Beginning
Samsoni ndi Delila
16 Tsiku lina Samsoni anapita ku Gaza. Kumeneko anaonako mkazi wachiwerewere, ndipo analowa mu nyumba yake. 2 Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.”
3 Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni.
4 Pambuyo pake, Samsoni anayamba kukonda mtsikana wina wa ku chigwa cha Soreki dzina lake Delila. 5 Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.”
6 Choncho Delila anati kwa Samsoni, “Inu tandiwuzani pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi ndi mmene anthu akhoza kukumangirani kuti akugonjetseni.”
7 Samsoni anamuyankha kuti, “Ngati wina atandimanga ndi zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndidzafowoka ndi kusanduka ngati munthu wina aliyense.”
8 Tsono atsogoleri a Afilisti aja anapita kwa mkazi uja namupatsa zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndipo mkaziyo anamanga nazo Samsoni. 9 Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike.
10 Kenaka Delila anati kwa Samsoni, “Inu mwandipusitsa ndi kundiwuza zabodza. Chonde tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.”
11 Iye anati, “Ngati aliyense atandimanga ine ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritseko ntchito, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala monga munthu wina aliyense.”
12 Choncho Delila anatenga zingwe zatsopano namumanga nazo. Kenaka anati “Amuna anga, Afilisti aja afikanso!” Nthawi iyi nʼkuti anthu omubisalira aja ali mʼchipinda chamʼkati. Koma iye anadulanso zingwe mʼmanja ake ngati akudula ulusi wa thonje.
13 Ndipo Delila anati kwa Samsoni, “Mpaka tsopano mwakhala mukundipusitsa ndi kumandiwuza zabodza. Chonde, tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.”
Iye anayankha kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziwiri za kumutu kwanga utazilukira mu cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala wofanana ndi munthu wina aliyense.” 14 Choncho iye akugona, Delila analukira njombi za ku mutu kwa Samsoni mu cholukira nsalu nachimanga molimba ndi chikhomo.
Pambuyo pake anati kwa Samsoni, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Tsono iye anadzuka ku tulo, nazula chikhomo chija ndipo njombi zinachoka mu cholukira chija.
15 Tsono mkaziyo ananenanso kwa iye kuti, “Munganene bwanji kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Aka ndi kachitatu mukundipusitsa ndipo simunandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.” 16 Tsono popeza anamupanikiza ndi mawu ake tsiku ndi tsiku ndi kumukakamiza, mtima wa Samsoni unatopa pafupi kufa.
17 Choncho anamuwuza mkaziyo zonse za mu mtima mwake nati “Lumo silinapitepo pa mutu wanga chifukwa ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu chibadwire. Ngati nditametedwa mphamvu zanga zidzandichokera, ndidzasanduka wofowoka ndipo ndidzafanana ndi munthu wina aliyense.”
18 Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo. 19 Mkazi uja anagoneka Samsoni pa miyendo yake. Kenaka anayitana munthu wina ndipo anadzameta Samsoni njombi zisanu ndi ziwiri zija kumutu kwake. Pamenepo anayamba kufowoka, ndipo mphamvu zake zinamuchokera.
20 Pambuyo pake mkaziyo anamuyitana kuti, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!”
Iye anadzuka kutuloko, naganiza kuti, “Ndituluka monga ndimachitira nthawi zonse ndi kudzimasula.” Koma sanadziwe kuti Yehova wamuchokera.
21 Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende. 22 Pambuyo pake tsitsi la pa mutu wake, monga linametedwa, linayambanso kumera.
Imfa ya Samsoni
23 Tsono atsogoleri a Afilisti anasonkhana kuti adzapereke nsembe yayikulu kwa Dagoni mulungu wawo ndi kukondwerera popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu mʼmanja mwathu.”
24 Anthuwo atamuona Samsoni, anayamba kutamanda mulungu wawo popeza ankanena kuti,
“Mulungu wathu wapereka mdani wathu
mʼmanja mwathu,
ndiye amene anawononga dziko lathu,
napha anthu athu ambirimbiri.”
25 Ali mʼkati mosangalala, anthu aja amafuwula kuti, “Mutulutseni Samsoniyo kuti adzatisangalatse.” Choncho anamutulutsadi Samsoni mʼndende, ndipo anawasangalatsadi.
Ndipo anamuyimiritsa pakati pa mizati. 26 Pambuyo pake Samsoni anawuza mnyamata amene anamugwira dzanja kuti, “Ndilole kuti ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi kuti ndiyitsamire.” 27 Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera. 28 Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri.” 29 Choncho Samsoni anagwira mizati iwiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Anayitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja ku mzati wina ndi dzanja lamanzere ku mzati winanso, 30 ndipo Samsoni anati, “Ndife nawo pamodzi!” Nthawi yomweyo anakankha ndi mphamvu zake zonse ndipo mizati inagwera atsogoleri a Afilisti ndi anthu onse anali mʼmenemo. Tsono chiwerengero cha anthu amene Samsoni anapha pa nthawi ya imfa yake chinaposa cha iwo amene anawapha akanali ndi moyo.
31 Kenaka abale ake ndi onse a pa banja la abambo ake anapita kukamutenga. Ndipo anakamuyika pakati pa Zora ndi Esitaoli mʼmanda a abambo ake, Manowa. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka makumi awiri.
Mafuno a Mika
17 Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti 2 “Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.”
Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!”
3 Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.”
4 Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake.
5 Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe. 6 Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera.
7 Ku Betelehemu mʼdziko la Yuda kunali mnyamata wina amene anali wa fuko la Levi. 8 Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika.
9 Tsono Mika anamufunsa kuti, “Mukuchokera kuti?”
Ndipo iye anayakha kuti, “Ndine Mlevi wochokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Ndikufunafuna malo okhala.”
10 Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.” 11 Choncho Mleviyo anavomera kuti azikhala naye, ndipo mnyamatayo anakhala ngati mmodzi mwa ana ake aamuna. 12 Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika. 13 Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.”
Fuko la Dani Likhala ku Laisi
18 Masiku amenewo munalibe mfumu mu Israeli.
Ndipo anthu a fuko la Dani amafunafuna malo okhalamo ngati cholowa chawo, chifukwa kufikira nthawi imeneyo anali asanalandire cholowa chawo pakati pa mafuko a Israeli. 2 Choncho fuko la Dani linatumiza kuchokera ku mabanja awo onse anthu olimba mtima asanu. Anthuwa anachokera ku Zora ndi ku Esitaoli ndipo anatumidwa kukazonda ndi kuliyendera dzikolo. Anthu amenewa ankayimira fuko lonse la Dani. Anthuwa anawawuza kuti, “Pitani mukazonde dzikolo.”
Anthuwa anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ndi kupita ku nyumba ya Mika komwe anakagona. 3 Ali ku nyumba ya Mika anazindikira mawu a mnyamata, Mlevi uja. Choncho anapita kwa iye namufunsa kuti, “Unabwera ndi ndani kuno? Nanga ukuchita chiyani ku malo ano? Komanso nʼchifukwa chiyani uli kuno?”
4 Iye anawawuza zimene Mika anamuchitira ndipo anati, “Iye anandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.”
5 Kenaka iwo anati kwa iye, “Chonde tifunsire kwa Mulungu kuti tidziwe ngati ulendo wathuwu tiyende bwino.”
6 Wansembeyo anawayankha kuti, “Pitani mu mtendere, Yehova ali ndi inu pa ulendo wanuwu.”
7 Choncho anthu asanuwo ananyamuka ndipo anafika ku Laisi, kumene anaona kuti anthu ankakhala mwabata monga anthu a ku Sidoni. Anali anthu opanda chowavuta ndiponso aphee. Tsono popeza mʼdziko mwawo analibe chosowa, iwo anali a chuma. Anaonanso kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Sidoni ndipo analibe ubale ndi wina aliyense.
8 Ozonda dziko aja atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi Esitaoli, abale awowo anawafunsa kuti, “Mwaonako zotani?”
9 “Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo popeza taliona dziko lawolo kuti ndi lachonde kwambiri. Kodi simuchitapo kanthu? Musachite mphwayi kupita mʼdzikomo ndi kukalilanda. 10 Mukalowa, mukapeza anthu amene ali osatekeseka ndi dziko lalikulu. Yehova wakupatsani dziko limeneli. Malowo ngosasowa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.”
11 Kenaka anthu 600 a fuko la Dani ananyamuka ku Zora ndi Esitaoli atanyamula zida za nkhondo. 12 Tsono anakamanga msasa ku Kiriati-Yearimu mʼdziko la Yuda. Malowa ali kumadzulo kwa Kiriati-Yearimu. Ichi ndi chifukwa chake malowo akutchedwa Mahane Dani mpaka lero. 13 Kuchokera kumeneko anapita ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anafika ku nyumba ya Mika.
14 Anthu asanu amene anakazonda dziko la Laisi anati kwa abale awo, “Kodi mukudziwa kuti imodzi mwa nyumba izi muli efodi, mafano a mʼnyumba otchedwa terafimu, fano losema ndiponso fano lokuta ndi siliva? Ndiye mudziwe chochita.” 15 Choncho anthuwa anapatuka napita ku nyumba ya Mika kumene mnyamata, Mlevi uja ankakhala ndipo anamufunsa za mmene zinthu zilili. 16 Nthawi imeneyi nʼkuti anthu 600 a fuko la Dani aja atayima pa chipata atanyamula zida za nkhondo. 17 Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata.
18 Anthuwo atalowa mʼnyumba ya Mika ndi kutenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba, ndi fano lokutidwa ndi siliva, wansembeyo anawafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani?”
19 Iwo anamuyankha kuti, “Khala chete usayankhule. Tsagana nafe ndipo udzakhala mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino kwa iwe kukhala wansembe wa fuko lonse la Israeli mʼmalo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?” 20 Wansembeyo anakondwera ndipo anatenga efodi, fano la mʼnyumba ndi fano losema natsagana nawo. 21 Choncho iwo anatembenuka nachoka, atatsogoza ana, zoweta ndi katundu wawo yense.
22 Atayenda mtunda pangʼono kuchokera pa nyumba ya Mika, anthu amene amakhala pafupi ndi nyumba ya Mika anasonkhana kulondola a fuko la Dani aja, ndipo anawapeza. 23 Atawafuwulira, a fuko la Dani aja anachewuka ndipo anafunsa Mika kuti, “Chavuta nʼchiyani kuti usonkhanitse anthu chotere?”
24 Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?”
25 Anthu a fuko la Dani aja anayankha kuti, “Usayankhuleponso kanthu chifukwa anthu awa angapse mtima nakumenya ndipo iwe ndi banja lako lonse nʼkutayapo miyoyo yanu.” 26 Choncho anthu a fuko la Dani anapitiriza ulendo wawo. Mika ataona kuti anthuwo anali amphamvu kuposa iye, anangotembenuka kubwerera kwawo.
27 Anthu a fuko la Dani aja anatenga zinthu zimene Mika anapanga pamodzi ndi wansembe uja. Iwo anakafika ku Laisi kwa anthu a phee, osatekeseka aja ndipo anawathira nkhondo, nawapha ndi kutentha mzindawo ndi moto. 28 Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu.
Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo. 29 Iwo anawutcha mzindawo Dani, kutengera dzina la kholo lawo Dani, amene anali mwana wa Israeli, ngakhale kuti mzindawo poyamba unali Laisi. 30 Anthu a fuko la Dani anayimiritsa fano losema lija. Yonatani mwana wa Geresomu, mwana wa Mose pamodzi ndi ana ake onse anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo. 31 Choncho anthu a fuko la Dani ankapembedza fano limene Mika anapanga nthawi yonse pamene nyumba ya Mulungu inali ku Silo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.