Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 13

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

13 Mpaka liti Yehova? Kodi mudzandiyiwala mpaka kalekale?
    Mpaka liti mudzandibisira nkhope yanu?
Ndidzalimbana ndi maganizo anga
    ndi kukhala ndi chisoni mu mtima mwanga tsiku lililonse mpaka liti?
    Mpaka liti adani anga adzandipambana?

Ndiyangʼaneni ndi kundiyankha, Inu Yehova Mulungu wanga.
    Walitsani maso anga kuti ndingafe;
mdani wanga adzati, “Ndamugonjetsa,”
    ndipo adani anga adzakondwera pamene ine ndagwa.

Koma ndikudalira chikondi chanu chosasinthika;
    mtima wanga umakondwera ndi chipulumutso chanu.
Ine ndidzayimbira Yehova
    pakuti wandichitira zokoma.

2 Mbiri 20:5-12

Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano ndipo anati:

“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, ‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’

10 “Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11 Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12 Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”

Agalatiya 5:7-12

Inu munkathamanga mpikisano wanu wabwino. Anakuletsani ndani kuti musamverenso choonadi? Kukopeka kwanu kumeneku sikuchokera kwa Iye amene anakuyitanani. “Yisiti wapangʼono amagwira ntchito mu buledi yense.” 10 Ine ndikutsimikiza mwa Ambuye kuti inu simudzasiyana nane maganizo. Iye amene akukusokonezani adzalangidwa, kaya iyeyo ndiye ndani. 11 Abale, ngati ine ndikulalikirabe za mdulidwe, nʼchifukwa chiyani ndikusautsidwabe? Ngati ndikanakhala kuti sindikulalikira chipulumutso cha mtanda, palibe amene akanakhumudwa. 12 Kunena za amene akukuvutani, ndikanakonda akanangodzithena okha!

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.