Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 46

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora. Nyimbo ya anamwali.

46 Mulungu ndiye kothawira kwathu ndi mphamvu yathu,
    thandizo lopezekeratu pa nthawi ya mavuto.
Nʼchifukwa chake sitidzaopa ngakhale dziko lapansi lisunthike,
    ngakhale mapiri agwe pakati pa nyanja,
ngakhale madzi ake atakokoma ndi kuchita thovu,
    ngakhale mapiri agwedezeke ndi kukokoma kwake.

Kuli mtsinje umene njira zake za madzi zimasangalatsa mzinda wa Mulungu,
    malo oyera kumene Wammwambamwamba amakhalako.
Mulungu ali mʼkati mwake, iwo sudzagwa;
    Mulungu adzawuthandiza mmawa.
Mitundu ikupokosera, mafumu akugwa;
    Iye wakweza mawu ake, dziko lapansi likusungunuka.

Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Bwerani kuti mudzaone ntchito za Yehova,
    chiwonongeko chimene wachibweretsa pa dziko lapansi.
Iye amathetsa nkhondo ku malekezero a dziko lapansi;
    Iye amathyola uta ndi kupindapinda mkondo;
    amatentha zishango ndi moto.
10 Iye akuti, “Khala chete, ndipo dziwa kuti ndine Mulungu;
    ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu;
    ine ndidzakwezedwa mʼdziko lapansi.”

11 Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ife,
    Mulungu wa Yakobo ndi linga lathu.

Genesis 12:1-9

Mulungu Ayitana Abramu

12 Tsiku lina Yehova anamuwuza Abramu kuti, “Tuluka mʼdziko lako. Siya abale ako ndi banja la abambo ako ndipo pita ku dziko limene ndidzakusonyeza.

“Ndidzakusandutsa kholo la mtundu waukulu wa anthu
    ndipo ndidzakudalitsa;
ndi kukusandutsa wotchuka kotero kuti
    udzakhala dalitso kwa anthu ambiri.
Ndidzadalitsa amene adzadalitsa iwe,
    ndi kutemberera amene adzatemberera iwe;
ndipo mafuko onse a pa dziko lapansi
    adzadalitsika kudzera mwa iwe.”

Choncho Abramu ananyamuka monga momwe Yehova anamuwuzira, napita pamodzi ndi Loti. Pamene Abramu amachoka ku Harani nʼkuti ali ndi zaka 75. Abramu anatenga mkazi wake Sarai, Loti, mwana wamngʼono wake, pamodzi ndi chuma chawo chimene anapeza ndi antchito amene anali nawo ku Harani. Iwo ananyamuka ulendo mpaka kukafika ku dziko la Kanaani.

Abramu anadutsa mʼdzikomo mpaka kukafika ku Sekemu pa mtengo wa thundu wa ku More. Nthawi imeneyo Akanaani analipobe mʼdzikomo. Yehova anadza kwa Abramu nati, “Kwa zidzukulu zako ndidzapereka dziko limeneli.” Choncho Abramu anamangira Yehova amene anadza kwa iye, guwa lansembe.

Atachoka pamenepo analowera cha ku mapiri a kummawa kwa Beteli namangako tenti yake pakati pa Beteli chakumadzulo ndi Ai chakummawa. Kumeneko anamangira Yehova guwa lansembe napemphera mʼdzina la Yehovayo. Kenaka Abramu ananyamuka kumalowera cha ku Negevi.

1 Akorinto 7:17-24

Kukhala Moyo Wosinthika

17 Koma aliyense akhale moyo umene Ambuye anamupatsa, umene Mulungu anamuyitanira. Ili ndiye lamulo limene ndalikhazikitsa mʼmipingo yonse. 18 Ngati pamene munthu amayitanidwa anali atachita mdulidwe, asavutike nʼkubisa za mdulidwe wakewo. Ngatinso pamene munthu amayitanidwa nʼkuti asanachite mdulidwe, asachite mdulidwe. 19 Mdulidwe si kanthu, kusachita mdulidwe si kanthunso. Chofunika nʼkusunga malamulo a Mulungu. 20 Aliyense akhale monga analili pamene Mulungu anamuyitana.

21 Kodi munali kapolo pamene Mulungu anakuyitanani? Musavutike nazo zimenezi. Koma ngati mutapeza mwayi woti mulandire ufulu, ugwiritseni ntchito mwayiwo. 22 Pakuti amene anali kapolo pamene amayitanidwa ndi Ambuye, ndi mfulu wa Ambuye; chimodzimodzinso amene anali mfulu pamene anayitanidwa, ndi kapolo wa Khristu. 23 Munagulidwa ndi mtengowapatali, choncho musakhalenso akapolo a anthu. 24 Abale, aliyense angokhala pamaso pa Mulungu monga momwe analili pamene Mulungu anamuyitana.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.