenaka mʼbale wake Buzi. Anaberekanso Kemueli, amene anali abambo ake a Aramu. 22 Ana ena ndi Kesede Hazo, Pilidasi, Yidilafi ndi Betueli.” 23 Betueli anabereka Rebeka. Milika anaberekera Nahori, mʼbale wake wa Abrahamu, ana aamuna asanu ndi atatu amenewa. 24 Mkazi wake wachiwiri, dzina lake Reuma, anamubaliranso Nahori ana awa: Teba, Gahamu, Tahasi ndi Maaka.
Yesu Alowa mu Yerusalemu
21 Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2 nawawuza kuti, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine. 3 Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.”
4 Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:
5 “Uza mwana wamkazi wa Ziyoni,
taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,
yofatsa ndi yokwera pa bulu,
pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”
6 Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. 7 Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo. 8 Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. 9 Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,
“Hosana Mwana wa Davide!”
“Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!”
“Hosana mmwambamwamba!”
10 Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”
11 Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.”
Yesu mʼNyumba ya Mulungu
12 Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. 13 Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”
14 Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa. 15 Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.
16 Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?”
Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti,
“Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda
mwatuluka mayamiko?”
17 Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona.
Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu
18 Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19 Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.
20 Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”
21 Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22 Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”
Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake
23 Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”
24 Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi. 25 Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”
Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’ 26 Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”
27 Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.”
Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”
Fanizo la Ana Amuna Awiri
28 “Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’
29 “Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.
30 “Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.
31 “Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?”
Anamuyankha nati, “Woyambayo.”
Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.” 32 Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.
Fanizo la Alimi
33 “Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. 34 Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.
35 “Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. 36 Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. 37 Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.
38 “Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ 39 Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.
40 “Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”
41 Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”
42 Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti:
“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana,
womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya.
Ambuye wachita izi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’
43 “Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake. 44 Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”
45 Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo. 46 Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.
Nzika Zatsopano za mu Yerusalemu
11 Nthawi imeneyo atsogoleri a anthu ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse anachita maere kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse kuti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulika. Anthu asanu ndi anayi otsalawo ankakhala mʼmidzi yawo. 2 Anthu anayamikira onse amene anadzipereka kuti azikhala mu Yerusalemu.
3 Aisraeli wamba, ansembe, Alevi, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ndiponso zidzukulu za antchito a Solomoni ankakhala mʼmidzi yawo, aliyense mu dera lake. Koma atsogoleri a chigawo cha Yuda anali atakhazikika mu Yerusalemu. 4 Ku Yerusalemu kunkakhalanso anthu ena a mafuko a Yuda ndi Benjamini.
Ena mwa zidzukulu za Yuda ndi awa:
Ataya, mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalaleli. Onsewa anali ana a Perezi. 5 Ena ndi awa: Maaseya mwana wa Baruki, mwana wa Koli-Hoze mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yowaribu, Zekariya mwana wa Msiloni. 6 Zidzukulu zonse za Perezi, anthu amphamvu zawo amene ankakhala ku Yerusalemu analipo anthu okwanira 468.
7 Nazi zidzukulu za Benjamini:
Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yowedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itieli, mwana wa Yesaiya. 8 Abale ake anali Gabayi ndi Salaya. Onse pamodzi anali 928. 9 Yoweli mwana wa Zikiri ndiye anali mtsogoleri wawo, ndipo Yuda mwana wa Hasenuya ndiye amayangʼanira chigawo cha chiwiri cha mzinda.
10 Ansembe anali awa:
Yedaya mwana wa Yowaribu; Yakini; 11 Seraya mwana wa Hilikiya mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi amene anali woyangʼanira Nyumba ya Mulungu, 12 ndi abale awo, amene ankagwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu. Onse pamodzi anali 822. Panalinso Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya, 13 ndi abale ake, amene anali atsogoleri a mabanja. Onse pamodzi anali 242. Kuphatikiza apo panalinso Amasisai mwana wa Azaireli, mwana wa Ahazayi, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri 14 ndi abale ake. Onse pamodzi anali 128 ndipo anali anthu olimba mtima kwambiri. Mtsogoleri wawo wamkulu anali Zabidieli mwana wa Hagedolimu.
15 Alevi anali awa:
Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni. 16 Sabetayi ndi Yozabadi anali atsogoleri amene ankayangʼanira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu. 17 Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu ndiye anali wotsogolera pa mapemphero achiyamiko. Panalinso Bakibukiya amene anali wachiwiri pakati pa abale ake. Kuwonjezera apo panalinso Abida mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni. 18 Alevi onse amene anali mu mzinda woyera analipo 284.
19 Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali awa:
Akubu, Talimoni ndi abale awo. Onse pamodzi anali 172.
20 Aisraeli ena onse pamodzi ndi ansembe ndi Alevi ankakhala mʼmizinda ya Yuda, ndipo aliyense ankakhala mʼdera la makolo ake.
21 Koma antchito a ku Nyumba ya Mulungu ankakhala pa phiri la Ofeli, ndipo Ziha ndi Gisipa ndiwo anali kuwayangʼanira.
22 Wamkulu wa Alevi mu Yerusalemu anali Uzi mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Uzi anali mmodzi wa zidzukulu za Asafu, amene anali oyimba nyimbo pa nthawi zachipembedzo mʼNyumba ya Mulungu. 23 Pakuti mfumu inalamula kuti tsiku ndi tsiku pa nthawi zachipembedzo oyimba nyimbowo azikhalapo.
24 Petahiya mwana wa Mesezabeli, mmodzi mwa zidzukulu za Zera mwana wa Yuda ndiye ankayimirira Aisraeli pa bwalo la mfumu ya Perisiya.
25 Anthu ena a fuko la Yuda ankakhala ku Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ku Diboni ndi midzi yake, ku Yekabizeeli ndi midzi yake, 26 ku Yesuwa, Molada, Beti-Peleti, 27 Hazari-Suwali, Beeriseba ndi midzi yawo. 28 Ku Zikilagi, Mekona ndi midzi yawo, 29 ku Eni-Rimoni, Zora, Yarimuti, 30 Zanowa, Adulamu ndi midzi yake, ku Lakisi ndi minda yake, ku Beeriseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.
31 Nazonso zidzukulu za Benjamini zinkakhala mʼdera lawo kuyambira ku Geba mpaka ku Mikimasi, Ayiya, Beteli ndi midzi yake, 32 ku Anatoti, Nobu ndi Ananiya, 33 ku Hazori, Rama ndi Gitaimu, 34 ku Hadidi, Zeboimu ndi Nebalati, 35 ku Lodi, Ono ndi ku chigwa cha Amisiri.
36 Magulu ena a Alevi a ku Yuda ankakhala ku Benjamini.
Paulo Apita ku Yerusalemu
21 Titalawirana nawo, tinachoka kumeneko mʼsitima ya pamadzi, ndipo tinayenda molunjika mpaka kufika ku Kosi. Mmawa mwake tinapita ku Rode, kuchokera kumeneko tinapita ku Patara. 2 Kumeneko tinapeza sitima yapamadzi yopita ku Foinike. Choncho tinalowamo nʼkunyamuka. 3 Tinaona chilumba cha Kupro ndipo tinadutsa kummwera kwake nʼkupita ku Siriya. Tinakayima ku Turo chifukwa sitima yathuyo imayenera kusiya katundu kumeneko. 4 Tinafunafuna ophunzira kumeneko, ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku asanu ndi awiri. Iwowa, mwa Mzimu Woyera anakakamiza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 5 Koma nthawi yathu itatha, tinachokako ndi kupitiriza ulendo wathu. Ophunzira onse pamodzi ndi akazi awo ndi ana anatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Ndipo kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja ndi kupemphera. 6 Titatsanzikana, tinalowa mʼsitima ija, iwowo anabwerera ku nyumba zawo.
7 Ife tinapitiriza ulendo wathu wochokera ku Turo mpaka tinafika ku Ptolemayi. Kumeneko tinalonjera abale ndi kukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tinachoka mmawa mwake, mpaka tinakafika ku Kaisareya. Tinapita kukakhala mʼnyumba ya mlaliki Filipo, amene anali mmodzi mwa atumiki a mpingo asanu ndi awiri aja. 9 Iye anali ndi ana aakazi anayi osakwatiwa amene anali ndi mphatso ya uneneri.
10 Titakhala kumeneko masiku ambiri, kunabwera mneneri wina wochokera ku Yudeya dzina lake Agabu. 11 Atafika kwa ife, anatenga lamba wa Paulo, nadzimanga naye manja ake ndi mapazi ake ndipo anati, “Mzimu Woyera akuti, ‘Mwini lambayu, Ayuda adzamumanga chomwechi ku Yerusalemu, ndipo adzamupereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina.’ ”
12 Titamva zimenezi, ife pamodzi ndi anthu kumeneko tinamudandaulira Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukulira ndi kunditayitsa mtima? Ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha ayi, komanso kufa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.” 14 Titalephera kumuletsa tinamuleka ndipo tinati, “Chifuniro cha Ambuye chichitike.”
15 Pambuyo pake, ife tinakonzeka ndi kunyamuka kumapita ku Yerusalemu. 16 Ena mwa ophunzira a ku Kaisareya anatiperekeza mpaka kukatifikitsa ku nyumba ya Mnasoni, kumene tinakonza kuti tizikhalako. Iye anali wa ku Kupro ndiponso mmodzi wa ophunzira oyambirira.
Paulo Afika ku Yerusalemu
17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mwachimwemwe. 18 Mmawa mwake Paulo pamodzi ndi ife tonse tinapita kwa Yakobo, ndipo akulu onse a mpingo anali komweko. 19 Paulo anawalonjera ndi kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.
20 Atamva zimenezi, iwo anayamika Mulungu. Kenaka anawuza Paulo kuti, “Mʼbale, ukuona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene anakhulupirira, ndipo ndi okhulupirika potsatira Malamulo a Mose. 21 Iwo anawuzidwa kuti iwe umaphunzitsa Ayuda onse amene akukhala pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Mose, kuti asamachite mdulidwe kapena kutsatira miyambo. 22 Nanga pamenepa ife titani? Iwo adzamva ndithu kuti iwe wabwera, 23 tsono iwe chita zimene ife tikuwuze. Tili nawo amuna anayi pano amene anachita lumbiro kwa Mulungu. 24 Muwatenge anthu amenewa, ndipo muchite nawo mwambo wowayeretsa ndipo muwalipirire zoti apereke kuti amete tsitsi lawo. Kotero aliyense adzadziwa kuti palibe choonadi pa zimene anamva za inu, koma kuti inu mwini mumakhala moyo womvera Malamulo. 25 Koma kunena za anthu a mitundu ina amene asandulika okhulupirira, ife tinawalembera zimene tinavomerezana zakuti asadye chakudya choperekedwa ku mafano, asadye magazi, asadye nyama yopotola ndiponso asachite zadama.”
26 Mmawa mwake Paulo anatenga amuna aja ndipo anachita mwambo wodziyeretsa. Kenaka anapita ku Nyumba ya Mulungu nakadziwitsa ansembe za tsiku limene adzatsiriza nthawi ya kudziyeretsa ndi kuperekera nsembe aliyense wa iwo.
Agwira Paulo
27 Ali pafupi kutsiriza masiku asanu ndi awiriwo, Ayuda ena ochokera ku Asiya anaona Paulo mʼNyumba ya Mulungu. Iwo anawutsa gulu lonse la anthu ndipo anamugwira Paulo, 28 akufuwula kuti, “Inu Aisraeli, tithandizeni! Ndi uyu munthu uja amaphunzitsa anthu onse ponseponse kuti azinyoza mtundu wathu ndiponso Malamulo athu ndi malo ano. Kuwonjezera pamenepo, walowetsa Agriki mʼbwalo la Nyumba ino ndipo wadetsa malo opatulika.” 29 Iwo ananena izi chifukwa anali ataona Trofimo wa ku Efeso ali ndi Paulo mu mzindamo ndipo iwo ankaganiza kuti Paulo anamulowetsa mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu.
30 Mzinda wonse unasokonezeka, ndipo anthu anabwera akuthamanga kuchokera kumbali zonse. Anamugwira Paulo, namukokera kunja kwa Nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo anatseka zipata. 31 Pamene anthuwo ankafuna kupha Paulo, nkhaniyi inamveka kwa mkulu wa magulu a asilikali a Aroma kuti mzinda wonse wa Yerusalemu wasokonezeka. 32 Nthawi yomweyo iye anatenga asilikali ndi atsogoleri a magulu a asilikali ndi kuthamangira kumene kunali anthuwo. Anthuwo ataona mkuluyo ndi asilikali ake analeka kumenya Paulo.
33 Mkulu wa asilikaliyo anabwera nagwira Paulo, ndipo analamula kuti amangidwe ndi maunyolo awiri. Kenaka iye anafunsa kuti ndi ndani ndipo wachita chiyani. 34 Ena mʼgulumo anafuwula chinthu china ndi enanso chinanso. Tsono popeza mkulu wa asilikaliyo sanathe kudziwa choonadi chenicheni chifukwa cha phokoso, analamula kuti Paulo atengedwe kupita ku malo a asilikali. 35 Paulo atafika pa makwerero olowera ku malo a asilikaliwo, ananyamulidwa ndi asilikali chifukwa cha ukali wa anthuwo. 36 Gulu la anthu limene linamutsatira linapitiriza kufuwula kuti, “Ameneyo aphedwe basi!”
Paulo Ayankhula
37 Asilikali ali pafupi kulowa naye ku malo awo, iye anapempha mkulu wa asilikaliyo kuti, “Kodi mungandilole ndiyankhulepo?”
Mkulu wa asilikaliyo anafunsa kuti, “Kodi umayankhula Chigriki? 38 Kodi sindiwe Mwigupto uja amene masiku apitawo unayambitsa kuwukira ndi kutsogolera anthu 4,000 owukira aja nʼkupita nawo ku chipululu?”
39 Paulo anayankha kuti, “Ine ndine Myuda, wa ku Tarisisi ku Kilikiya. Sindine nzika ya mzinda wamba. Chonde loleni ndiyankhule nawo anthuwa.”
40 Ataloledwa ndi mkulu wa asilikaliyo, Paulo anayimirira pa makwereropo nakweza dzanja lake kwa gulu la anthuwo. Onse atakhala chete, iye anayankhula nawo mʼChihebri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.