Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
Zokonzekera za Munthu ndi Zokonzekera za Mulungu
2 Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu,
kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo!
Kukacha mmawa amakachitadi
chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.
2 Amasirira minda ndi kuyilanda,
amasirira nyumba ndi kuzilanda.
Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo,
munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.
3 Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
“Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa,
tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha.
Inu simudzayendanso monyada,
pakuti idzakhala nthawi ya masautso.
4 Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe;
adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro:
‘Tawonongeka kotheratu;
dziko la anthu anga lagawidwa.
Iye wandilanda!
Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”
5 Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova
kuti agawe dziko pochita maere.
Aneneri Onyenga
6 Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere!
Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi;
ife sitidzachititsidwa manyazi.”
7 Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena:
“Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya?
Kodi Iye amachita zinthu zotere?”
“Kodi mawu ake sabweretsa zabwino
kwa amene amayenda molungama?
8 Posachedwapa anthu anga andiwukira
ngati mdani.
Mumawavula mkanjo wamtengowapatali
anthu amene amadutsa mosaopa kanthu,
monga anthu amene akubwera ku nkhondo.
9 Mumatulutsa akazi a anthu anga
mʼnyumba zawo zabwino.
Mumalanda ana awo madalitso anga
kosatha.
10 Nyamukani, chokani!
Pakuti ano si malo anu opumulirapo,
chifukwa ayipitsidwa,
awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.
11 Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti,
‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri,
woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’
Alonjeza Chipulumutso
12 “Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse;
ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli.
Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola,
ngati ziweto pa msipu wake;
malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.
13 Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo;
iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka.
Mfumu yawo idzawatsogolera,
Yehova adzakhala patsogolo pawo.”
15 “Tsono mukadzaona chinthu chonyansa chosakaza chitayima pamalo oyera chimene anayankhula mneneri Danieli, owerengayo azindikire. 16 Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire ku mapiri. 17 Yemwe ali pa denga la nyumba yake asatsike kukatulutsa chinthu chilichonse mʼnyumba. 18 Yemwe ali ku munda asapite kukatenga mkanjo wake. 19 Kudzakhala koopsa kwambiri masiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi kwa oyamwitsa! 20 Pempherani kuti kuthawa kwanu kusadzachitike nthawi yozizira kapena pa Sabata. 21 Popeza kudzakhala masautso aakulu, omwe safanana ndi ena ali onse chiyambireni cha dziko lapansi mpaka lero lino ndipo sadzafanananso ndi ena. 22 Ngati masiku amenewo sakanafupikitsidwa, palibe mmodzi akanapulumuka, koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa. 23 Pa nthawi imeneyo ngati wina adzati kwa inu, ‘Onani, Khristu ali pano!’ Kapena, ‘Uyo ali ukoyo!’ Musakhulupirire. 24 Chifukwa akhristu onama ndi aneneri onama adzaoneka ndipo adzachita zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kuti akanyenge ngakhale osankhidwawo ngati kukanakhala kotheka kutero. 25 Onani, ndakuwuzani izi nthawi isanafike.
26 “Ndiye ngati wina akuwuzani inu kuti, ‘Uyo ali ku chipululu,’ inu musapiteko; kapena akati, ‘Uyu ali kuno mʼchipinda chamʼkati,’ musakhulupirire. 27 Monga momwe mphenzi ingʼanima kuchokera kummawa kupita kumadzulo, momwemonso kudzakhala kubwera kwa Mwana wa Munthu. 28 Kulikonse kuli chinthu cha kufa, makwangwala adzasonkhanako.
29 “Akadzangotha mavuto a masiku amenewo,
“ ‘dzuwa lidzadetsedwa,
ndipo mwezi sudzawala;
nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba,
ndipo mphamvu za mmwamba zidzagwedezeka.’
30 “Pa nthawi imeneyo chizindikiro cha Mwana wa Munthu chidzaoneka mlengalenga, ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzalira. Idzaona Mwana wa Munthu akubwera ndi mitambo, mphamvu ndi ulemerero waukulu. 31 Ndipo adzatuma angelo ake, ndi kulira kwa lipenga kwakukulu, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinayi, ndi kuchokera kumathero a thambo kufika mbali ina.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.