Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Oweruza 10-12

Tola

10 Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu. Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri.

Yairo

Atafa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi, amene anatsogolera Israeli kwa zaka 22. Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi. Atamwalira Yairi anayikidwa mʼmanda ku Kamoni.

Yefita

Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova. Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni. Iwowa anawagonjetseratu Aisraeli mʼchaka chimenechi, ndipo kwa zaka 18 anakhala akusautsa Aisraeli onse amene anali pa tsidya la Yorodani, mʼdziko la Aamori ku Giliyadi. Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri. 10 Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.”

11 Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti? 12 Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa? 13 Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso. 14 Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.”

15 Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.” 16 Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira.

17 Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa. 18 Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”

11 Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wa mphamvu. Iyeyu amayi ake anali mkazi wachiwerewere, ndipo abambo ake anali Giliyadi. Mkazi wake wa Giliyadi anabereka naye ana aamuna. Tsono ana amenewa atakula anapirikitsa Yefita ndi kumuwuza kuti, “Sudzalandirako cholowa mʼnyumba ya abambo athu chifukwa ndiwe mwana wa mkazi wina.” Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu.

Patapita nthawi Aamoni anadzachita nkhondo ndi Israeli. Tsono pamene Aamoni ankathira nkhondo Aisraeli, akuluakulu a ku Giliyadi anapita kukamutenga Yefita ku dziko la Tobu. Iwo anati kwa iye, “Bwera ukhale mkulu wathu wankhondo kuti timenyane ndi Amoni.”

Yefita anawawuza Agiliyadi kuti, “Kodi inu suja munkadana nane ndi kundithamangitsa ku nyumba ya abambo anga? Nʼchifukwa chiyani lero mwabwera kwa ine pamene muli pa mavuto?”

Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.”

Yefita anawayankha akuluakulu a ku Giliyadi kuti, “Ngati mundibwezeranso kwathu kuti ndikachite nkhondo ndi Aamoni ndipo Yehova nʼkukandithandiza kuwagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani?”

10 Akuluakulu a ku Giliyadi anamuyankha kuti, “Yehova akhale mboni pakati pa inu ndi ife, ngati sitidzachita monga mwa mawu anu.” 11 Choncho Yefita anapita nawo akuluakulu a ku Giliyadi aja, ndipo anthu a kumeneko anamusandutsa kukhala wowalamulira ndi mkulu wankhondo. Tsono Yefita anabwerezanso mawu omwewa pamaso pa Yehova ku Mizipa.

12 Kenaka Yefita anatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni ndi funso lakuti, “Kodi ife takuchimwirani chiyani kuti muzichita nkhondo ndi dziko langa?”

13 Ndipo mfumu ya Aamoni inayankha amithenga a Yefita aja kuti, “Pamene Israeli amatuluka kuchokera mu Igupto, analanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yorodani. Tsopano mundibwezere dziko langa mwamtendere.”

14 Yefita anatumizanso amithenga akewo kwa mfumu ya Aamoni 15 kukanena kuti,

Yefita akuti, “Israeli sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la Aamoni. 16 Koma pamene Aisraeli ankachoka ku Igupto anadzera njira ya ku chipululu mpaka ku Nyanja Yofiira nakafika ku Kadesi. 17 Kenaka Israeli anatumiza amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu,’ Koma mfumu ya ku Edomu sinamvere zimenezo. Aisraeli anatumizanso amithenga kwa mfumu ya ku Mowabu, ndipo iyo inakananso. Choncho Israeli anakhala ku Kadesi.

18 “Pambuyo pake, Aisraeli ananyamuka ulendo kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo anafika ku mmawa kwa dziko la Mowabu ndi kumanga zinthando zawo ku mbali ina ya mtsinje wa Arinoni. Iwo sanalowe mʼdziko la Mowabu, chifukwa mtsinje wa Arinoni ndiwo unali malire a dziko la Mowabu.

19 “Pambuyo pake Israeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni ndipo anati kwa iye, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu popita kwathu.’ 20 Koma Sihoni sanalole Israeli kuti adzere mʼdziko mwake. Mʼmalo mwake Sihoni anasonkhanitsa ankhondo ake onse nakamanga msasa ku Yahazi ndipo anachita nkhondo ndi Israeli.

21 “Koma Yehova Mulungu wa Israeli anamupereka Sihoni pamodzi ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Israeli, ndipo anawagonjetsa. Choncho Aisraeli analanda dziko lonse la Aamori amene amakhala mʼdzikolo. 22 Analanda dziko lonse kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki ndiponso kuchokera ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yorodani.

23 “Ndiye kuti Yehova Mulungu wa Aisraeli ndiye analanda dziko la Aamori, kuwalandirira anthu ake. Kodi inu mukufuna kutilanda dzikolo? 24 Bwanji inu osakhazikika mʼdziko limene Kemosi mulungu wanu anakupatsani, ifenso tikhazikike mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa? 25 Kodi ndinu abwino kuposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu? Kodi iye anakanganapo kapena kuchita nkhondo ndi Israeli? 26 Pamene Aisraeli ankakhala mʼdziko la Hesiboni ndi mʼmidzi yake, mʼdziko la Aroeri ndi midzi yake, komanso mʼmizinda yonse imene ili mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani inu simunalande malowo nthawi imeneyo? 27 Choncho ine sindinakuchimwireni. Koma inu mukundilakwira pomenyana nane. Yehova woweruza, ndiye aweruze lero mlandu wa pakati pa Aisraeli ndi Aamoni.”

28 Koma mfumu ya Aamori, sinasamale mawu amene Yefita anatumiza kwa iyo.

29 Tsono Mzimu wa Yehova unatsikira pa Yefita. Ndipo iye ananyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Anafika ku Mizipa mʼdziko la Giliyadi, ndipo kuchokera kumeneko anapita kukalimbana ndi Aamoni. 30 Yefita analumbira kwa Yehova kuti, “Ngati mupereka Aamoni mʼmanja mwanga, 31 aliyense amene atuluke pa khomo la nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera nditagonjetsa Aamoni adzakhala wake wa Yehova, ndipo ndidzamupereka kuti akhale nsembe yopsereza.”

32 Kenaka Yefita anawolokera kwa Aamoni kukamenya nawo nkhondo, ndipo Yehova anawaperekadi mʼmanja mwake. 33 Iye anawononga mizinda makumi awiri kuchokera ku Ariori mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti. Anapitirira mpaka ku Abeli-Keranimu. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamoni.

34 Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. 35 Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.”

36 Mwanayo anayankha kuti, “Abambo, ngati munalonjeza kwa Yehova ndi pakamwa panu, chitani zimene munalonjezera pakuti Yehova wakuthandizani kulipsira adani anu Amowabu.” 37 Anatinso kwa abambo ake, “Ndikupempheni chinthu ichi: Mundilole ndikayendeyende ku mapiri miyezi iwiri ndizikalira pamodzi ndi anzanga chifukwa ndikufa ndikanali namwali wosadziwa mwamuna.”

38 Yefita anamuyankha kuti, “Pita.” Ndipo anamulola kuti apite miyezi iwiri. Tsono anapita kumapiri ndi atsikana anzake kukalira chifukwa cha unamwali wake. 39 Miyezi iwiri itatha iye anabwerera kwa abambo ake, ndipo anachitadi zimene analonjeza.

Motero unakhala mwambo wa Aisraeli, 40 kuti atsikana a Israeli ankapita chaka chilichonse kukalira maliro a mwana wa mkazi wa Yefita, Mgiliyadi uja masiku makumi anayi pa chaka.

Yefita ndi Aefereimu

12 Gulu la nkhondo la fuko la Efereimu linayitanidwa ndipo anawolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Nʼchifukwa chiyani unawoloka kukachita nkhondo ndi Aamoni osatiyitana kuti tipite nawe? Ife tikutenthera mʼnyumba mwakomu.”

Yefita anayankha kuti, “Ine ndi anthu anga tinakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndinakuyitanani koma inu simunandipulumutse mʼmanja mwawo. Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?”

Choncho Yefita anasonkhanitsa anthu a ku Giliyadi ndi kuchita nkhondo ndi Aefereimu. Ndipo Agiliyadi anagonjetsa Aefereimu chifukwa Aefereimuwo amati, “Inu a Giliyadi ndinu othawa kuchokera ku Efereimu ndi pakati pa Amanase.” Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi” Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’ ” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000.

Yefita anatsogolera Israeli zaka zisanu ndi chimodzi. Kenaka Yefita wa ku Giliyadi anamwalira, ndipo anayikidwa mu mzinda wake ku Giliyadi.

Ibizani, Eloni ndi Abidoni

Atamwalira Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu anatsogolera Israeli. Iye anali ndi ana aamuna makumi atatu ndi ana aakazi makumi atatu. Anakwatitsa ana ake akaziwo kwa anthu a fuko lina, ndipo ana ake aamuna aja anawabweretsera atsikana makumi atatu kuti awakwatire amenenso anali a fuko lina. Ibizani anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi ziwiri. 10 Kenaka Ibizani anamwalira, ndipo anayikidwa mu Betelehemu.

11 Iye atamwalira, Eloni wa fuko la Zebuloni anakhala mtsogoleri wa Aisraeli, ndipo anatsogolera Aisraeli kwa zaka khumi. 12 Kenaka Eloni anamwalira ndipo anayikidwa ku Ayaloni mʼdziko la Zebuloni.

13 Iye atamwalira, Abidoni mwana wa Hilelo wochokera ku Piratoni, anatsogolera Israeli. 14 Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu. 15 Ndipo Abidoni mwana wa Hilelo Mpiratoni uja anamwalira, nayikidwa ku Piratoni, mʼdziko la Efereimu, dziko lamapiri la Aamaleki.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.