Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
148 Tamandani Yehova.
Tamandani Yehova, inu a kumwamba,
mutamandeni Iye, inu a mlengalenga.
2 Mutamandeni, inu angelo ake onse,
mutamandeni, mutamandeni, inu zolengedwa za mmwamba.
3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi,
mutamandeni, inu nonse nyenyezi zowala.
4 Mutamandeni, inu thambo la kumwambamwamba
ndi inu madzi a pamwamba pa thambo.
5 Zonse zitamande dzina la Yehova
pakuti Iye analamula ndipo zinalengedwa.
6 Iye anaziyika pa malo ake ku nthawi za nthawi;
analamula ndipo sizidzatha.
7 Tamandani Yehova pa dziko lapansi,
inu zolengedwa zikuluzikulu za mʼnyanja, ndi nyanja zonse zakuya,
8 inu zingʼaningʼani ndi matalala, chipale ndi mitambo,
mphepo yamkuntho imene imakwaniritsa mawu ake,
9 inu mapiri ndi zitunda zonse,
inu mitengo ya zipatso ndi mikungudza yonse,
10 inu nyama zakuthengo ndi ngʼombe zonse,
inu zolengedwa zingʼonozingʼono ndi mbalame zowuluka.
11 Inu mafumu a dziko lapansi ndi anthu a mitundu yonse,
inu akalonga ndi olamulira a dziko lapansi.
12 Inu anyamata ndi anamwali,
inu nkhalamba ndi ana omwe.
13 Onsewo atamande dzina la Yehova
pakuti dzina lake lokha ndi lolemekezeka;
ulemerero wake ndi woopsa pa dziko lapansi pano ndi kumwamba komwe.
14 Iye wakwezera nyanga anthu ake,
matamando a anthu ake onse oyera mtima,
Aisraeli, anthu a pamtima pake.
Tamandani Yehova.
Ulemerero Wamʼtsogolo wa Ziyoni
54 “Sangalala, iwe mayi wosabala,
iwe amene sunabalepo mwana;
imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe,
iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
kuposa mkazi wokwatiwa,”
akutero Yehova.
2 Kulitsa malo omangapo tenti yako,
tambasula kwambiri nsalu zake,
usaleke;
talikitsa zingwe zako,
limbitsa zikhomo zako.
3 Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere;
ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina
ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.
4 “Usachite mantha; sadzakunyozanso.
Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso.
Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako
ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.
5 Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu;
dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6 Yehova wakuyitananso,
uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima,
mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,”
akutero Mulungu wako.
7 “Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya,
koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri.
8 Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa
ndili wokwiya kwambiri.
Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya,
ndidzakuchitira chifundo,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako.
9 “Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa.
Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi.
Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima,
sindidzakudzudzulaninso.
10 Ngakhale mapiri atagwedezeka
ndi zitunda kusunthidwa,
koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha.
Pangano langa lamtendere silidzasintha,”
akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.
11 “Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza,
Ine ndidzakongoletsa miyala yako.
Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro.
12 Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi.
Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto,
ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.
13 Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,
ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.
Kumwamba ndi Dziko Lapansi Zatsopano
21 Kenaka ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano pakuti kumwamba koyamba ndi dziko lapansi loyamba zinapita ndipo kunalibenso nyanja ina iliyonse. 2 Ndinaona mzinda wopatulika, Yerusalemu watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wovala zokongola kukonzekera mwamuna wake. 3 Ndipo ndinamva mawu ofuwula kuchokera ku Mpando Waufumu kuti, “Taonani! Malo wokhalapo Mulungu ali pakati pa anthu, ndipo Iye adzakhala ndi anthuwo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulungu mwini adzakhala nawo nakhala Mulungu wawo. 4 ‘Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo. Sikudzakhalanso imfa kapena kukhuza maliro kapena kulira kapena ululu popeza zakale zapita.’ ”
5 Amene anakhala pa mpando waufumuyo anati, “Ndikulenga zinthu zonse zikhale zatsopano!” Ndipo anati, “Lemba izi, pakuti mawu awa ndi okhulupirika ndi woona.”
6 Iye anandiwuza kuti, “Kwatha. Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza. Kwa onse akumva ludzu, ndidzawapatsa zakumwa zaulere zochokera ku kasupe wamadzi amoyo. 7 Iye amene adzapambane adzalandira zonsezi, ndipo ndidzakhala Mulungu wake ndi Iye adzakhala mwana wanga.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.