Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
2 Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.
3 Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
Mulungu waulemerero abangula,
Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
4 Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
liwu la Yehova ndi laulemerero.
5 Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
6 Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
Siriyoni ngati mwana wa njati:
7 Liwu la Yehova limakantha
ngati kungʼanima kwa mphenzi.
8 Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
9 Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”
10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.
39 “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi
ndi kukhutitsa misona ya mikango
40 pamene ili khale mʼmapanga mwawo
kapena pamene ikubisala pa tchire?
41 Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani
pamene ana ake akulirira kwa Mulungu
ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya?
39 “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera?
Kodi umaonerera pamene nswala ikubala?
2 Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere?
Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa?
3 Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo;
pamenepo ululu wobereka nʼkutha.
4 Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo;
kenaka amachoka ndipo sabwereranso.
5 “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera?
Ndani amamasula zingwe zake?
6 Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake,
nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo
7 Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda;
ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu.
8 Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu
ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira.
9 “Kodi njati ingavomere kukutumikira?
Kodi ingagone mu gome lako usiku?
10 Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima?
Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako?
11 Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake?
Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa?
12 Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako
ndi kumuyika ku malo opunthira?
Mphatso za Mzimu Woyera
12 Tsopano abale anga okondedwa, sindikufuna mukhale osadziwa za mphatso za Mzimu. 2 Inu mukudziwa kuti pamene munali akunja, ankakusocheretsani mʼnjira zosiyanasiyana ndi kukukokerani ku mafano osayankhula. 3 Nʼchifukwa chake ndikuwuzani kuti palibe munthu amene ali ndi Mzimu wa Mulungu angayankhule kuti, “Yesu atembereredwe,” ndiponso palibe munthu anganene kuti “Yesu ndi Ambuye,” popanda kutsogozedwa ndi Mzimu Woyera.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.