Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
33 Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,
nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.
2 Mutamandeni Yehova ndi pangwe;
muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.
3 Muyimbireni nyimbo yatsopano;
imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.
4 Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;
Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.
5 Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;
dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.
6 Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,
zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.
7 Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;
amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.
8 Dziko lonse lapansi liope Yehova;
anthu onse amulemekeze Iye.
9 Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;
Iye analamulira ndipo zinakhazikika.
10 Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;
Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.
11 Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,
zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.
12 Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,
anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.
Pangano la Mulungu ndi Abramu
15 Zitatha izi, Yehova anayankhula ndi Abramu mʼmasomphenya nati:
“Usaope Abramu.
Ine ndili ngati chishango chokutchinjiriza.
Mphotho yako idzakhala yayikulu.”
2 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, mukhoza kundipatsa chiyani popeza ndikanali wopanda mwana ndipo amene adzatenge chuma changa ndi Eliezara wa ku Damasiko? 3 Inu simunandipatse ana kotero kuti wantchito wa ku nyumba kwanga ndiye amene adzalowe mʼmalo mwanga.”
4 Yehova anayankhula naye nati: “Munthu uyu sadzalowa mʼmalo mwako, koma mwana wako weniweni wamwamuna, wobereka wekha ndiye adzalowe mʼmalo mwako.” 5 Yehova anapita naye Abramu panja nati, “Tayangʼana kumwambaku, ndipo chifukwa cha chimenechi uwerenge nyenyezi ngati ungathe kuziwerenga.” Ndipo anamuwuza kuti, “Ndi mmene adzakhalire ana ako ndi zidzukulu zako.”
6 Abramu anakhulupirira Yehova, ndipo ichi chinamuchititsa kukhala wolungama.
7 Ndipo anamuwuza kuti, “Ine ndine Yehova amene ndinakuchotsa iwe ku mzinda wa Uri wa ku Akaldeya kuti ndikupatse dziko ili kuti likhale lako.”
8 Koma Abramu anati, “Haa! Ambuye Yehova, kodi ndingadziwe bwanji kuti lidzakhaladi langa?”
9 Kotero Yehova anati kwa iye, “Kanditengere kamsoti kangʼombe ka zaka zitatu, kamsoti ka mbuzi ka zaka zitatu, ndi nkhosa yayimuna ya zaka zitatu pamodzi ndi nkhunda ndi kamwana ka njiwa.”
10 Abramu anabweretsadi zonsezi nadula chilichonse pakati nʼkuzindandalika, chidutswa chilichonse kuyangʼanana ndi chinzake; koma njiwa ndi nkhunda sanazidule pakati. 11 Pamene miphamba inabwera kuti itole nyama ija, Abramu anayipirikitsa.
12 Pamene dzuwa limalowa Abramu anagona tulo tofa nato ndipo mdima wandiweyani ndi wochititsa mantha unamuphimba. 13 Tsono Yehova anati kwa iye, “Uyenera kudziwa mosakayika kuti zidzukulu zako zidzakhala alendo mʼdziko lachilendo ndipo zidzakhala akapolo ndi kuzunzidwa zaka 400. 14 Koma ndidzalanga dziko limene zidzukulu zako zidzagwireko ukapolo ndipo pambuyo pake iwo adzatulukamo ndi chuma chambiri. 15 Komabe iweyo udzamwalira mu mtendere ndi kuyikidwa mʼmanda utakalamba bwino. 16 Patapita mibado inayi, adzukulu ako adzabwereranso kuno popeza tchimo la Aamori silinafike pachimake kuti alangidwe.”
17 Dzuwa litalowa ndipo mdima utagwa, panaoneka mʼphika wofuka nthunzi ya moto ndi sakali yoyaka ndipo zinadutsa pakati pa zidutswa za nyama zija. 18 Pa tsiku limenelo, Yehova anachita pangano ndi Abramu nati, “Ndikulonjeza kuti ndidzapereka dziko ili kwa zidzukulu zako, kuchokera ku mtsinje wa ku Igupto mpaka ku mtsinje waukulu wa Yufurate. 19 Ndidzakupatsani dziko la Akeni, Akenizi, Akadimoni, 20 Ahiti, Aperezi, Arefaimu,
Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula
27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”
28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?”
Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”
29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.
32 Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. 33 Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”
34 Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.