M’Cheyne Bible Reading Plan
Kubadwa kwa Isake
21 Yehova anakomera mtima Sara monga ananenera, ndipo Yehovayo anachita monga momwe analonjezera. 2 Sara anakhala ndi pathupi ndipo anamuberekera Abrahamu mwana wamwamuna mu ukalamba wake, pa nyengo imene Mulungu anamulonjeza. 3 Abrahamu anapereka dzina loti Isake kwa mwana wamwamuna amene Sara anamuberekera. 4 Isake atakwanitsa masiku asanu ndi atatu, Abrahamu anamuchita mdulidwe monga Mulungu anamulamulira. 5 Abrahamu anali ndi 100 pamene mwana wake Isake anabadwa.
6 Sara anati, “Mulungu wandibweretsera mseko, ndipo aliyense amene adzamva zimenezi adzaseka nane pamodzi.” 7 Ndipo anawonjezera kuti, “Ndani akanamuwuza Abrahamu kuti Sara nʼkudzayamwitsako ana? Chonsecho ndamubalira mwana wamwamuna kuwukalamba wake.”
Kuchotsedwa kwa Hagara ndi Ismaeli
8 Mwana uja anakula mpaka kumuletsa kuyamwa. Tsiku lomuletsa Isake kuyamwa, Abrahamu anakonza phwando lalikulu. 9 Koma Sara anaona kuti mwana wamwamuna amene Hagara Mwigupto anamuberekera Abrahamu amamuseka, 10 ndipo anati kwa Abrahamu, “Muchotse mdzakazi ndi mwana wake wamwamunayu, pakuti mwana wa kapolo sadzagawana chuma ndi mwana wanga Isake.”
11 Nkhaniyi inamumvetsa chisoni kwambiri Abrahamu chifukwa imakhudza mwana wake. 12 Koma Mulungu anamuwuza Abrahamu kuti, “Usamve chisoni motero ndi mnyamatayu ndi mdzakazi wakoyu. Mvetsera chilichonse chomwe Sara akukuwuza, chifukwa zidzukulu zako zidzachokera mwa Isake. 13 Mwana wa mdzakazi wakoyu ndidzamusandutsa mtundu wa anthu chifukwa ndi mwana wako.”
14 Mmamawa wake, Abrahamu anatenga chakudya ndi botolo la madzi nazipereka kwa Hagara. Anasenzetsa Hagara nawaperekeza pangʼono ndi mnyamatayo. Hagara ananyamuka nayendayenda mʼchipululu cha Beeriseba.
15 Madzi atatha mʼbotolo muja, anamuyika mnyamatayo pansi pa zitsamba. 16 Kenaka Hagara anachoka nakakhala pansi cha pakatalipo, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi, popeza mʼmaganizo mwake amati, “Sindingaonerere mwanayu akufa.” Ndipo anakhala pansi cha poteropo nʼkumalira.
17 Mulungu anamva mnyamatayo akulira ndipo mngelo wa Mulungu anayankhula kwa Hagara kuchokera kumwamba nati, “Chavuta nʼchiyani Hagara? Usachite mantha; Mulungu wamva kulira kwa mnyamatayo pamene wagonapo. 18 Munyamule mnyamatayo ndipo umugwire dzanja pakuti ndidzamupanga kukhala mtundu waukulu.”
19 Kenaka Mulungu anatsekula maso a Hagara ndipo anaona chitsime cha madzi. Choncho anapita nadzaza botolo lija ndi madzi ndi kumupatsa mnyamatayo kuti amwe.
20 Mulungu anali ndi mnyamatayo pamene ankakula. Anakhala ku chipululu nakhala katswiri wolasa uta. 21 Akukhala ku chipululu cha Parani, mayi ake anamupezera mkazi wochokera ku Igupto.
Pangano la ku Beeriseba
22 Pa nthawiyo, Abimeleki ndi Fikolo wamkulu wankhondo wake anati kwa Abrahamu, “Mulungu ali nawe pa chilichonse umachita. 23 Tsopano undilumbirire ine pano pamaso pa Mulungu kuti sudzachita mwa chinyengo ndi ine kapena ana anga kapena zidzukulu zanga. Undionetse ine pamodzi ndi dziko limene ukukhalamo ngati mlendo, kukoma mtima kokhala ngati kumene ndinakuonetsa ine.”
24 Abrahamu anati, “Ine ndikulumbira.”
25 Kenaka Abrahamu anadandaula kwa Abimeleki pa za chitsime chimene antchito a Abimeleki analanda. 26 Koma Abimeleki anati, “Ine sindikudziwa amene anachita zimenezi. Iwe sunandiwuze, ndipo ndazimva lero zimenezi.”
27 Choncho Abrahamu anabweretsa nkhosa ndi ngʼombe nazipereka kwa Abimeleki, ndipo anthu awiriwo anachita pangano. 28 Abrahamu anapatulako ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri kuchoka pagulu la nkhosa zina, 29 ndipo Abimeleki anafunsa Abrahamu, “Kodi tanthauzo lake la ana ankhosa aakazi asanu ndi awiri amene wawapatula pawokhawa nʼchiyani?”
30 Iye anayankha kuti, “Landirani ana ankhosa aakazi kuchokera mʼdzanja langa ngati umboni kuti ndinakumba chitsime ichi.”
31 Kotero malo amenewo anatchedwa Beeriseba, chifukwa anthu awiriwo analumbirirapo malumbiro.
32 Atatha kuchita pangano pa Beeriseba, Abimeleki ndi Fikolo mkulu wankhondo wake anabwerera ku dziko la Afilisti. 33 Abrahamu anadzala mtengo wa bwemba ku Beeriseba, ndipo anapemphera pamenepo mʼdzina la Yehova, Mulungu Wamuyaya. 34 Ndipo Abrahamu anakhala mʼdziko la Afilisti kwa nthawi yayitali.
Fanizo la Aganyu Mʼmunda wa Mphesa
20 “Ufumu wakumwamba uli ngati mwini munda amene anapita mmawa kukalemba anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa. 2 Anagwirizana kuwalipira dinari monga malipiro a tsiku limodzi ndipo anawatumiza mʼmunda wake wamphesa.
3 “Nthawi 9 koloko mmawa, anatulukanso naona ena atayimirira pa msika akungokhala. 4 Anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa, ndipo ndidzakulipirani malipiro oyenera.’ 5 Ndipo anapita.
“Anatulukanso nthawi ya 12 koloko masana, ndi nthawi ya 3 koloko masananso nachita chimodzimodzi. 6 Nthawi ya 5 koloko madzulo anatulukanso ndipo anapeza enanso atangoyimirira. Anawafunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukungoyimirira pano tsiku lonse osagwira ntchito?’
7 “Iwo anayankha kuti, ‘Chifukwa palibe munthu amene watilemba ganyu.’
“Iye anawawuza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito mʼmunda wanga wa mpesa.’
8 “Ndipo pofika madzulo, mwini munda wamphesa anayitana kapitawo wake nati, ‘Itana antchito ndipo uwapatse malipiro awo, kuyambira omalizira aja mpaka oyamba.’
9 “Antchito amene anawalemba ganyu pa 5 koloko masana anafika ndipo aliyense analandira dinari. 10 Ndipo atabwera kwa amene analembedwa poyamba anayembekezera kuti alandira zambiri. Koma aliyense wa iwo analandira dinari. 11 Atalandira, anayamba kuderera kwa mwini mundayo. 12 Iwo anati, ‘Anthu amene munawalemba pomalizira agwira ntchito ora limodzi, ndipo mwawafananitsa ndi ife amene tathyoka nayo ntchito ndi kutentha kwa dzuwa tsiku lonse.’
13 “Koma iye anamuyankha mmodzi wa iwo nati, ‘Bwenzi, ine sikuti sindinachite chilungamo. Kodi sunavomereze kuti ugwira ntchito ndi kulandira dinari? 14 Tenga malipiro ako pita. Ndikufuna kumupatsa munthu amene ndinamulemba pomaliza mofanana ndi mmene ndakupatsira iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi ndalama zanga? Kapena ukuyipidwa chifukwa ndine wopereka mowolowamanja?’
16 “Momwemo omalizira adzakhala oyamba ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
Yesu Anenanso za Imfa Yake
17 Tsopano pamene Yesu ankapita ku Yerusalemu, anatengera pambali ophunzira ake khumi ndi awiriwo nati kwa iwo, 18 “Tikupita ku Yerusalemu, ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Iwo adzamuweruza kuti aphedwe, 19 ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amunyoze ndi kumukwapula ndi kumupachika. Pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa!”
Pempho la Mkazi wa Zebedayo
20 Amayi a ana a Zebedayo anabwera ndi ana ake kwa Yesu, nagwada pansi namupempha Iye.
21 Yesu anawafunsa kuti, “Mukufuna chiyani?”
Amayiwo anati, “Lolani kuti ana anga awiriwa adzakhale mmodzi ku dzanja lanu lamanja ndi wina ku dzanja lanu lamazere mu ufumu wanu.”
22 Yesu anawawuza kuti, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungathe kumwera chikho chimene ndidzamwera Ine?”
Iwo anayankha nati, “Inde tingathe.”
23 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi mudzamwera chikho changa, koma kuti mudzakhale ku dzanja langa lamanja kapena lamazere si kwa Ine kupereka. Malo awa ndi a iwo amene anakonzeredweratu ndi Atate anga.”
24 Ophunzira khumi aja, anawapsera mtima abale awiriwo. 25 Yesu anawayitana onse pamodzi nati, “Mukudziwa kuti olamulira a mitundu ina ali ndi mphamvu pa iwo, ndipo akuluakulu awo amawalamulira. 26 Siziyenera kutero ndi inu. Mʼmalo mwake, aliyense amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu akhale wotumikira wanu. 27 Ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyamba akhale kapolo wanu. 28 Momwenso Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kukhala dipo la anthu ambiri.”
Yesu Achiritsa Anthu Awiri Osaona
29 Pamene Yesu ndi ophunzira ake ankachoka ku Yeriko, gulu lalikulu la anthu linawatsata. 30 Amuna awiri osaona anakhala mʼmbali mwa msewu, ndipo pamene anamva kuti Yesu akudutsa anafuwula kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
31 Gulu la anthulo linawadzudzula iwo ndi kuwawuza kuti akhale chete, koma anafuwulitsabe kuti, “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”
32 Yesu anayima ndi kuwayitana ndipo anawafunsa kuti, “Mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
33 Anamuyankha nati, “Ambuye, tikufuna tione!”
34 Yesu anamva nawo chifundo ndipo anakhudza maso awo. Nthawi yomweyo anaona namutsata Iye.
10 Amene anasindikiza chidindo anali awa:
Nehemiya, bwanamkubwa uja, mwana wa Hakaliya.
Zedekiya, 2 Seraya, Azariya, Yeremiya
3 Pasuri, Amariya, Malikiya,
4 Hatusi, Sebaniya, Maluki,
5 Harimu, Meremoti, Obadiya,
6 Danieli, Ginetoni, Baruki,
7 Mesulamu, Abiya, Miyamini
8 Maziya, Biligai ndi Semaya
Awa anali ansembe.
9 Alevi anali awa:
Yesuwa mwana wa Azaniya, Binuyi wa fuko la Henadadi, Kadimieli,
10 ndi abale awo awa: Sebaniya,
Hodiya, Kelita, Pelaya, Hanani,
11 Mika, Rehobu, Hasabiya,
12 Zakuri, Serebiya, Sebaniya,
13 Hodiya, Bani ndi Beninu.
14 Atsogoleri a anthu anali awa:
Parosi, Pahati-Mowabu, Elamu, Zatu, Bani,
15 Buni, Azigadi, Bebai,
16 Adoniya, Bigivai, Adini,
17 Ateri, Hezekiya, Azuri,
18 Hodiya, Hasumu, Bezayi
19 Harifu, Anatoti, Nebayi,
20 Magipiyasi, Mesulamu, Heziri
21 Mesezabeli, Zadoki, Yaduwa
22 Pelatiya, Hanani, Ananiya,
23 Hoseya, Hananiya, Hasubu
24 Halohesi, Piliha, Sobeki,
25 Rehumu, Hasabiya, Maaseya,
26 Ahiya, Hanani, Anani,
27 Maluki, Harimu ndi Baana.
28 Ife otsalafe, ndiye kuti ansembe, Alevi, alonda a ku Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo, ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu, onse amene anadzipatula pakati pa anthu a mitundu ina kuti atsate malamulo a Yehova, pamodzi ndi akazi athu, ana athu ndi onse amene ali ndi nzeru, 29 tikuphatikana ndi abale athu wolemekezeka, ndipo tikulonjeza molumbira kuti tidzayenda motsata malamulo a Mulungu amene anapereka kudzera mwa Mose mtumiki wa Mulungu. Tilonjeza kumvera ndi kutsata bwino mawu onse, miyambo yonse ndi malangizo onse a Yehova. Yehova atilange ngati sitidzachita zimenezi.
30 “Ife tikulonjeza kuti sitidzapereka ana athu aakazi kuti akwatiwe ndi amuna a mayiko ena kapena kutenga ana awo aakazi kuti akwatiwe ndi ana athu aamuna.
31 “Ngati anthu a mitundu ina abwera ndi zinthu za malonda, monga tirigu, kudzagulitsa pa tsiku la Sabata, sitidzawagula pa tsiku la Sabata kapena pa tsiku lina lililonse loyera. Pa chaka chilichonse cha chisanu ndi chiwiri tidzagoneka munda wosawulima ndipo tidzafafaniza ngongole zonse.
32 “Tikulonjezanso molumbira kuti chaka ndi chaka tizipereka magalamu anayi a siliva kuti zithandize ntchito ya ku Nyumba ya Mulungu wathu. 33 Ndalamayi izithandiza kulipirira buledi wa pa tebulo, chopereka cha chakudya cha nthawi zonse, zopereka zopsereza za nthawi zonse, zopereka za pa tsiku la Sabata, za pachikondwerero cha Mwezi Watsopano, za pa masiku a chikondwerero osankhika, zopereka za zinthu zopatulika, zopereka za nsembe yopepesera machimo a Aisraeli ndi ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Mulungu.
34 “Ife ansembe, Alevi ndi anthu onse, tachita maere kuti tidziwe pamene banja lathu lililonse lidzabweretsa ku nyumba ya Mulungu wathu pa nthawi yoyikika ya chaka zopereka za nkhuni zoyaka pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wathu, monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo.”
35 “Tilonjezanso kuti tidzabwera ndi zipatso zoyamba kucha za mʼminda yathu ndi zipatso zoyamba kucha za mtengo uliwonse wa zipatso chaka ndi chaka kuti tidzapereke ku Nyumba ya Mulungu wathu.”
36 “Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”
37 “Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse. 38 Wansembe, mdzukulu wa Aaroni azikhala pamodzi ndi Alevi pamene akulandira chakhumi. Ndipo Alevi azibwera ndi chakhumicho ku nyumba ya Mulungu wathu, kuzipinda zosungiramo chuma.” 39 Choncho Israeli, kuphatikiza zidzukulu za Alevi, azipititsa zopereka za tirigu, vinyo ndi mafuta ku zipinda zosungiramo katundu wopatulika, komanso kokhala ansembe amene akutumikira pamodzi ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu ndi anthu oyimba nyimbo.
“Kwambiri ife sitidzaleka kusamala Nyumba ya Mulungu.”
Paulo Apita ku Makedoniya ndi ku Grisi
20 Litatha phokoso, Paulo anayitanitsa ophunzira ndipo atawalimbikitsa anawatsanzika ndipo ananyamuka kupita ku Makedoniya. 2 Iye anayendera madera a kumeneko, nalimbitsa mtima anthu, ndipo pomaliza pake anapita ku Grisi. 3 Kumeneko anakhala miyezi itatu. Popeza kuti Ayuda anakonza zomuchita chiwembu pamene amati azinyamuka kupita ku Siriya pa sitima ya pamadzi, iye anaganiza zobwereranso kudzera ku Makedoniya. 4 Iye anapita pamodzi ndi Sopatro mwana wa Puro wa ku Bereya, Aristariko ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Derbe ndi Timoteyo, ndipo a ku Asiya anali Tukiko ndi Trofimo. 5 Anthu amenewa anatsogola ndipo anakatidikira ku Trowa. 6 Koma ife tinayenda pa sitima ya pamadzi kuchokera ku Filipi chitatha Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Patapita masiku asanu tinakumana nawo enawo ku Trowa, ndipo tinakhala kumeneko masiku asanu ndi awiri.
Paulo Aukitsa Utiko ku Trowa
7 Pa tsiku loyamba la Sabata, tinasonkhana kuti tidye mgonero. Paulo analalikira kwa anthu chifukwa anaganiza zoti achoke tsiku linalo, ndipo analalika mpaka pakati pa usiku. 8 Munali nyale zambiri mʼchipinda chammwamba mʼmene tinasonkhanamo. 9 Pa chipinda chachitatu chammwamba cha nyumbayo, pa zenera, panakhala mnyamata wina dzina lake Utiko, amene ankasinza pomwe Paulo amayankhulabe. Atagona tulo, iye anagwa pansi kuchokera pa chipinda chammwamba ndipo anamutola atafa. 10 Paulo anatsika, nadziponya pa mnyamatayo, namukumbatira. Paulo anati, “Musadandaule, ali moyo!” 11 Kenaka Paulo anakweranso, mʼchipinda muja nanyema buledi nadya. Atayankhula mpaka kucha, anachoka. 12 Anthu anatenga mnyamatayo kupita kwawo ali moyo ndipo anatonthozedwa mtima kwambiri.
Paulo Alawirana ndi Akulu Ampingo a ku Efeso
13 Ife tinatsogola kukakwera sitima ya pa madzi kupita ku Aso, kumene tinayembekeza kukatenga Paulo. Iye anakonza motero chifukwa amayenda wapansi. 14 Pamene anakumana nafe ku Aso tinamutenga ndipo tinapita ku Mitilene. 15 Mmawa mwake tinachoka kumeneko pa sitima ya pamadzi ndipo tinafika pafupi ndi Kiyo. Tsiku linalo tinawolokera ku Samo, ndipo tsiku linanso tinafika ku Mileto. 16 Paulo anali atatsimikiza kuti alambalale Efeso kuopa kutaya nthawi ku Asiya, pakuti ankafulumira kuti akafike ku Yerusalemu kuti ngati nʼkotheka kuti tsiku la Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.
17 Paulo ali ku Mileto, anatumiza mawu ku Efeso kuyitana akulu ampingo. 18 Iwo atafika, Paulo anati, “Inu mukudziwa mmene ndinakhalira nanu nthawi yonse imene ndinali nanu kuyambira tsiku loyamba limene ndinafika ku Asiya. 19 Ndinatumikira Ambuye modzichepetsa kwambiri ndiponso ndi misozi, ngakhale ndinayesedwa kwambiri ndi ziwembu za Ayuda. 20 Inu mukudziwa kuti, sindinakubisireni kanthu kalikonse kopindulitsa koma ndinakuphunzitsani poyera komanso nyumba ndi nyumba. 21 Ine ndinawuza Ayuda komanso Agriki kuti ayenera kutembenukira kwa Mulungu polapa ndikuti akhulupirire Ambuye athu Yesu.
22 “Ndipo tsopano, mokakamizidwa ndi Mzimu, ndikupita ku Yerusalemu, sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko.” 23 Chimene ndikudziwa ndi chakuti Mzimu Woyera wandichenjeza mu mzinda uliwonse kuti ndende ndi mavuto zikundidikira. 24 Koma sindilabadira konse za moyo wanga ngati kuti ndi wa mtengo wapatali kwa ine, malingana ndikatsirize ntchito yanga ndi utumiki umene Ambuye Yesu anandipatsa, ntchito yochitira umboni Uthenga Wabwino wachisomo cha Mulungu.
25 “Tsopano ndikudziwa kuti inu nonse amene ndinakuyenderani ndi kumakulalikirani ufumu wa Mulungu simudzaonanso nkhope yanga. 26 Chifukwa chake, ine ndikukuwuzani lero kuti ndilibe mlandu ndi munthu aliyense. 27 Pakuti sindinakubisireni pokulalikirani chifuniro chonse cha Mulungu. 28 Mudziyangʼanire nokha ndiponso muyangʼanire gulu lankhosa limene Mzimu Woyera anakuyikani kuti mukhale oyangʼanira ake. Khalani abusa a mpingo wa Mulungu umene Iye anawugula ndi magazi ake. 29 Ndikudziwa kuti ndikachoka ine, padzafika mimbulu yolusa pakati panu imene sidzalekerera gulu lankhosalo. 30 Ngakhale pakati pa inu nokha padzapezeka anthu oyankhula zonama ndi cholinga chofuna kukhala ndi ophunzira kuti awatsate. 31 Tsono inu, samalani! Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usana ndi usiku ndiponso ndi misozi sindinaleke kuchenjeza aliyense wa inu.
32 “Tsopano ine ndikukuperekani kwa Mulungu ndiponso kwa mawu a chisomo chake, amene ali ndi mphamvu zokulitsa inu ndi kukupatsani chuma pakati pa onse amene anayeretsedwa. 33 Ine sindinasirire siliva kapena golide kapena zovala za munthu aliyense. 34 Inu nomwe mukudziwa kuti manja angawa ananditumikira kuti tipeze zimene ine ndi anzanga tinkazifuna. 35 Pa zonse zimene ndinachita, ndinakuonetsani kuti pogwira ntchito molimbika motere tiyenera kuthandiza ofowoka, pokumbukira mawu a Ambuye Yesu akuti, ‘Kupereka kumadalitsa kuposa kulandira.’ ”
36 Atanena zimenezi, anagwada pansi pamodzi ndi ena onse, napemphera. 37 Onse analira pamene amamukumbatira ndi kupsompsona. 38 Chimene chinamvetsa chisoni kwambiri ndi mawu ake akuti sadzaonanso nkhope yake. Kenaka iwo anamuperekeza ku sitima yapamadzi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.