Beginning
Zoletsedwa pa Maliro
14 Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Osamadzichekacheka kapena kudzimeta pamphumi chifukwa cha abale anu amene amwalira, 2 pakuti ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu. Pakati pa anthu onse pa dziko lonse lapansi, Yehova wasankha inu kuti chikhale chuma chake chamtengo wapatali.
3 Musamadye chinthu chilichonse chonyansa. 4 Nyama zomwe mukhoza kudya ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi, 5 mbawala, gwape, mphoyo, mphalapala, ngoma, nyumbu ndi mbalale. 6 Nyama iliyonse imene ili ndi chipondero chogawikana pakati ndi yobzikula mukhoza kudya. 7 Komabe pakati pa nyama zimene zimabzikula kapena zogawikana zipondero, zimene simukuyenera kudya ndi ngamira, kalulu ndi mbira. Zimenezi ngakhale zimabzikula, zipondero zake sizogawikana, choncho ndi zodetsedwa, musadye. 8 Nkhumba simabzikula ndi yodetsedwanso ngakhale ili ndi zipondero zogawikana. Musamadye nyama yake kapena kukhudza imene yafa.
9 Mwa zamoyo zonse zimene zimakhala mʼmadzi, mukhoza kudya chilichonse chimene chili ndi minga ya pa msana ndi mamba. 10 Koma chilichonse chimene chilibe minga ya pa msana ndi mamba musadye pakuti nʼchodetsedwa.
11 Mukhoza kudya mbalame iliyonse yoyenera kudya. 12 Koma simukuyenera kudya izi: mphungu, nkhwazi, mwimba, 13 nankapakapa, akamtema, akhungubwi a mitundu yonse, ndi mtundu uliwonse wa miphamba, 14 mtundu uliwonse wa khwangwala, 15 kadzidzi wamphondo, kadzidzi wodzuma, chipudo, mtundu uliwonse wa akabawi, 16 kadzidzi wamngʼono, chiswankhono ndi mantchichi, 17 tsekwe, vuwo, dembo, 18 indwa, zimeza za mitundu yonse, nsadzu ndi mleme.
19 Zowuluka zonse za miyendo inayi ndi zodetsedwa. Musamadye zimenezi. 20 Koma chowuluka chilichonse choyenera kudya mukhoza kudya.
21 Musamadye chilichonse chimene mwachipeza chofaifa. Mukhoza kupatsa mlendo amene akukhala mu mzinda wina uliwonse wa mizinda yanu. Iyeyo akhoza kudya kapena mukhoza kugulitsa kwa wina aliyense amene sali wa mtundu wanu. Koma inu ndinu anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu.
Musamaphike mwana wambuzi mu mkaka wa mayi wake.
Za Chakhumi
22 Muzionetsetsa kuti mukupatula chakhumi pa zokolola zanu chaka chilichonse. 23 Muzidyera chakhumi cha tirigu wanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta, ndi ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene adzasankhe ngati kokhalako dzina lake, kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu. 24 Koma ngati malo amenewa ali kutali kwambiri ndipo kuti inu mwadalitsidwa ndi Yehova Mulungu wanu, ndipo simungathe kunyamula chakhumi chanu (chifukwa chakuti malo amene Yehova adzasankha kukayikako dzina lake ali kutali kwambiri), 25 ndiye musinthitse chakhumi chanucho ndi siliva, ndipo mutenge silivayo ndi kupita naye kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 26 Gwiritsani ntchito silivayo kugula chilichonse chimene muchifuna monga ngʼombe, nkhosa, vinyo kapena zakumwa zina zosasitsa, kapena china chilichonse chimene muchifuna. Ndipo inu ndi anthu a pa banja panu mudzazidyera komweko pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kukondwera. 27 Alevi okhala mʼmizinda yanu musaleke kuwathandiza popeza alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo.
28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzibweretsa zakhumi zonse pa zokolola za chaka chimenecho ndi kuzisunga mʼmidzi yanu, 29 kuti Alevi (amene alibe gawo lawo la chuma kapena cholowa chawochawo), alendo, ana ndi akazi amasiye, amene akukhala mʼmizinda yanu akhoza kubwera kudzadya ndi kukhuta. Ndipo kuti akutero Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa ntchito zanu zonse.
Chaka Chokhululukira Ngongole
15 Kumapeto kwa zaka zisanu ndi ziwiri zilizonse, muzikhululukirana ngongole. 2 Zimenezi muzichita motere: wobwereketsa aliyense adzakhululukira ngongole imene anabwereketsa kwa Mwisraeli mnzake. Iye asadzafunenso kuti Mwisraeli mnzakeyo kapena mʼbale wake amubwezere chifukwa nthawi ya Ambuye yokhululukirana ngongole yalengezedwa. 3 Mukhoza kulonjerera ngongole kwa mlendo, koma mukhululukire ngongole ina iliyonse imene mʼbale wanu ali nayo. 4 Komabe pasadzakhale wosauka pakati panu chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani kwambiri mʼdziko limene adzakupatsani kuti likhale lanu ngati cholowa chanu. 5 Adzakudalitsani pokhapokha ngati mudzamveradi Yehova Mulungu wanu posunga ndi kutsatira malamulo onse amene ndikukupatsani lero. 6 Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani monga analonjeza, ndipo inu mudzabwereketsa chuma kwa mitundu yambiri ya anthu koma inu simudzabwereka kwa aliyense. Mudzalamulira mitundu yambiri ya anthu koma inuyo palibe amene adzakulamulireni.
7 Ngati pali mʼbale wanu wina wosauka mu mzinda wanu wina uliwonse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musawumitse mitima yanu kapena kuchita kaligwiritsa kwa mʼbale wanu wosaukayo. 8 Koma mukhale ofewa manja ndipo mumukongoze mʼbale wanu momasuka pa chilichonse chimene akufuna. 9 Musayesere ndi pangʼono pomwe kusunga maganizo oyipa awa mu mtima mwanu: “Chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka chokhululukirana ngongole, chayandikira,” kuti musaonetse mtima woyipa kwa mʼbale wanu wosauka nʼkusamupatsa chilichonse. Iye angadzakunenereni inu mlandu kwa Ambuye, ndipo mudzapezeka wochimwa. 10 Mumupatse iye mowolowamanja ndipo muchite zimenezi mosasungira kanthu kumtima. Tsono chifukwa cha zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse ndi pa chilichonse chimene mukhudza. 11 Anthu osauka sadzatha mʼdziko lanu. Chomwecho ndikukulamulani kuti mukhale ofewa manja kwa abale anu ndi kwa osauka, osowa mʼdziko mwanu.
Kumasula Akapolo a Chihebri
12 Ngati mʼbale wanu wamwamuna kapena wamkazi adzigulitsa yekha kwa inu, nakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, muzimumasula mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri. 13 Ndipo pamene mumumasula, musangomulola apite chimanjamanja. 14 Mumupatse mowolowamanja zochokera pa ziweto zanu, kopunthira tirigu ndi kopsinyira vinyo. Inu mumupatse iye monga Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 15 Kumbukirani kuti munali akapolo mʼdziko la Igupto ndipo Yehova Mulungu wanu anakupulumutsani. Nʼchifukwa chake ndikukupatsani lamulo ili lero lino.
16 Koma ngati kapoloyo akuwuzani kuti, “Ine sindikufuna kumasulidwa,” chifukwa choti wakukondani inuyo pamodzi ndi banja lanu ndiponso kuti kwamukomera iyeyo kuti azikhalabe nanu, 17 pamenepo muzitenga chobowolera chachitsulo ndi kubowola khutu lake pa chitseko, ndipo mukatero adzakhala kapolo wanu moyo wake wonse. Mdzakazi wanu muzimuchitanso chimodzimodzi.
18 Musaone ngati chopweteka kumasula wantchito wanu, chifukwa ntchito imene wayigwira pa zaka zisanu ndi chimodzi zimenezi ndi yopindula kawiri pa ntchito imene akanagwira waganyu chabe. Ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita.
Ziweto Zoyamba Kubadwa
19 Mumupatulire Yehova Mulungu wanu choyamba kubadwa chachimuna chilichonse pa ngʼombe ndi nkhosa zanu. Musamazigwiritse ntchito ngʼombe zoyamba kubadwa kapena kumeta nkhosa zoyamba kubadwa. 20 Inuyo ndi banja lanu, chaka chilichonse muzizidya zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu pa malo amene Iye adzasankhe. 21 Ngati chiweto chili ndi chilema monga kulumala kapena chosaona, kapena ngati chili ndi cholakwika chachikulu chilichonse, musachipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu. 22 Muzichidya mʼmizinda yanuyanu. Onse odetsedwa monga mwa mwambo ndi oyeretsedwa omwe akhoza kuchidya monga akudya gwape kapena mbawala. 23 Koma musadye magazi ake. Muwathire pansi ngati madzi.
Paska
16 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. 2 Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. 3 Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. 4 Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.
5 Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, 6 koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. 7 Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. 8 Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.
Chikondwerero cha Masabata
9 Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili. 10 Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani 11 Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake. 12 Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa.
Chikondwerero cha Misasa
13 Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri. 14 Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu. 15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
16 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. 17 Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.
Oweruza
18 Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. 19 Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. 20 Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Kupembedza Milungu Ina
21 Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, 22 ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.