Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Ezara 4-7

Atsutsa za Kumanganso Nyumba ya Yehova

Adani a Yuda ndi Benjamini anamva kuti anthu obwera ku ukapolo aja akumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”

Koma Zerubabeli, Yesuwa ndi atsogoleri ena otsala a mabanja a Aisraeli anayankha kuti, “Inu simungatithandize kumangira Nyumba Yehova, Mulungu wathu. Tokha tidzamumangira Nyumba Yehova, Mulungu wa Aisraeli, monga mfumu Koresi, mfumu ya Perisiya inatilamulira.”

Tsono anthu a mʼdzikomo anayamba kuchititsa ulesi anthu a ku Yuda, ndi kuwachititsa mantha kuti aleke ntchito yomangayo. Analemba alangizi ena kuti alepheretse cholinga chawo pa ntchitoyo pa nthawi yonse ya Koresi, mfumu ya ku Perisiya, ndiponso mpaka pamene Dariyo mfumu ya ku Perisiya ankalamulira dzikolo.

Kutsutsa Kwina pa Nthawi ya Ahasiwero ndi Aritasasita

Mfumu Ahasiwero atangoyamba kulamulira dzikolo, adani aja analemba kalata yoneneza anthu a Yuda ndi Yerusalemu.

Ndiponso mʼnthawi ya Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzawo ena analemba kalata inanso kwa Aritasasita. Kalatayo inalembedwa mʼChiaramu ndipo ankatanthauzira poyiwerenga.

Rehumu mkulu wankhondo ndi Simisai mlembi, nawonso analemba kalata yawo yoneneza anthu a ku Yerusalemu kwa mfumu Aritasasita. Anayilemba motere:

Kalata yochokera kwa Rehumu, mkulu wa gulu lankhondo, mlembi Simisai ndi anzawo awa: oweruza, nduna, akuluakulu ena, anthu a ku Peresiya, Ereki, Babuloni, Susa mʼdziko la Elamu, 10 ndi mitundu ina imene mkulu wolemekezeka, Osanipara anayisamutsa ndi kuyikhazika mʼmizinda ya Samariya ndi mʼmadera ena apatsidya la Yufurate.

11 Mawu a mʼkalata ya kwa Aritasasita anali awa:

Kwa mfumu Aritasasita:

Kuchokera kwa atumiki anu, anthu a kutsidya kwa Yufurate:

12 Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.

13 Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa. 14 Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse. 15 Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga. 16 Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.

17 Mfumu inatumiza yankho ili:

Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate.

Landirani moni.

18 Kalata imene munatumiza ija yawerengedwa bwino lomwe pamaso panga. 19 Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo. 20 Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse. 21 Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula 22 Musachedwe kuchita zimenezi. Kodi ine ndingalole bwanji kuti zowononga zotere zikule ndi kupweteka ine mfumu?

23 Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.

24 Motero ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu inayimitsidwa mpaka chaka cha chiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya ku Perisiya.

Kalata ya Tatenai Yopita kwa Dariyo

Nthawi imeneyo aneneri Hagai ndi Zekariya, mwana wa Ido, ankayankhula kwa Ayuda okhala mʼdziko la Yuda ndi mu Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Israeli, amene anali nawo. Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza.

Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?” Anawafunsanso kuti, “Kodi anthu amene akumanga nyumbayi mayina awo ndani?” Koma Mulungu wawo amayangʼanira atsogoleri Ayuda, motero kuti anthu aja anaganiza kuti asawaletse kumanga Nyumbayo mpaka atalembera mfumu Dariyo kalata ndi kulandira yankho lake.

Iyi ndi kalata imene Tatenai bwanamkubwa wa dera la patsidya pa Yufurate, ndiponso Setari-Bozenai ndi anzake, akazembe amene anali mʼchigawo cha patsidya pa Yufurate, anatumiza kwa mfumu Dariyo Analemba kalatayo motere:

Kwa mfumu Dariyo:

Mukhale ndi mtendere wonse.

Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo.

Ndipo tinawafunsa atsogoleriwo kuti, “Anakulolezani kuti mumangenso Nyumbayi ndi kutsiriza makoma ake ndani?” 10 Tinawafunsanso mayina a atsogoleri awo, kuti tikalemba mayina atsogoleriwo tidzakudziwitseni kuti muwadziwe.

11 Yankho limene anatipatsa ndi ili:

“Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo. 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.

13 “Komabe chaka choyamba cha Koresi, mfumu ya ku Babuloni, mfumu Koresiyo anapereka lamulo lakuti Nyumba ya Mulunguyi imangidwenso. 14 Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa. 15 Tsono mfumuyo inamuwuza kuti, ‘Tenga ziwiyazi ukaziyike mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Ndipo Nyumba ya Mulunguyo ikamangidwenso pa maziko ake akale.’

16 “Choncho Sesibazarayo anabwera ndi kumanga maziko a Nyumba ya Mulunguyo mu Yerusalemu. Kuyambira tsiku limenelo mpaka lero yakhala ikumangidwa ndipo sinathebe.”

17 Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.

Lamulo la Mfumu Dariyo

Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale. Ndipo ku Ekibatana, likulu la dera la Mediya, kunapezeka mpukutu mmene munalembedwa kuti,

Chikumbutso:

Mʼchaka choyamba cha ufumu wa Koresi, mfumuyo inapereka lamulo lokhudza Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu.

Analamula kuti Nyumba ya Mulungu imangidwenso kukhala malo woperekerako nsembe. Maziko ake amangidwe kolimba pa malo pomwe paja pali maziko ake akale ndipo mulitali mwake mukhale mamita 27, mulifupi mwake mukhale mamita 27. Mumange mizere itatu ya miyala yayikulu ndi mzere umodzi wa matabwa, ndalama zake zolipirira ntchitoyo zichokere mʼthumba la ufumu. Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.

Tsopano Tatenai, bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate ndiponso Setari-Bozenai pamodzi ndi anzanu muchokeko kumeneko. Ntchito yomanga Nyumba ya Mulunguyi muyileke. Mulekeni bwanamkubwa wa Ayuda ndiponso akuluakulu a Ayuda kuti amangenso Nyumba ya Mulunguyo pamalo pake.

Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo:

Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate. Ndipo zonse zofunikira monga, ana angʼombe, nkhosa zazimuna, ana ankhosa aamuna zoperekera nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba, ndi tirigu, mchere, vinyo ndi mafuta monga mmene ansembe a ku Yerusalemu angafunire, muziwapatsa zimenezo tsiku ndi tsiku ndipo musamalephere kutero. 10 Zikatero ndiye kuti azipereka nsembe za fungo lokomera Mulungu wakumwamba ndi kupempherera moyo wa mfumu ndi ana ake.

11 Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala. 12 Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko.

Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.

Kutsiriza ndi Kupereka Nyumba ya Mulungu

13 Tsono potsata zomwe analamula mfumu Dariyo, Tatenai bwanamkubwa wa dera la Patsidya pa Yufurate, Setari-Bozenai ndi anzawo anatsatira mosamala kwambiri zimene mfumu Dariyo analamula. 14 Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya. 15 Anatsiriza kumanga Nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara mʼchaka chachisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa mfumu Dariyo.

16 Choncho Aisraeli, ansembe, Alevi ndi anthu ena onse amene anali atabwerako ku ukapolo, anachita chikondwerero chopereka Nyumba ya Mulungu mwachimwemwe. 17 Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli. 18 Ndipo anakhazikitsa ansembe ndi Alevi pa ntchito zawo zotumikira Mulungu mu Yerusalemu monga zinalembedwera mʼbuku la Mose.

Paska

19 Pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba, obwera ku ukapolo aja anachita chikondwerero cha Paska. 20 Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni. 21 Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli. 22 Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.

Ezara Abwera ku Yerusalemu

Zitatha izi, Aritasasita ali mfumu ya ku Perisiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu abambo ake anali Seraya mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi, mwana wa Amariya, mwana wa Azariya, mwana wa Merayoti, mwana wa Zerahiya, mwana wa Uzi, mwana wa Buki, mwana wa Abisuwa, mwana wa Finehasi, mwana wa Eliezara, mwana wa Aaroni mkulu wa ansembe uja. Ezara ameneyu anabwera kuchokera ku Babuloni. Iyeyu anali wophunzira kwambiri za malamulo a Mose, amene Yehova Mulungu wa Israeli anapereka. Mfumu inamupatsa chilichonse chimene anapempha pakuti dzanja la Yehova Mulungu wake linali pa iye. Tsono mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wa Aritasasita, Ezara pamodzi ndi Aisraeli ena, kuphatikizapo ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda, ndi anthu ogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu ananyamuka kubwerera ku Yerusalemu.

Ezara anafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu. Iye anayamba ulendo wochoka ku Babuloni pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linali pa iye. 10 Popeza Ezara anadzipereka kuwerenga ndi kusunga malamulo a Yehova, iye anafunitsitsa kuphunzitsa Aisraeli malamulo ndi malangizo a Mulungu.

Kalata ya Aritasasita Yopita kwa Ezara

11 Iyi ndi kalata imene mfumu Aritasasita anapereka kwa wansembe Ezara, mlembi wa malamulo, munthu wophunzira kwambiri zokhudza malamulo ndi malangizo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli.

12 Ndine Aritasasita, mfumu ya mafumu.

Ndikulembera iwe Ezara wansembe ndi mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba.

Malonje.

13 Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite. 14 Ine mfumu pamodzi ndi alangizi anga asanu ndi awiri tikukutumani kuti mukafufuze za dziko la Yuda ndi mzinda wa Yerusalemu kuti mukaone mmene anthu akutsatira malamulo a Mulungu wanu, amene anawapereka kwa inu. 15 Utenge siliva ndi golide zimene ine mfumu ndi alangizi anga tapereka mwa ufulu kwa Mulungu wa Israeli, amene amakhala ku Yerusalemu. 16 Mutengenso siliva yense ndi golide amene mungamupeze mʼdziko lonse la Babuloni, ngakhalenso zinthu zimene anthu pamodzi ndi ansembe adzapereka mwaufulu kuperekera ku Nyumba ya Mulungu wawo ya ku Yerusalemu. 17 Ndi ndalama zimenezi mudzaonetsetse kuti mwagula ngʼombe zazimuna, nkhosa zazimuna ndi ana ankhosa aamuna pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa. Mudzapereke zimenezi pa guwa lansembe la Nyumba ya Mulungu wanu ya ku Yerusalemu.

18 Ndalama zotsala mudzagwiritse ntchito zimene inuyo ndi abale anu zikakukomerani malingana nʼkufuna kwa Mulungu wanu. 19 Ziwiya zonse zimene akupatsani kuti mukatumikire nazo mʼNyumba ya Mulungu wanu, kaziperekeni kwa Mulungu ku Yerusalemu. 20 Ndipo chilichonse chimene chingafunike mʼNyumba ya Mulungu wanu, chimene mudzapeze mpata wopereka, ndalama zake zogulira zidzachokere mʼthumba la chuma cha mfumu.

21 Tsopano Ine, mfumu Aritasasita, ndikulamula asungichuma onse a dera la Patsidya pa Yufurate kuti, chilichonse chimene wansembe Ezara, mlembi wa malamulo a Mulungu Wakumwamba adzapempha kwa inu, mupatseni mwa msanga. 22 Ngakhale atafunika makilogalamu 3,400 asiliva, makilogalamu 10,000 a tirigu, malita 2,000 a vinyo, malita 2,000 a mafuta ndi mchere wochuluka motani, zonsezi mupereke monga zingafunikire. 23 Chimene Mulungu Wakumwamba walamula, chichitike mosamalitsa ku Nyumba ya Mulungu Wakumwamba kuopa kuti mkwiyo wa Mulungu ungayakire mfumu, dziko lake ndi ana ake. 24 Tikukudziwitsaninso kuti kudzakhala kosaloledwa kukhometsa msonkho uliwonse anthu awa: ansembe, Alevi, oyimba nyimbo, alonda kapena aliyense wogwira ntchito ku Nyumba ya Mulungu.

25 Ndipo iwe, Ezara, monga mwa nzeru za Mulungu wako zimene uli nazo, usankhe oyendetsa zinthu ndi oweruza kuti azilamulira anthu onse okhala ku dera la Patsidya pa Yufurate, onse amene amadziwa malamulo a Mulungu wako. Ndipo uphunzitse aliyense amene sawadziwa. 26 Ndipo amene sadzamvera lamulo la Mulungu wako ndi lamulo la mfumu alangidwe kolimba kapena aphedwe kapena achotsedwe mʼdzikolo, kapena katundu wake alandidwe, kapena aponyedwe mʼndende.

27 Ezara anati atamandike Yehova, Mulungu wa makolo athu, amene wayika ichi mu mtima wa mfumu kuti alemekeze Nyumba ya Yehova ya ku Yerusalemu mʼnjira imeneyi. 28 Ameneyonso waonetsa chikondi chake chosasinthika kwa ine pamaso pa mfumu, alangizi ake ndi nduna zake zamphamvu kuti andikomere mtima. Choncho ndinalimba mtima popeza Yehova, Mulungu wanga anali nane, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri ambiri a Israeli kuti apite nane pamodzi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.