Beginning
Mikaya Anenera Motsutsa Ahabu
18 Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu. 2 Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi 3 Ahabu mfumu ya Israeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti, “Kodi mudzapita nane kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi?”
Yehosafati anayankha kuti, “Ine ndili ngati inu nomwe, ndi anthu anga ngati anthu anu. Ife tikhala nanu limodzi pa nkhondoyi.” 4 Koma Yehosafati anatinso kwa mfumu ya Israeli, “Choyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
5 Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”
Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.”
6 Koma Yehosafati anafunsanso kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene ife tingafunsireko?”
7 Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.”
Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.”
8 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa akuluakulu ake ndipo inati, “Kamutengeni Mikaya mwana wa Imula, abwere msanga.”
9 Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo. 10 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ”
11 Aneneri ena onse amanenera chimodzimodzi kuti, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo kapambaneni, pakuti Mulungu adzamupereka mʼdzanja la mfumu.”
12 Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”
13 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndidzanena zimene Mulungu wanga andiwuze.”
14 Iye atafika mfumu inamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite ku nkhondo kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”
Iye anayankha kuti, “Kathireni nkhondo ndipo kapambaneni, pakuti mzindawo udzaperekedwa mʼdzanja lanu.”
15 Mfumu inati kwa iye, “Kodi ndikuwuze kangati kuti ulumbire kuti usandiwuze chilichonse koma zoonadi mʼdzina la Yehova?”
16 Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’ ”
17 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti sandinenera zabwino koma zoyipa zokhazokha?”
18 Mikaya anapitiriza ndi kunena kuti, “Imvani tsono mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu ndi gulu lonse lakumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi lamanzere. 19 Ndipo Yehova anati, ‘Ndani amene adzamunyengerere Ahabu mfumu ya Israeli kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi ndi kukafera komweko?’
“Wina ananena zina, winanso ananena zina.” 20 Pomaliza mzimu wina unatuluka ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, “Ine ndikamunyengerera!”
Yehova anafunsa kuti, “Ukagwiritsa ntchito njira yanji?”
21 Mzimuwo unati, “Ine ndidzapita ndi kukhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse!”
Yehova anati, “ ‘Iwe ukamunyengadi iyeyo. Pita kachite zimenezo.’
22 “Choncho Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa. Yehova waneneratu kuti inu mukaona tsoka.”
23 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi ndi kumenya khofi Mikaya. Zedekiya anafunsa kuti, “Kodi mzimu wochokera kwa Yehova unadzera njira iti pamene unachoka kwa ine kupita kwa iwe?”
24 Mikaya anayankha kuti, “Udzadziwa pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
25 Pamenepo mfumu ya Israeli inalamula kuti, “Tengani Mikaya ndipo mupite naye kwa Amoni, wolamulira mzindawo ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu, 26 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyike munthu uyu mʼndende ndipo musamupatse kanthu kalikonse koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwera mwamtendere.’ ”
27 Mikaya anayankhula kuti, “Ngati inu mukabwera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo anawonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”
Ahabu Aphedwa ku Ramoti-Giliyadi
28 Choncho mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. 29 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Ine ndipita ku nkhondo modzibisa koma iwe uvale mikanjo yaufumu.” Kotero mfumu ya Israeli inadzibisa ndipo inapita ku nkhondoko.
30 Tsono mfumu ya Aramu inalamulira olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu koma mfumu ya Israeli yokha.” 31 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, iwo anaganiza kuti, “Mfumu ya Israeli ndi iyi.” Kotero anatembenuka kukamenyana naye koma Yehosafati anafuwula, ndipo Yehova anamuthandiza. Mulungu anawabweza mʼmbuyo, 32 pakuti olamulira magaleta ataona kuti sanali mfumu ya Israeli, anasiya kumuthamangitsa.
33 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndipo analasa mfumu ya Israeli pakati polumikizira malaya achitsulo. Mfumu inawuza oyendetsa galeta kuti, “Bwerera, undichotse pa nkhondo pano. Ndavulazidwa.” 34 Nkhondo inakula kwambiri tsiku lonse, ndipo mfumu ya Israeli inakhala tsonga mʼgaleta lake kuyangʼanana ndi Aaramu mpaka madzulo. Ndipo pamene dzuwa linkalowa inamwalira.
19 Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, 2 mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu. 3 Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”
Yehosafati Asankha Oweruza
4 Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 5 Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda. 6 Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. 7 Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”
8 Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu. 9 Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova. 10 Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.
11 “Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”
Yehosafati Agonjetsa Mowabu ndi Amoni
20 Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.
2 Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). 3 Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4 Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.
5 Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6 ndipo anati:
“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. 7 Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? 8 Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, 9 ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’
10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”
13 Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova.
14 Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano.
15 Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16 Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17 Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”
18 Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19 Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri.
20 Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21 Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:
“Yamikani Yehova
pakuti chikondi chake ndi chosatha.”
22 Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23 Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.
24 Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25 Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26 Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero.
27 Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28 Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga.
29 Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30 Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.
Kutha kwa Ufumu wa Yehosafati
31 Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32 Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33 Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.
34 Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
35 Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36 Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37 Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.