Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 126

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

126 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,
    tinali ngati amene akulota.
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;
    malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,
    “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
Yehova watichitira zinthu zazikulu,
    ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,
    monga mitsinje ya ku Negevi.
Iwo amene amafesa akulira,
    adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
Iye amene amayendayenda nalira,
    atanyamula mbewu yokafesa,
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,
    atanyamula mitolo yake.

Habakuku 2:1-5

Ndidzakhala pa malo anga aulonda,
    ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo;
ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze,
    ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.

Yankho la Yehova

Tsono Yehova anandiyankha, nati:

“Lemba masomphenyawa
    ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale
    kuti wowerenga awawerenge mosavuta.
Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;
    masomphenyawa akunena zamʼtsogolo
    ndipo sizidzalephera kuchitika.
Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;
    zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.

“Taona, mdani wadzitukumula;
    zokhumba zake sizowongoka,
    koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.
Ndithu, wasokonezeka ndi vinyo;
    ndi wodzitama ndiponso wosakhazikika.
Pakuti ngodzikonda ngati manda,
    ngosakhutitsidwa ngati imfa,
wadzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu
    ndipo wagwira ukapolo anthu a mitundu yonse.

Afilipi 3:7-11

Koma zonse zimene ndinkaziyesa zaphindu, tsopano ndikuziona kuti nʼzosapindulitsa chifukwa cha Khristu. Kuwonjeza pamenepo, ndikuziona zonse kuti nʼzopanda phindu poyerekeza ndi phindu lopambana la kudziwa Khristu Yesu Ambuye anga. Nʼchifukwa cha Yesuyo ndataya zinthu zonse ndipo ndikuziyesa zinyalala kuti ndipindule Khristu ndi kuti ndipezeke mwa Iyeyo, osati ndi chilungamo changa chobwera chifukwa chotsata malamulo, koma chimene chimabwera chifukwa chokhulupirira Khristu. Chilungamochi nʼchochokera kwa Mulungu, timachilandira mwachikhulupiriro. 10 Ine ndikufuna kudziwa Khristu, ndithu, kudziwa mphamvu zake za kuuka kwa akufa. Ndikufuna kuyanjana naye mʼmasautso ake, kufanana naye pa imfa yake 11 kuti nanenso ndidzaukitsidwe kwa akufa.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.