Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Yona Apita ku Ninive
3 Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti, 2 “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.”
3 Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa. 4 Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.” 5 Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli.
10 Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho.
5 Peza mpumulo mwa Mulungu yekhayo iwe moyo wanga;
chiyembekezo changa chichokera mwa Iye.
6 Iye yekhayo ndiye thanthwe langa ndi chipulumutso changa;
Iyeyo ndi linga langa; sindidzagwedezeka.
7 Chipulumutso changa ndi ulemu wanga zimachokera kwa Mulungu:
Iye ndiye thanthwe langa lamphamvu; Mulungu ndiye pothawira panga.
8 Dalirani Iye nthawi zonse, inu anthu;
khuthulani mitima yanu kwa Iye,
pakuti Mulungu ndiye pothawirapo pathu.
Sela
9 Anthu wamba ndi mpweya chabe;
anthu apamwamba ndi bodza chabe;
ngati atayezedwa pa sikelo iwo ndi chabe;
iwowo pamodzi ndi mpweya ndi chabe
10 Musadalire kulanda mwachinyengo
kapena katundu wobedwa;
ngakhale chuma chanu chichuluke,
musayike mtima wanu pa icho.
11 Mulungu wayankhula kamodzi,
ine ndamvapo zinthu ziwiri;
choyamba nʼchakuti Inu Mulungu ndinu wamphamvu,
12 komanso Inu Ambuye, chikondi chanu nʼchosasinthika.
Chachiwiri nʼchakuti mumamuchitira munthu
molingana ndi ntchito zake.
29 Abale, chimene ndikutanthauza nʼchakuti nthawi yatha. Kuyambira tsopano anthu okwatira akhale ngati sanakwatire. 30 Amene akulira akhale monga ngati sakulira. Amene akukondwa akhale ngati sakukondwa. Amene akugula zinthu akhale ngati alibe zinthuzo. 31 Amene akugwiritsa ntchito zinthu za dziko lapansi lino, akhale ngati sizikuwakhudza. Pakuti dziko lapansi lino mmene lilirimu, likupita.
Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino
14 Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, 15 “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
16 Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. 17 Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 18 Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. 20 Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.