Beginning
Mordekai Apatsidwa Ulemu
6 Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. 2 Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero.
3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?”
Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.”
4 Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera.
5 Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.”
“Mulowetseni,” Mfumu inalamulira.
6 Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?”
Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” 7 Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: 8 Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. 9 Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ”
10 Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.”
11 Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!”
12 Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. 13 Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira.
Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” 14 Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza.
Hamani Aphedwa
7 Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. 2 Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.”
3 Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. 4 Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.”
5 Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?”
6 Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.”
Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. 7 Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake.
8 Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo.
Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?”
Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. 9 Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.”
Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” 10 Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika.
Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda
8 Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. 2 Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani.
3 Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. 4 Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake.
5 Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. 6 Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?”
7 Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. 8 Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.”
9 Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. 10 Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu.
11 Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. 12 Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. 13 Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo.
14 Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa.
15 Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. 16 Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. 17 Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo.
Chigonjetso cha Ayuda
9 Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. 2 Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. 3 Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. 4 Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe.
5 Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. 6 Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. 7 Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, 8 Porata, Adaliya, Aridata, 9 Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, 10 ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo.
11 Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. 12 Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.”
13 Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.”
14 Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. 15 Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo.
16 Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. 17 Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero.
Kukondwerera Purimu
18 Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero.
19 Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso.
20 Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: 21 Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, 22 ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka.
23 Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. 24 Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. 25 Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. 26 Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, 27 Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. 28 Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira.
29 Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. 30 Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika 31 kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. 32 Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku.
Ukulu wa Mordekai
10 Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. 2 Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? 3 Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.