Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Nehemiya 1-3

Pemphero la Nehemiya

Awa ndi mawu a Nehemiya mwana wa Hakaliya:

Pa mwezi wa Kisilevi, chaka cha makumi awiri, pamene ndinali mu mzinda wa Susa, Hanani mmodzi mwa abale anga, anabwera ndi anthu ena kuchokera ku Yuda, ndipo ine ndinawafunsa za Ayuda otsala amene sanatengedwe ukapolo, ndiponso za mzinda wa Yerusalemu.

Anandiyankha kuti, “Amene sanatengedwe ukapolo aja ali pa mavuto aakulu ndipo ali ndi manyazi. Khoma la Yerusalemu ndilogamukagamuka ndipo zipata zake zinatenthedwa ndi moto.”

Nditamva zimenezi, ndinakhala pansi ndi kuyamba kulira. Ndinalira kwa masiku angapo. Ndinkasala zakudya ndi kumapemphera pamaso pa Mulungu Wakumwamba. Ndinkati:

“Inu Yehova, Mulungu wakumwamba, Mulungu wamkulu ndi woopsa. Mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa onse amene amakukondani ndi kumvera malamulo anu. Tcherani khutu lanu ndi kutsekula maso anu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune limene ndikupemphera usana ndi usiku pamaso panu kupempherera Aisraeli, atumiki anu. Ndikuvomereza machimo a Aisraeli amene tinakuchimwirani. Ndithu, ine ndi banja la makolo anga tinakuchimwirani. Ife tinakuchitirani zoyipa zambiri. Sitinamvere mawu anu, malamulo ndi malangizo anu amene munapereka kwa mtumiki wanu Mose.

“Kumbukirani mawu amene munawuza mtumiki wanu Mose akuti, ‘Ngati mukhala osakhulupirika, ndidzakubalalitsani pakati pa mitundu ina. Koma mukabwerera kwa Ine, mukamvera malamulo anga ndi kuwatsatadi, ndiye kuti ngakhale anthu anu atabalalika kutali chotani, Ine ndidzawasonkhanitsa kuchokera kumeneko ndi kubwera nawo ku malo amene ndinasankha kuti azidzayitanira dzina langa.’

10 “Iwo ndi atumiki anu ndi anthu anu, amene munawawombola ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. 11 Inu Ambuye tcherani khutu lanu kuti mumve pemphero la mtumiki wanune ndiponso pemphero la atumiki anu amene amakondwera kuchitira ulemu dzina lanu. Lolani kuti mtumiki wanune zinthu zindiyendere bwino lero ndi kuti mfumu indichitire chifundo.”

Nthawi imeneyi nʼkuti ndili woperekera zakumwa kwa mfumu.

Aritasasita Atumiza Nehemiya ku Yerusalemu

Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake. Tsono mfumu inandifunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani nkhope yako ikuoneka yachisoni pamene iwe sukudwala? Ichi si chinthu china koma chisoni cha mu mtima.”

Ine ndinachita mantha kwambiri. Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”

Apo mfumu inandifunsa kuti, “Tsono ukufuna kundipempha chiyani?”

Ndipo ine ndinapemphera kwa Mulungu Wakumwamba. Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”

Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.

Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. Mundipatsenso kalata yokapereka kwa Asafu woyangʼanira nkhalango ya mfumu, kuti akandipatse mitengo yokapangira mitanda ya zipata za nsanja yoteteza Nyumba ya Mulungu, mitanda ya khoma la mzinda ndi ya nyumba yokhalamo ine.” Mfumu indipatse zomwe ndinapempha popeza Yehova wokoma mtima anali nane. Choncho ndinanyamuka ulendo wanga ndipo ndinafika kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Mfumu nʼkuti itatumiza akulu ankhondo ndi okwera pa akavalo kuti atsagane nane.

10 Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.

Nehemiya Ayendera Makoma a Yerusalemu

11 Ndinafika ku Yerusalemu, ndipo ndinakhala kumeneko masiku atatu. 12 Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.

13 Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto. 14 Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse. 15 Kotero usikuwo ndinapita ku chigwa, ndikuyangʼana khomalo. Pomaliza ndinabwerera ndi kukalowanso mu mzinda kudzera ku Chipata cha ku Chigwa. 16 Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi.

17 Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.” 18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza.

Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.

19 Koma Sanibalati wa ku Horoni, Tobiya wa ku Amoni ndi Gesemu Mwarabu atamva zimenezi, anatiseka ndi kutinyoza. Iwo anafunsa kuti, “Kodi muti ndi chiyani chimene mukuchitachi? Kodi mufuna kuwukira mfumu?”

20 Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”

Anthu Omanga Makoma a Yerusalemu

Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli. Anthu a ku Yeriko anamanga chigawo china pambali pake ndipo Zakuri mwana wa Imuri anamanga chigawo chinanso choyandikana nawo.

Chipata cha Nsomba chinamangidwanso ndi ana a fuko la Hasena. Iwo anayika mitanda yake ndi zitseko, zotsekera zake, ndi mipiringidzo yake. Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, anakonza chigawo choyandikana nacho. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya, mwana wa Mesezabeli anakonza chigawo china. Pambali pake, Zadoki mwana wa Baana anakonzanso chigawo china. Pambali pa iwowa anthu a ku Tekowa anakonza chigawo china. Koma wolemekezeka awo anakana kugwira ntchito imene akuluakulu awo anawapatsa.

Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Pambali pawo Melatiya Mgibeyoni ndi Yadoni Mmerenoti ndiponso anthu a ku Gibiyoni ndi a ku Mizipa anakonza chigawo chawo mpaka ku nyumba ya bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate. Pambali pawo Uzieli mwana wa Harihaya wa mʼgulu amisiri osula golide anakonzanso chigawo china. Pambali pake Hananiya mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, anakonzanso chigawo china. Iwo anakonzanso Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka. Refaya mwana wa Huri wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu anakonza chigawo china motsatana nawo. 10 Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye. 11 Malikiya mwana wa Harimu ndi Hasubu mwana wa Pahati-Mowabu anakonzanso chigawo china ndiponso Nsanja ya Ngʼanjo. 12 Salumu mwana wa Halohesi wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu, anakonzanso chigawo chotsatana nawo mothandizidwa ndi ana ake akazi.

13 Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala.

14 Chipata cha Zinyalala chinakonzedwa ndi Malikiya mwana wa Rekabu, wolamulira chigawo cha Beti-Hakeremu. Iye anachimanganso ndi kuyika zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo.

15 Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide. 16 Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo.

17 Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake. 18 Pambuyo pa iyeyu abale awo anapitiriza kukonza, ndipo mtsogoleri wawo anali Bawai mwana wa Henadadi, wolamulira theka lina la chigawo cha Keyila. 19 Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya. 20 Motsatana naye, Baruki mwana wa Zakai anakonzanso chigawo china kuchokera pa ngodya mpaka pa chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mkulu wa ansembe. 21 Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake.

22 Pambuyo pake ansembe okhala ku chidikha anakonzanso chigawo china. 23 Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo. 24 Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya. 25 Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi, 26 ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija. 27 Motsatana nawo, anthu a ku Tekowa anakonzanso chigawo china choyangʼanana ndi nsanja ija yayikulu ndi yayitali mpaka ku khoma la Ofeli.

28 Kuyambira ku Chipata cha Akavalo anakonza ndi ansembe ena ndipo aliyense amakonza khoma loyangʼanana ndi nyumba yake. 29 Motsatana nawo, Zadoki mwana wa Imeri anakonza chigawo china choyangʼanana ndi nyumba yake. Motsatana naye, Semeya mwana wa Sekaniya, mlonda wa Chipata cha Kummawa, anakonzanso khoma. 30 Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake. 31 Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya. 32 Ndipo pakati pa chipinda chapamwamba chapangodya ndi Chipata cha Nkhosa anakonza ndi amisiri a golide ndi anthu amalonda.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.