Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 147:12-20

12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu;
    tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni,
13 pakuti Iye amalimbitsa mipiringidzo ya zipata zako
    ndi kudalitsa anthu ako mwa iwe.
14 Iye amabweretsa mtendere mʼmalire mwako
    ndi kukukhutitsa ndi ufa wa tirigu wosalala.

15 Iyeyo amapereka lamulo pa dziko lapansi;
    mawu ake amayenda mwaliwiro.
16 Amagwetsa chisanu ngati ubweya
    ndi kumwaza chipale ngati phulusa.
17 Amagwetsa matalala ngati miyala.
    Kodi ndani angathe kupirira kuzizira kwake?
18 Amatumiza mawu ake ndipo chisanucho chimasungunuka;
    amawombetsa mphepo ndipo madzi amayenda.

19 Iye anawulula mawu ake kwa Yakobo,
    malamulo ake ndi zophunzitsa zake kwa Israeli.
20 Sanachitepo zimenezi kwa mtundu wina uliwonse wa anthu;
    anthu enawo sadziwa malamulo ake.

Tamandani Yehova.

1 Mbiri 28:1-10

Ndondomeko ya Kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu

28 Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima.

Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.” Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.”

“Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse. Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.” Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.”

“Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.”

“Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya. 10 Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.”

1 Akorinto 3:10-17

10 Mwachisomo chimene Mulungu wandipatsa, ine ndinayika maziko monga mmisiri waluntha, ndipo ena akumangapo. Koma aliyense ayenera kuchenjera mmene akumangira. 11 Pakuti wina sangayikenso maziko ena oposera amene anakhazikitsidwa kale, amene ndi Yesu Khristu. 12 Ngati munthu aliyense amanga pa maziko awa pogwiritsa ntchito golide, siliva, miyala yamtengowapatali, milimo yamitengo, tsekera kapena udzu, 13 ntchito yake idzaonekera pamene Tsiku la chiweruzo lidzazionetsa poyera. Tsikulo lidzafika ndi moto, ndipo motowo ndi umene udzayesa ntchito ya munthu aliyense. 14 Ngati zimene zamangidwazo sizidzagwa, adzalandira mphotho yake. 15 Ndipo ngati zidzanyeke ndi moto, sadzalandira mphotho koma iye mwini adzapulumukabe, koma monga ngati munthu amene wapulumuka mʼmoto.

16 Kodi inu simukudziwa kuti ndinu Nyumba ya Mulungu ndipo kuti Mzimu wa Mulungu amakhala mwa inu? 17 Ngati wina aliyense awononga Nyumba ya Mulunguyo, Mulungu nayenso adzamuwononga ameneyo; popeza Nyumba ya Mulungu ndi yopatulika ndipo Nyumbayo ndi inu amene.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.