Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
1 Mbiri 15-17

Bokosi la Chipangano Alibweretsa ku Yerusalemu

15 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.”

Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera. Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi:

kuchokera ku banja la Kohati,

mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120.

Kuchokera ku banja la Merari,

mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220;

kuchokera ku banja la Geresomu,

mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130;

kuchokera ku banja la Elizafani,

mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200;

kuchokera ku banja la Hebroni,

mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80;

10 kuchokera ku banja la Uzieli,

mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112.

11 Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu. 12 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera. 13 Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.” 14 Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli. 15 Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova.

16 Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga.

17 Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya; 18 ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata.

19 Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa; 20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera; 21 ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika. 22 Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi.

23 Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo. 24 Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo.

25 Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. 26 Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri. 27 Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala. 28 Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe.

29 Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.

16 Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu. Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma.

Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu.

Nyimbo Yotamanda ya Davide

Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova:

Yamikani Yehova, itanani dzina lake;
    lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu.
Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando;
    nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa.
10 Nyadirani dzina lake loyera;
    ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova.
11 Dalirani Yehova ndi mphamvu zake;
    funafunani nkhope yake nthawi zonse.
12 Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita,
    zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake,
13 inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake,
    inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.

14 Iye ndiye Yehova Mulungu wathu;
    chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi.
15 Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse,
    mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda,
16 pangano limene anachita ndi Abrahamu,
    lonjezo limene analumbira kwa Isake.
17 Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo,
    kwa Israeli monga pangano lamuyaya.
18 “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani
    monga cholowa chimene udzachilandira.”

19 Ali anthu owerengeka,
    ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo,
20 iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,
    ku ufumu wina kupita ku ufumu wina.
21 Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze;
    chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu:
22 “Musakhudze odzozedwa anga;
    musawachitire choyipa aneneri anga.”

23 Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi;
    lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.
24 Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse,
    ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse.
25 Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda;
    Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse.
26 Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake,
    koma Yehova analenga kumwamba.
27 Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake;
    mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye.
28 Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu,
29     perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake.
Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake;
    pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake.
30 Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi!
    Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe.
31 Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere;
    anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!”
32 Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;
    minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo!
33 Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba,
    idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova,
    pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

34 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino;
    chikondi chake chikhala mpaka muyaya.
35 Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu,
    mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina,
kuti tiyamike dzina lanu loyera,
    kuti tikutamandeni.”
36 Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli,
    kuyambira muyaya mpaka muyaya.

Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.”

37 Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse. 38 Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata.

39 Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni 40 kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli. 41 Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.” 42 Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata.

43 Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake.

Lonjezo la Mulungu kwa Davide

17 Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”

Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.”

Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati,

“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’ Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena. Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”

Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja; 10 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse.

“ ‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako. 11 Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 12 Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 13 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo. 14 Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’ ”

15 Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.

Pemphero la Davide

16 Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati,

“Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa? 17 Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.”

18 “Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu. 19 Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse.

20 “Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu. 21 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 22 Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.

23 “Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera, 24 kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.

25 “Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 26 Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 27 Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.