Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 85:1-2

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.

85 Yehova munakomera mtima dziko lanu;
    munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
Munakhululukira mphulupulu za anthu anu
    ndi kuphimba machimo awo onse.
            Sela

Masalimo 85:8-13

Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;
    Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,
    koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,
    kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;
    chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,
    ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,
    ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
13 Wolungama amapita patsogolo pake
    ndi kukonza njira za mapazi ake.

Ezekieli 36:24-28

24 “Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. 25 Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. 27 Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. 28 Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.

Marko 11:27-33

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

27 Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. 28 Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”

29 Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi. 30 Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”

31 Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 32 Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).

33 Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”

Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.