Beginning
Samueli Adzoza Sauli
9 Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. 2 Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa.
3 Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.” 4 Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe.
5 Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.”
6 Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.”
7 Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?”
8 Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” 9 (Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi).
10 Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo.
11 Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?”
12 Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri. 13 Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.”
14 Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika.
15 Koma chadzulo lake Sauli asanafike, Yehova anali atamuwuza kale Samueli za zimenezi kuti, 16 “Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.”
17 Samueli atamuona Sauli, Yehova anamuwuza kuti, “Munthu ndinakuwuza uja ndi uyu. Iyeyu adzalamulira anthu anga.”
18 Tsono Sauli anayandikira Samueli pa chipata ndipo anamufunsa, “Kodi mungandiwuze kumene kuli nyumba ya mlosi?”
19 Samueli anayankha, “Ine ndine mlosiyo. Tsogolani kupita ku phiri pakuti lero mudya ndi ine, ndipo mawa mmawa ndidzakuwuzani zonse zimene zili mu mtima mwanu. 20 Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?”
21 Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?”
22 Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wake uja ndi kulowa nawo mʼchipinda chachikulu ndipo anawakhazika kutsogolo kwa anthu oyitanidwa. Onse pamodzi analipo anthu makumi atatu. 23 Tsono Samueli anati kwa wophika, “Bwera nayo nyama imene ndinakupatsa, imene ndinakuwuza kuti uyisunge pambali.”
24 Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli.
25 Atatsika kuchoka ku phiri kuja, Samueli anamukonzera Sauli malo ogona pa denga la nyumba yake, ndipo Sauli anagona pamenepo. 26 Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu. 27 Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.”
10 Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi: 2 Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ”
3 “Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo. 4 Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo.
5 “Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera. 6 Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina. 7 Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe.
8 “Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.”
Sauli Avekedwa Ufumu
9 Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo. 10 Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo. 11 Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?”
12 Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?” 13 Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri.
14 Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?”
Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.”
15 Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.”
16 Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza.
17 Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa. 18 Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’ 19 Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.”
20 Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa. 21 Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze. 22 Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?”
Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.”
23 Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa. 24 Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.”
Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
25 Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo.
26 Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima. 27 Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko.
Sauli Apulumutsa Mzinda wa Yabesi
11 Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.”
2 Koma Nahasi Mwamoni uja anayankha kuti, “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditakolowola diso lakumanja la aliyense wa inu kuti ndichititse manyazi Aisraeli onse.”
3 Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.”
4 Amithenga aja atafika kwawo kwa Sauli ku Gibeya ndi kufotokoza nkhaniyi kwa anthu onse, iwo analira motaya mtima. 5 Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena.
6 Sauli atamva mawu awo, Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwa mphamvu ndipo anakwiya kwambiri. 7 Tsono anatenga ngʼombe ziwiri za ntchito, nazidula nthulinthuli. Ndipo anatumiza amithenga ndi nthulizo dziko lonse la Israeli ndi mawu akuti, “Umo ndi mmene adzachite ndi ngʼombe ya aliyense amene satsata Sauli ndi Samueli.” Ndipo anthu anachita mantha aakulu motero kuti onse ananyamuka ndi mtima umodzi. 8 Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.
9 Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri. 10 Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”
11 Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake.
Sauli Avomerezedwa kukhala mfumu
12 Kenaka anthu anafunsa Samueli kuti, “Kodi ndani aja ankanena kuti, ‘Kodi Sauli nʼkutilamulira ife?’ Bwera nawoni kuno kuti tidzawaphe.”
13 Koma Sauli anati, “Palibe amene ati aphedwe lero, pakuti lero lino Yehova wagwira ntchito yopulumutsa Israeli.”
14 Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” 15 Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu.
Samueli Atsanzika Anthu
12 Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. 2 Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero. 3 Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”
4 Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.”
5 Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.”
Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.”
6 Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto. 7 Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu.
8 “Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano.
9 “Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu. 10 Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ 11 Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere.
12 “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. 13 Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu. 14 Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. 15 Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe.
16 “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! 17 Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.”
18 Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli.
19 Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.”
20 Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. 21 Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe. 22 Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake. 23 Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo. 24 Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani. 25 Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.