Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 126

Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.

126 Yehova atabwezera akapolo ku Ziyoni,
    tinali ngati amene akulota.
Pakamwa pathu panadzaza ndi kuseka;
    malilime athu ndi nyimbo zachimwemwe.
Pamenepo kunanenedwa pakati pa anthu kuti,
    “Yehova wawachitira zinthu zazikulu.”
Yehova watichitira zinthu zazikulu,
    ndipo tadzazidwa ndi chimwemwe.

Tibwezereni madalitso athu, Inu Yehova,
    monga mitsinje ya ku Negevi.
Iwo amene amafesa akulira,
    adzakolola akuyimba nyimbo zachimwemwe.
Iye amene amayendayenda nalira,
    atanyamula mbewu yokafesa,
adzabwerera akuyimba nyimbo zachimwemwe,
    atanyamula mitolo yake.

Yesaya 19:18-25

18 Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.

19 Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. 20 Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. 21 Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. 22 Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.

23 Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. 24 Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. 25 Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”

2 Petro 1:2-15

Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.

Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu

Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.

Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.

10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Kukhala Oyera Mtima

12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. 13 Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, 14 chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. 15 Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.