Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 86:11-17

11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,
    ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;
patseni mtima wosagawikana
    kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;
    ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;
    mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.

14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;
    anthu ankhanza akufuna kundipha,
    amene salabadira za Inu.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
    wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;
    perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu
    ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu
    kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,
    pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.

Genesis 25:12-18

Ana Aamuna a Ismaeli

12 Nazi zidzukulu za Ismaeli, mwana wa Abrahamu amene wantchito wa Sara, Hagara Mwigupto uja, anaberekera Abrahamu.

13 Awa ndi mayina a ana a Ismaeli monga mwa mndandanda wa mabadwidwe awo: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli; kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, 14 Misima, Duma, Masa, 15 Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema; 16 Amenewa ndi ana a Ismaeli ndi mayina awo monga mwa midzi ndi misasa yawo. Anali olamulira mafuko khumi ndi awiri. 17 Ismaeli anakhala ndi moyo zaka 137. Iye anamwalira ndipo anakakhala ndi anthu a mtundu wake. 18 Zidzukulu za Ismaeli zinkakhala mʼdera la pakati pa Havila ndi Suri, kummwera kwa Igupto, mukamapita cha ku Asuri. Choncho anakhala kummawa kwa abale awo.

Chivumbulutso 2:8-11

Kalata Yolembera Mpingo wa ku Simurna

“Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti:

Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo. Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. 10 Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.

11 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.