Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yoswa 12-15

Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa

12 Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa:

Sihoni mfumu ya Aamori,

amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga.

Ogi mfumu ya mzinda wa Basani,

amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni.

Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo.

Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa:

mfumu ya Yerikoimodzi
mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteliimodzi
10 mfumu ya Yerusalemuimodzi
mfumu ya Hebroniimodzi
11 mfumu ya Yarimutiimodzi
mfumu ya Lakisiimodzi
12 mfumu ya Egiloniimodzi
mfumu ya Gezeriimodzi
13 mfumu ya Debriimodzi
mfumu ya Gederiimodzi
14 mfumu ya Horimaimodzi
mfumu ya Aradiimodzi
15 mfumu ya Libinaimodzi
mfumu ya Adulamuimodzi
16 mfumu ya Makedaimodzi
mfumu ya Beteliimodzi
17 mfumu ya Tapuwaimodzi
mfumu ya Heferiimodzi
18 mfumu ya Afekiimodzi
mfumu ya Lasaroniimodzi
19 mfumu ya Madoniimodzi
mfumu ya Hazoriimodzi
20 mfumu ya Simuroni Meroniimodzi
mfumu ya Akisafuimodzi
21 mfumu ya Taanakiimodzi
mfumu ya Megidoimodzi
22 mfumu ya Kadesiimodzi
mfumu ya Yokineamu ku Karimeliimodzi
23 mfumu ya Dori ku Nafoti Doriimodzi
mfumu ya Goyini ku Giligalaimodzi
24 mfumu ya Tirizaimodzi
mafumu onse pamodzi analipo 31.

Mayiko Otsala Oyenera Kulandidwa

13 Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu.

“Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto. Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori. Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati.

“Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira. Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.”

Kugawidwa kwa Dziko la Kummawa kwa Yorodani

Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani.

Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni. 10 Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni. 11 Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka. 12 Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali. 13 Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero.

14 Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera.

15 Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni.

16 Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba. 17 Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni, 18 Yahaza, Kedemoti, Mefaati. 19 Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa, 20 Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti. 21 Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni. 22 Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga. 23 Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo.

24 Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili:

25 Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba; 26 ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri. 27 Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto. 28 Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi.

29 Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo.

30 Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko. 31 Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo.

32 Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani. 33 Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo.

Kugawa kwa Dziko la Kumadzulo kwa Yorodani

14 Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli. Madera anagawidwa mwa maere kwa mafuko asanu ndi anayi ndi theka, monga momwe Yehova analamulira kudzera mwa Mose. Mose anapereka kwa mafuko awiri ndi theka dziko la kummawa kwa Yorodani, koma fuko la Levi lokha silinagawiridwe malo. Tsono fuko la Yosefe analigawa pawiri, Manase ndi Efereimu. Mose sanawagawire malo mabanja a fuko la Levi, koma iwo anangolandira mizinda imene ankakhalamo pamodzi ndi malo amene ankawetako nkhosa ndi ngʼombe zawo. Choncho Aisraeli anagawana dzikolo, monga momwe Yehova analamulira Mose.

Apereka Hebroni kwa Kalebe

Tsono anthu a fuko la Yuda anabwera kwa Yoswa ku Giligala, ndipo Kalebe mwana wa Yefune Mkeni anati kwa iye, “Inu mukudziwa zimene Yehova ananena kwa Mose munthu wa Mulungu za inu ndi ine ku Kadesi Barinea. Nthawi imene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi Barinea kudzayendera dzikoli ndinali ndi zaka makumi anayi. Ndipo nditabwerako ndinamuwuza zoona zokhazokha monga momwe ndinaonera. Koma abale anga amene ndinapita nawo anachititsa anthu mantha. Komabe ine ndinamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. Kotero tsiku limenelo Mose anandilonjeza kuti, ‘Dziko limene unayendamo lidzakhala lako ndiponso la ana ako kwamuyaya chifukwa unamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’

10 “Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85. 11 Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse. 12 Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.”

13 Ndipo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndi kumupatsa Hebroni kukhala dziko lake. 14 Choncho dera la Hebroni lakhala lili la Kalebe mwana wa Yefune Mkeni mpaka lero chifukwa anamvera Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wonse. 15 (Hebroni ankatchedwa Kiriati Ariba chifukwa cha Ariba amene anali munthu wamphamvu kwambiri pakati pa Aanaki).

Ndipo kenaka mʼdziko monse munakhala mtendere.

Dziko Limene Yuda Analandira

15 Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni.

Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere, kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika. Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera.

Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere.

Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo, napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani. Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli. Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu. Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu). 10 Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna. 11 Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja.

12 Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu.

Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda.

13 Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki). 14 Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. 15 Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 16 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 17 Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake.

18 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.”

19 Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi.

20 Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili:

21 Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali:

Kabizeeli, Ederi, Yaguri 22 Kina, Dimona, Adada 23 Kedesi, Hazori, Itinani 24 Zifi, Telemu, Bealoti, 25 Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori) 26 Amamu, Sema, Molada 27 Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti 28 Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya, 29 Baalahi, Iyimu, Ezemu 30 Elitoladi, Kesili, Horima 31 Zikilagi, Madimena, Sanisana, 32 Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

33 Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi:

Esitaoli, Zora, Asina 34 Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu, 35 Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka, 36 Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

37 Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi, 38 Dileani, Mizipa, Yokiteeli, 39 Lakisi, Bozikati, Egiloni, 40 Kaboni, Lahimasi, Kitilisi, 41 Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira.

42 Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani, 43 Ifita, Asina, Nezibu, 44 Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.

45 Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake; 46 komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu. 47 Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.

48 Mizinda ya kumapiri inali:

Samiri, Yatiri, Soko, 49 Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri) 50 Anabu, Esitemo, Animu, 51 Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.

52 Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani, 53 Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki 54 Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake.

55 Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta 56 Yezireeli, Yokideamu, Zanowa, 57 Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake.

58 Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori, 59 Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake

60 Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake.

61 Mizinda ya ku chipululu inali iyi:

Beti-Araba, Midini, Sekaka, 62 Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake.

63 Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.