Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
18 Koma Samueli amatumikira pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala. 19 Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka. 20 Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.”
26 Ndipo mnyamata Samueli anapitirira kukula mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Yehova ndi anthu.
148 Tamandani Yehova.
Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse,
mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
5 Zonse zitamande dzina la Yehova
pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
analamula ndipo sizidzatha.
7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
9 inu mapiri ndi zitunda zonse,
inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
inu nkhalamba ndi ana omwe.
13 Onsewo atamande dzina la Yehova
pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
matamando a anthu ake onse oyera mtima,
Aisraeli, anthu a pamtima pake.
Tamandani Yehova.
12 Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. 13 Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu. 14 Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
15 Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika. 16 Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika. 17 Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Yesu mʼNyumba ya Mulungu
41 Chaka chilichonse makolo ake ankapita ku Yerusalemu ku phwando la Paska. 42 Iye ali ndi zaka khumi ndi ziwiri, anapita ku phwando, monga mwa mwambo. 43 Phwando litatha, pamene makolo ake ankabwerera kwawo, mnyamata Yesu anatsalira ku Yerusalemu, koma iwo sanadziwe zimenezi. 44 Poganiza kuti anali nawo mʼgulu lawo, anayenda tsiku limodzi. Kenaka anayamba kumufunafuna pakati pa abale awo ndi anzawo. 45 Atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu kukamufuna. 46 Patatha masiku atatu anamupeza ali mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, atakhala pakati pa aphunzitsi, akumvetsera ndi kuwafunsa mafunso. 47 Aliyense amene anamumva Iye anadabwa ndi chidziwitso chake ndi mayankho ake. 48 Makolo ake atamuona, anadabwa. Amayi ake anati kwa Iye, “Mwanawe, watichitira zimenezi chifukwa chiyani? Abambo ako ndi ine takhala tili ndi nkhawa kukufunafuna Iwe.”
49 Iye anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumandifunafuna? Kodi simukudziwa kuti ndikuyenera kukhala mʼnyumba ya Atate anga?” 50 Koma iwo sanazindikire chomwe Iye amatanthauza.
51 Kenaka anapita nawo ku Nazareti ndipo anawamvera iwo. Koma amayi ake anasunga zinthu zonsezi mu mtima mwawo.
52 Ndipo Yesu anakula mu nzeru, msinkhu ndi chisomo cha Mulungu ndi anthu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.