Beginning
32 Mverani, inu mayiko a mmwamba ndipo ine ndidzayankhula;
imva, iwe dziko lapansi, mawu a pakamwa panga.
2 Chiphunzitso changa chigwe ngati mvula
ndipo mawu anga atsike ngati mame,
ngati mvumbi pa udzu watsopano,
ngati mvula yochuluka pa zomera zanthete.
3 Ndidzalalikira dzina la Yehova.
Aa, tamandani ukulu wa Mulungu wathu!
4 Iye ndi Thanthwe, ntchito zake ndi zangwiro,
njira zake zonse ndi zolungama.
Mulungu wokhulupirika amene salakwitsa,
Iye ndiye wolungama ndi wosalakwa.
5 Koma iwo achita mosakhulupirika pamaso pake,
iwo si ana akenso,
koma iwo ndi mʼbado wachinyengo ndi wokhotakhota.
6 Kodi mukumubwezera Yehova chotere,
inu anthu opusa ndi opanda nzeru?
Kodi Iye si Atate anu, Mlengi wanu,
amene anakupangani ndi kukuwumbani?
7 Kumbukirani masiku amakedzana;
ganizirani za mibado yakalekale.
Funsa abambo ako ndipo adzakuwuza,
akuluakulu ako, ndipo adzakufotokozera.
8 Pamene Wammwambamwamba anapereka mayiko kwa anthu a mitundu ina kukhala cholowa chawo,
pamene analekanitsa anthu onse,
anayikira malire anthu onse
molingana ndi chiwerengero cha ana a Israeli.
9 Pakuti gawo la Yehova ndi anthu ake,
Yakobo ndiye cholowa chake.
10 Anamupeza mʼchipululu,
ku malo owuma ndi kopanda kanthu.
Anamuteteza ndi kumusamalira;
anamutchinjiriza ngati mwanadiso wake,
11 ngati chiwombankhanga chimene chimasasula chisa chake
nʼkumazungulira pamwamba pa ana ake,
chimene chimatambalalitsa mapiko ake kuti chigwire anawo
ndi kuwanyamula pa mapiko ake otambalalawo.
12 Yehova yekha ndiye anamutsogolera;
popanda thandizo la mulungu wachilendo.
13 Anamuyendetsa pamwamba pa mapiri a mʼdziko
ndi kumudyetsa zipatso za mʼminda.
Anamudyetsa uchi wofula pa thanthwe,
ndiponso mafuta ochokera mʼnthaka ya miyala,
14 pamodzi ndi chambiko ndi mkaka wochokera ku ngʼombe ndi nkhosa,
ndiponso ana ankhosa onenepa ndi mbuzi,
pamodzinso ndi nkhosa zazimuna zabwino za ku Basani
ndiponso tirigu wabwino kwambiri.
Munamwa vinyo wa thovu lofiira.
15 Yesuruni ananenepa ndi kuyamba kuwukira;
atakhuta, ananenepa ndi kukula thupi.
Anasiya Mulungu amene anamulenga
ndipo anakana Thanthwe ndi Mpulumutsi wake.
16 Anamuchititsa nsanje ndi milungu yawo yachilendo
ndiponso anamukwiyitsa ndi mafano awo onyansa.
17 Anapereka nsembe kwa ziwanda zimene si Mulungu,
milungu imene sankayidziwa nʼkale lomwe,
milungu yongobwera kumene,
milungu imene makolo anu sankayiopa.
18 Inu munasiya Thanthwe limene linakulerani;
munayiwala Mulungu amene anakubalani.
19 Yehova anaona zimenezi ndipo anawakana
chifukwa ana ake aamuna ndi aakazi anamukwiyitsa.
20 Iye anati, “Ndidzawabisira nkhope yanga,
ndi kuona kuti mathero awo adzakhala otani;
pakuti ndi mʼbado wopotoka,
ana amene ndi osakhulupirika.
21 Anandichititsa kukhala wansanje pamene ankapembedza chimene si mulungu
ndi kundikwiyitsa chifukwa cha mafano awo achabechabe.
Ine ndidzawachititsa kuti achite nsanje ndi mtundu wina wopandapake;
ndidzawakwiyitsa ndi mtundu wina wachabechabe.
22 Pakuti mkwiyo wanga wayaka ngati moto,
umene umayaka mpaka ku dziko la anthu akufa.
Motowo udzanyeketsa dziko lapansi ndi zokolola zake
ndipo udzapsereza maziko a mapiri.
23 “Ndidzawawunjikira masautso
ndipo mivi yanga yonse idzathera pa iwo.
24 Ndidzawatumizira njala yoopsa,
malungo woopsa ndi nthenda zofa nazo;
ndidzawatumizira zirombo zakuthengo zowavuta,
ululu wa njoka ya mʼphiri imene imakwawa pa fumbi.
25 Mʼmisewu lupanga lidzawasandutsa kukhala wopanda ana;
mantha adzalamulira nyumba zawo.
Anyamata ndi atsikana adzafa,
ngakhalenso makanda ndi okalamba.
26 Ine ndinanena kuti ndidzawamwaza
ndi kuwafafaniza kuti anthu asawakumbukirenso,
27 koma sindinafune kuti adani anga adzandinyoze,
mwina adani anga sadzandimvetsetsa
ndipo adzanena kuti, ‘Tagonjetsa anthuwa ndife;
Yehova sanachite zonsezi.’ ”
28 Iwo ndi mtundu wopanda maganizo,
iwo alibe nzeru nʼpangʼono pomwe.
29 Ngati iwo akanakhala anzeru akanamvetsetsa izi
ndi kuzindikira kuti mathero awo adzakhala otani!
30 Kodi munthu mmodzi akanathamangitsa bwanji anthu 1,000
kapena anthu awiri kuthamangitsa anthu 10,000, kuti awagonjetse,
Thanthwe lawo likanapanda kuwagulitsa,
Yehova akanapanda kuwataya?
31 Pakuti thanthwe lawo silofanana ndi Thanthwe lathu,
ngakhale adani athu amavomereza zimenezi.
32 Mpesa wawo umachokera ku mpesa wa ku Sodomu
ndiponso ku minda ya ku Gomora.
Mphesa zawo zili ndi ululu wakupha
ndipo maphava ake ndi owawa.
33 Vinyo wawo ndi wa ululu wa njoka,
ululu woopsa wa mphiri.
34 “Kodi zimenezi sindinazisunge
ndi kuzitsekera mʼkatikati mwa chuma changa?
35 Kubwezera chilango nʼkwanga; ndidzawalanga ndine.
Pa nthawi yake phazi lawo lidzaterera;
tsiku lawo la masautso layandikira
ndipo chiwonongeko chawo chikubwera pa iwo mofulumira.”
36 Yehova adzaweruza anthu ake
ndipo adzachitira atumiki ake chifundo
pamene adzaona kuti mphamvu zawo zatha
ndipo kuti palibe amene watsala, kapolo kapena mfulu.
37 Iye adzanena kuti, “Nanga ili kuti milungu yawo,
thanthwe limene ankabisalamo,
38 milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo
ndi kumwa vinyo wa chopereka chawo cha chakumwa?”
Iwuzeni ibwere kuti idzakuthandizeni!
Ibwere kuti idzakutetezenitu!
39 “Onani tsopano kuti Ine ndine Iyeyo!
Palibe mulungu wina koma Ine ndekha.
Ine ndimapha ndiponso kupereka moyo,
ndavulaza ndipo ndidzachiritsa,
ndipo palibe angathe kupulumutsa munthu mʼmanja mwanga.
40 Ndikweza dzanja langa kumwamba ndi kulumbira kuti,
‘Pali Ine wamoyo wamuyaya,
41 pamene ndidzanola lupanga langa lonyezimira
ndipo dzanja liligwira pakubweretsa chiweruzo,
ndidzabwezera chilango adani anga
ndi kulanga onse odana nane.
42 Mivi yanga idzakhuta magazi awo
pamene lupanga langa lidzawononga mnofu:
magazi a anthu ophedwa ndi ogwidwa ukapolo,
mitu ya atsogoleri a adani.’ ”
43 Kondwerani, inu mitundu yonse ya anthu pamodzi ndi anthu ake,
pakuti Iye adzabwezera chilango anthu amene anapha atumiki ake;
adzabwezera chilango adani ake
ndipo adzakhululukira dziko lake ndi la anthu ake.
44 Mose anabwera ndi Yoswa mwana wa Nuni ndipo anayankhula mawu onsewa mʼnyimbo anthu akumva. 45 Mose atatsiriza kunena mawu onsewa pamtima kwa Aisraeli, 46 iye anawawuza kuti, “Muwasunge bwino mu mtima mwanu, mawu onse amene lero lino ndikukuwuzani kuti mudzawuze ana anu, kuti adzamvere mosamalitsa mawu onse a malamulo amenewa. 47 Mawuwa sikuti ndi mawu achabe kwa inu. Mawuwa ndi moyo wanu. Mukawamvera mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukalitenga kukhala lanu mukawoloka Yorodani.”
Mose Adzafera pa Phiri la Nebo
48 Tsiku lomwelo Yehova anawuza Mose kuti, 49 “Pita ku mapiri a ku Abarimu ukakwere pa Phiri la Nebo ku Mowabu, moyangʼanana ndi Yeriko, ndipo ukaone dziko la Kanaani, dziko limene ndikulipereka kwa Aisraeli kukhala lawo. 50 Iwe udzafera pa phiri limenelo ndipo udzapita kumene makolo ako anapita, monga mʼbale wako Aaroni anafera pa phiri la Hori ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 51 Chifukwa chake nʼchakuti inu nonse awiri simunakhulupirike kwa Ine pamaso pa Aisraeli pa madzi a Meriba ku Kadesi mʼchipululu cha Zini chifukwa simunandilemekeze kokwanira pakati pa Aisraeli. 52 Choncho udzalionera kutali dziko limene ndikupereka kwa Aisraeli. Sudzalowa mʼdziko limene ndi kulipereka kwa Aisraeli.”
Mose Adalitsa Mafuko a Aisraeli
33 Awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu, anawapereka kwa Aisraeli asanafe. 2 Iye anati:
“Yehova anabwera kuchokera ku Sinai
ndipo anatulukira kuchokera ku Seiri;
anawala kuchokera pa Phiri la Parani.
Iye anabwera ndi chiwunyinji cha angelo
kuchokera kummwera, moto woyaka uli mʼdzanja mwake.
3 Ndithu ndinu amene mumakonda anthu anu;
opatulika ake onse ali mʼmanja mwake.
Onse amagwada pansi pa mapazi anu
kuchokera kwa inu amalandira malangizo,
4 malamulo amene Mose anatipatsa,
chuma chopambana cha mtundu wa Yakobo.
5 Iye anali mfumu ya Yesuruni
pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,
pamodzi ndi mafuko a Israeli.
6 “Lolani Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,
anthu ake asachepe pa chiwerengero.”
7 Ndipo ponena za Yuda anati:
“Inu Yehova, imvani kulira kwa Yuda;
mubweretseni kwa anthu ake.
Ndi manja ake omwe adziteteze yekha.
Inu khalani thandizo lake polimbana ndi adani ake!”
8 Za fuko la Alevi anati:
“Tumimu wanu ndi Urimu ndi za
mtumiki wanu wokhulupirika.
Munamuyesa ku Masa;
munalimbana naye ku madzi a ku Meriba.
9 Iye ananena za abambo ake ndi amayi ake kuti,
‘Sindilabadira za iwo.’
Sanasamale za abale ake
kapena ana ake,
koma anayangʼanira mawu anu
ndipo anateteza pangano lanu.
10 Iye amaphunzitsa Yakobo malangizo anu
ndi malamulo anu kwa Israeli.
Amafukiza lubani pamaso panu
ndiponso amapereka nsembe zanu zonse zopsereza pa guwa lanu.
11 Inu Yehova, dalitsani luso lake lonse
ndipo mukondwere ndi ntchito za manja ake.
Menyani adani awo mʼchiwuno
kanthani amene amuwukira kuti asadzukenso.”
12 Za fuko la Benjamini anati:
“Wokondedwa wa Yehova akhale mwamtendere mwa Iye,
pakuti amamuteteza tsiku lonse,
ndipo amene Yehova amamukonda amawusa pa mapewa ake.”
13 Za fuko la Yosefe anati:
“Yehova adalitse dziko lake
ndi mame ambiri ochokera kumwamba
ndiponso madzi ambiri ochokera pansi pa nthaka;
14 ndi zinthu zambiri zimene zimacha ndi dzuwa
ndiponso ndi zokolola zabwino kwambiri zimene zimacha ndi mwezi uliwonse;
15 ndi zipatso zabwino kwambiri zochokera mʼmapiri amakedzanawa
ndiponso zokolola zochuluka zochokera ku zitunda zakalekale;
16 ndi mphatso zabwino kwambiri zochokera pa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mʼmenemo
ndiponso kukoma mtima kwa Iye amene amakhala mʼchitsamba choyaka moto.
Madalitso onsewa akhale pa mutu pa Yosefe,
wapaderadera pakati pa abale ake.
17 Ulemerero wake uli ngati ngʼombe yayimuna yoyamba kubadwa;
nyanga zake zili ngati za njati.
Ndi nyanga zakezo adzapirikitsa anthu a mitundu ina,
ngakhale iwo amene akukhala ku malekezero a dziko lapansi.
Nyanga zimenezi ndiye anthu miyandamiyanda a Efereimu;
nyanga zimenezi ndiye anthu 1,000 a Manase.”
18 Za fuko la Zebuloni anati:
“Kondwera Zebuloni, pamene ukutuluka,
ndipo iwe, Isakara, kondwera mʼmatenti ako.
19 Adzayitanira mitundu ya anthu kumapiri,
kumeneko adzaperekako nsembe zachilungamo;
kumeneko adzadyerera zinthu zochuluka zochokera ku nyanja,
chuma chobisika mu mchenga.”
20 Za fuko la Gadi anati:
“Wodala amene amakulitsa malire a Gadi!
Gadi amakhala kumeneko ngati mkango,
kukhadzula mkono kapena mutu.
21 Iye anadzisankhira dziko labwino kwambiri;
gawo la mtsogoleri anasungira iye.
Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana,
anachita chifuniro cha Yehova molungama,
ndiponso malamulo onena za Israeli.”
22 Za fuko la Dani anati:
“Dani ndi mwana wamkango,
amene akutuluka ku Basani.”
23 Za fuko la Nafutali anati:
“Nafutali wadzaza ndi kukoma mtima kwa Yehova
ndipo ndi wodzaza ndi madalitso ake;
cholowa chake chidzakhala mbali ya kummwera kwa nyanja.”
24 Za fuko la Aseri anati:
“Mwana wodalitsika kwambiri ndi Aseri;
abale ake amukomere mtima,
ndipo asambe mapazi ake mʼmafuta.
25 Zotsekera za zipata zako zidzakhala za chitsulo ndi za mkuwa,
ndi mphamvu zako zidzakhala ngati masiku a moyo wako.
26 “Palibe wina wofanana ndi Mulungu wa Yesuruni,
amene amakwera pa thambo kukuthandizani
ndiponso pa mitambo ya ulemerero wake.
27 Mulungu wamuyaya ndiye pothawirapo pathu,
ndipo pa dziko lapansi amakusungani ndi mphamvu zosatha.
Adzathamangitsa patsogolo panu mdani wanu,
adzanena kuti, ‘Muwonongeni!’
28 Motero Israeli adzakhala yekha mwamtendere;
zidzukulu za Yakobo zili pa mtendere
mʼdziko la tirigu ndi vinyo watsopano,
kumene thambo limagwetsa mame.
29 Iwe Israeli, ndiwe wodala!
Wofanana nanu ndani
anthu opulumutsidwa ndi Yehova?
Iye ndiye chishango ndi mthandizi wanu
ndi lupanga lanu la ulemerero.
Adani ako adzakugonjera,
ndipo iwe udzapondereza pansi malo awo achipembedzo.”
Mose Amwalira
34 Ndipo Mose anakwera Phiri la Nebo kuchokera ku chigwa cha Mowabu ndi kukafika pamwamba pa Phiri la Pisiga, kummawa kwa Yeriko. Kumeneko Yehova anamuonetsa dziko lonse; kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani. 2 Dera lonse la Nafutali, dziko lonse la Efereimu ndi Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kukafika kumadzulo kwa nyanja, 3 Negevi ndi chigawo chonse kuchokera ku Chigwa cha Yeriko, Mzinda wa mitengo ya migwalangwa, mpaka ku Zowari. 4 Kenaka Yehova anawuza Mose kuti, “Limenelo ndi dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo pamene ndinanena kuti, ‘Ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndakulola kuti ulione, koma sudzawoloka kuti ukalowemo.”
5 Choncho Mose mtumiki wa Yehova anamwalira kumeneko ku Mowabu, monga momwe ananenera Yehova. 6 Yehova anamuyika mʼmanda ku Mowabu, mʼchigwa choyangʼanana ndi Beti-Peori, koma mpaka lero palibe amene amadziwa pamene pali manda ake. 7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120, koma maso ake ankaonabe ndipo anali amphamvu. 8 Aisraeli analira maliro a Mose mʼchikhwawa cha Mowabu kwa masiku makumi atatu mpaka nthawi ya kulira maliro ndi kukhuza inatha.
9 Tsono Yoswa, mwana wa Nuni anadzazidwa ndi mzimu wanzeru chifukwa nʼkuti Mose atamusanjika manja. Choncho Aisraeli anamumvera ndipo anachita zomwe Yehova analamula Mose.
10 Kuyambira nthawi imeneyi, mu Israeli simunakhalepo mneneri wina aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova amayankhula naye maso ndi maso. 11 Amene anachita zizindikiro zozizwitsa zonsezi ndi zozizwitsa zimene Yehova anamutuma kuti achite mu Igupto, kwa Farao ndi kwa nduna zake zonse ndiponso mʼdziko lake lonse. 12 Ndithudi palibe mneneri wina aliyense amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa zofanana ndi zomwe Mose anachita pamaso pa Aisraeli onse.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.